Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/15 tsamba 3-4
  • Mtendere—Kodi Udzabwera mwa Kuchotsapo Zida?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtendere—Kodi Udzabwera mwa Kuchotsapo Zida?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoyesayesa za Kuchotsapo Zida
  • Kuŵerengera Mtengo
  • Anthu Akufunafuna Zothetsera
    Galamukani!—1988
  • Kodi Anthu Angathetse Nkhondo Komanso Zachiwawa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2025
  • Loto la Mtendere wa Dziko Lonse—Masomphenya Olakwika
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Tidzafunikira Magulu Ankhondo Nthaŵi Zonse?
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/15 tsamba 3-4

Mtendere​—Kodi Udzabwera mwa Kuchotsapo Zida?

“KULI kuphophonya kwakukulu kwambiri kusokoneza kuchotsa zida ndi mtendere,”  anatero Winston Churchill zaka zisanu mitundu isanaloŵe mu nkhondo yadziko yachiŵiri. “Pamene mudzakhala ndi mtendere ndi pamene zida zidzachotsedwa,” iye anawonjezera tero.

Nchosemphana chotani nanga! Kodi ndani akaika pangozi kuchotsapo zida kufikira mtendere utatsimikiziridwa? Koma kodi ndimotani mmene pangakhalire mtendere weniweni pamene zida zawunjikidwa kaamba ka nkhondo? Uli mkhalidwe mu umene andale zadziko sanapeze njira yotulukiramo.

Winston Churchill anapanga ndemanga yake mu 1934, pambuyo pa Msonkhano wa Kuchotsapo Zida wochitidwa ndi Chigwirizano cha Amitundu kokha zaka ziŵiri kuchiyambi. Cholinga cha msonkhano umenewu, umene unatenga zaka 12 zokonzekera, chinali kupeŵa kuwunjika zida mu Europe. Anthu kuzungulira dziko lapansi amakumbukirabe kuphedwa kowopsya kwa asilikali mamiliyoni asanu ndi anayi mkati mwa Nkhondo Yadziko ya I, kuwonjezera ku mamiliyoni ambiri ovulazidwa ndi chiŵerengero chachikulu cha anthu wamba ovulala. Komabe, kuchotsapo zida sikunachitike konse. Kodi nchifukwa ninji?

Zoyesayesa za Kuchotsapo Zida

Lamulo la kuchotsapo zida lingalimbitsidwe koma kaŵirikaŵiri silimakhala logwira ntchito. Mwachitsanzo, pansi pa Pangano la mu 1919 la ku Versailles, Germany anachotseredwa zida ndipo “zitsimikizo zokwanira zinaperekedwa ndi kutengedwa zakuti zida za mtunduwo zidzachepetsedwa ku mlingo waung’ono wogwirizana ndi chisungiko cha mkatimo.” Izi zinali m’chigwirizano ndi chimodzi cha zolingalira za presidenti Woodrow Wilson wa ku U.S., zomwe pambuyo pake zinaphatikizidwa mu Article 8 (nambala ya lamulo) ya pangano la Chigwirizano cha Amitundu. Koma pamene Hitler anayamba kulamulira, posakhalitsa ananyalanyaza lamulolo.

Kodi Mitundu Yogwirizana inali yachipambano m’kukhazikitsa maziko okhazikika kaamba ka kuchotsapo zida pambuyo pa nkhondo yadziko yachiŵiri? Ayi, koma kusoŵeka kwake kwa chipambano sikunali kufunafuna kuyesayesa kogamulapo. Ngakhale kuli tero, pamene zida za nyukliya zowononga kwambiri zinakhalako, kuchotsapo zida kunali nkhani yofunika kwambiri. “Mkangano wapapitapo wakuti mpikisano wa zida zankhondo unali wosakaza zinthu mwachuma ndipo unatsogolera ku nkhondo yosapeŵeka,” ikutero The New Encyclopædia Britannica, “unaloŵedwa m’malo ndi mkangano wakuti kugwiritsira ntchito kwa mtsogolo kwa zida za nyukliya mu unyinjiwo kunawopsyeza kutsungula kwenikweniko.”

