N’chifukwa Chiyani Nkhondo Komanso Zachiwawa Zikuchitikabe Padzikoli?
Baibulo limafotokoza zinthu zimene zimachititsa kuti nkhondo komanso zachiwawa zizipitirira padzikoli.
UCHIMO
Mulungu analenga makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, m’chifaniziro chake. (Genesis 1:27) Zimenezi zikutanthauza kuti mwachibadwa, anthuwa ankafunika kusonyeza makhalidwe a Mulungu monga mtendere komanso chikondi. (1 Akorinto 14:33; 1 Yohane 4:8) Komabe, Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo anachimwa. Chifukwa cha zimenezi, tonsefe tinatengera uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Choncho, popeza kuti tinatengera uchimowu, tonsefe timakhala ndi maganizo ofuna kuchita zachiwawa.—Genesis 6:5; Maliko 7:21, 22.
MABOMA A ANTHU
Mulungu sanatilenge kuti tizidzilamulira. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) N’chifukwa chake n’zosatheka kuti maboma a anthu athetseretu nkhondo ndiponso zachiwawa.
SATANA NDI ZIWANDA ZAKE
Baibulo limanena kuti “dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” amene akutchulidwa pavesili ndi Satana Mdyerekezi ndipo iye ndi chigawenga chopha anthu. (Yohane 8:44) Ngakhale kuti Satana ndi ziwanda zake saoneka, iwo ndi amene amachititsa kuti anthu azimenya nkhondo komanso azichita zachiwawa.—Chivumbulutso 12:9, 12.
Anthu sangakwanitse kuthetsa zimene zimayambitsa nkhondo komanso zachiwawa koma Mulungu ndi amene angazithetse