Loto la Mtendere wa Dziko Lonse—Masomphenya Olakwika
CHIDALIRO cha ziyembekezo za mtendere wa dziko lonse chikukuladi. M’danga lake m’nyuzipepala ya The Toronto Star, Carol Goar analemba kuti: “Mapangano a mtendere akufalikira kuchokera ku Afghanistan kufika ku Angola. Mikangano ya m’zigawo imene inawoneka kukhala yosakhoza kuthetsedwa miyezi yochepa yapitayo ikusonyeza zizindikiro zakutha. Ndipo bungwe la Mitundu Yogwirizana likulimbanso mosangalatsa.” Goar akuti zimenezi zadzutsa “mliri wa chiwunda chonse wa chiyembekezo.” Nyuzipepala ya USA Today inalengeza mofananamo kuti: “Mtendere ukubuka kuzungulira dziko lonse.”
Chapadera kwenikweni chaposachedwapa ndichimene UN Chronicle inachilongosola kukhala “kumvana kumene kukuchitika pakati pa Soviet Union ndi United States.” Kuchotsa magulu a asilikali, zochitika zodabwitsa mu Eastern Europe, nkhani za kuchepetsa magulu a asilikari ndi zida—zochitika zimenezi zadzutsa ziyembekezo zakuti maiko amphamvu koposa pomalizira pake angaleke mpikisano wa zida. M’dziko limene kuwonongera ndalama pa zankhondo kukusimbidwa kukhala kukutha chuma choposa pa madola zikwi mamiliyoni 850 pa chaka, chimenechi ndicho chiyembekezo cholandirika koposa.
Mosasamala kanthu za zimenezo, kodi nzothekera motani kuti loto la munthu la mtendere wa dziko lonse lidzakwaniritsidwa? Ngakhale achidaliro koposa akuvomereza kuti pali mpata waukulukulu kuchokera pa kuchepetsa zida kufika pa kuchotsapo zida. Kuchotsapo zida za nyukliya kukafuna kukhulupirirana kosayerekezeka. Komabe, mwachisoni, maiko amphamvu koposa ali ndi mbiri yaitali ya kusakhulupirirana. Monga mmene zinaloseredwa m’Baibulo, iyi yakhala nyengo mu imene anthu atsimikizira kukhala “osayanjanitsika [“akuswa mapangano,” King James Version].”—2 Timoteo 3:3.
Pambali pa izi, si aliyense amene ali wokhutiritsidwa kuti kuchotsedwa kwa zida zanyukliya kudzabweretsa mtendere. Ngakhale ngati mitundu inakokosedwa kuwononga miyulu yawo ya zida za nyukliya, zida wamba zingaphebe mokulira. Nkhondo Zadziko za I ndi II zikupereka umboni wapoyera ku nsonga imeneyi. Ndiponso, luso la zopangapanga lofunikira kupanganso zida zanyukliya likanakhalapobe—lokonzekera ndi lodikirira chizindikiro choyamba cha mkangano wa ndale zadziko. Ena, monga wasayansi wa ndale zadziko Richard Ned Lebow, amatsutsadi kuti: “Mwinamwake kusunga zida za nyukliya zingapo apa ndi apo kumapangitsa anthu kukhala ochenjera.”
Koma malinga ngati zida za nyukliya ziripo, tsoka la chiwonongeko cha nyukliya lidzanyodola chipambano cha mtendere chirichonse chonenedwa; ndipo adzateronso mavuto osakhala azankhondo opitirizabe amene alanda mtendere wa mamiliyoni m’miyoyo yawo yatsiku ndi tsiku. Mlembi wamkulu wa UN Javier Pérez de Cuéllar analankhula za “tsoka la mamiliyoni a nzika zinzathu amene alibe nyumba kapena okhala m’nyumba za mkhalidwe wosayenera kotheratu. Vutolo likuipirabe mosalekeza.” UN Chronicle ikusimbanso kuti kutsalira m’zachuma kukukantha “mbali ziŵiri mwa zitatu za mtundu wa anthu, m’zochitika zina pali kusauka limodzi ndi umphaŵi wosasiyana ndi kuvutika kochititsidwa ndi nkhondo.” Ndipo bwanji ponena za mkhalidwe wa othaŵa m’dziko lawo okwanira chifupifupi 12 miliyoni? Kodi kuchepetsa zida kapena ngakhale kuzichotseratu kudzabweretsa mtendere ku miyoyo yawo?
Mowonekeratu, loto la munthu la mtendere wa dziko lonse liri masomphenya olakwika—achimbuuzi, ochepa, ogoma. Kodi pali chiyembekezo chabwinopo cha mtendere? Ndithudi chiripo. M’kope lapita la magazine ano, tinawona kuti Baibulo limapereka chiyembekezo chotsimikizirika cha mtendere.a Posachedwapa Yesu Kristu, monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzabweretsa mtendere wopambana kutalitali ziyembekezo zaumunthu zirizonse. Koma kodi mtendere umenewu udzatanthauzanjidi kwa mtundu wa anthu? Nkhani yotsatira idzalongosola zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani nkhani yakuti “Kodi Ndani Amene Adzatsogolera Mtundu wa Anthu ku Mtendere?” m’kope lathu la April 1, 1990.