Bungwe la Kuchotsapo Zida la mitundu 12 linakhazikitsidwa mu 1952 kuti lithetse mpikisano wa zida womayambika wa Kummawa/​Kumadzulo. Linalephera kupambana, ndipo potsirizira pake mphamvu zazikulu ziŵirizo zinalimbitsa magulu awo olimbana. Zimvano ndi mapangano osiyanasiyana apangidwa kufikira nthaŵi ino. Komabe, mkhalidwe wa kusakhulupirirana sunalole kuthetsedwa kotheratu kwa zida zonse zankhondo. The New Encyclopædia Britannica ikunena kuti, chimenecho ndichinachake “chochilikizidwa ndi olingalira zongopeka.”

Kuŵerengera Mtengo

Kuchotsa zida kapena kusatero​—kodi ndi zowonongedwa zotani zimene zikuloŵetsedwamo? Nthaŵi zambiri zowonongedwa sizimaŵerengedwa mwa ndalama. Kulembedwa ntchito m’maindasitale ogwirizanitsidwa ndi zida kuyeneranso kulingaliridwa choyamba. M’maiko ambiri ndalama zamsonkho zimagwiritsidwa ntchito kugula zida zankhondo, zimene kupangidwa kwake kumachilikiza ntchito. Chotero kuchotsapo zida kungatsogolere ku kusoŵa ntchito. Chimenecho ndicho chifukwa chake maiko amene ali odera nkhaŵa kwambiri ndi ndalama zachitetezo amakwiya ndi lingaliro la kuchotsapo zida. Kwa iwo lingaliro loterolo liri loto lowopsya m’malo mwa loto Longopeka.

Komabe, sitinganyalanyaze unyinji wokulira wa ndalama zoloŵetsedwamo m’kugwiritsira ntchito makina ankhondo. Chayerekezedwa kuti 10 peresenti ya phindu la chiwonkhetso chonse cha phindu la zopangidwa za dziko imawonongedwa pa zida zankhondo. Kodi umenewo ndi unyinji wotani? Ziŵerengero zenizeni zimasiyana ndi kuchepa mphamvu kwa ndalama, koma lingalirani za kuwononga £1 miliyoni ($1.54 miliyoni, U.S.) mwanjira imeneyi mphindi iriyonse ya tsiku! Kodi ndi zoyambirira zotani zimene mukanasankha mukanakhala ndi unyinji umenewo? Thandizo kwa anjala? Chisamaliro chaumoyo? Ubwino wa ana? Kubwezeretsa kulinganizika kwa dziko ndi zamoyo? Palidi zambiri zomwe zingachitidwe!

Mwachitsanzo, lingalirani za programu ya “akasinja kukhala matilakitala” yolengezedwa posachedwapa mu U.S.S.R., kumene mafakitale ena a zida zankhondo akusinthidwa kuti atulutse mitundu 200 ya “zipangizo zopambana kwenikweni za malimidwe.” Kodi nchifukwa ninji zipangizo za malimidwe zimenezo zikufunika kwambiri chotero? Chifukwa chakuti, mogwirizana ndi Farming News ya ku Britain, “kokha mbali imodzi mwa zitatu ya zipatso ndi ndiwo zamasamba zolimidwa m’mafamu aboma ndizo zimene zimafikira anthu, zotsalazo zimasiyidwa kuwola m’mindayo kapena kuwonongeka pamalo otumizira ndi m’nkhokwe zosungira.”

Monga mmene kupanga matilakitala kungakhalire koyamikirika, kumapanga mbiri chifukwa nkwachilendo. Kuwonjezerapo, chiyambukiro chake pa kutulutsidwa kwa zida zankhondo nkwakung’ono kwambiri. Mapaundi, maruble, ndi madola mazanamazana a mamiliyoni osaŵerengeka akupitirizabe kuwonongedwa pa zida zankhondo m’dziko limene “anthu akukomoka ndi mantha, ali kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi,” monga mmene Yesu Kristu ananeneratu. Kodi mantha amenewo angathetsedwe motani? Kodi kuchotseratu zida kudzangokhala loto wamba? Ngati sitero, kodi nchiyani chimene chikufunikira kuti tibweretse iko?​—Luka 21:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena