Anthu sangathetse nkhondo
Kodi Nkhondo Komanso Zachiwawa Zidzathetsedwa Bwanji?
Baibulo limanena kuti Mulungu, osati anthu, ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.
MULUNGU ADZACHOTSERATU MABOMA A ANTHU
Mulungu adzathetsa maboma a anthu pogwiritsira ntchito nkhondo imene Baibulo limaitchula kuti Aramagedo.a (Chivumbulutso 16:16) Pa nthawi imeneyo, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” adzasonkhanitsidwa pamodzi “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Aramagedo ndi nkhondo ya Mulungu imene idzathetse nkhondo zonse.
Mulungu adzachotsa maboma onse a anthu ndipo adzakhazikitsa Ufumu, kapena kuti boma lake lakumwamba limene lidzalowe m’malo mwa mabomawa ndipo lidzalamulira dziko lapansi mpaka kalekale. (Danieli 2:44) Mulungu anasankha Mwana wake Yesu Khristu kukhala Mfumu ya Ufumuwu. (Yesaya 9:6, 7; Mateyu 28:18) Boma limeneli ndi Ufumub umene Yesu anauza otsatira ake kuti aziupempherera. (Mateyu 6:9, 10) Anthu onse padzikoli adzakhala ogwirizana komanso azidzalamuliridwa ndi boma limodzi ndipo Wolamulira wake adzakhala Yesu.
Mosiyana ndi anthu amene akulamulira masiku ano, Yesu sadzagwiritsira ntchito mphamvu zake pofuna kudzipezera phindu. Popeza kuti iye ndi wachikondi komanso wopanda tsankho, palibe munthu amene azidzadandaula kuti akusalidwa chifukwa cha mtundu wake, dziko lake kapenanso chikhalidwe chake. (Yesaya 11:3, 4) Anthu sazidzamenyeranso maufulu awo. Zili choncho chifukwa chakuti Yesu azidzasamalira munthu wina aliyense. Iye “adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo. . . . Adzawapulumutsa kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa.”—Salimo 72:12-14.
Ufumu wa Mulungu udzachotsa zida zankhondo zonse padzikoli. (Mika 4:3) Ufumuwu udzachotsanso anthu oipa amene safuna kusiya nkhondo kapenanso amene amasokoneza mtendere wa ena. (Salimo 37:9, 10) Anthu azidzapita kulikonse mosaopa padzikoli kaya ndi amuna, akazi ngakhalenso ana.—Ezekieli 34:28.
Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira padzikoli, anthu onse azidzakhala moyo wabwino kwambiri. Ufumuwu udzathetsa mavuto onse amene amayambitsa nkhondo, monga umphawi, njala komanso kusowa pokhala. Aliyense adzakhala ndi chakudya chabwino chochuluka komanso adzasangalala ndi malo okhala abwino kwambiri.—Salimo 72:16; Yesaya 65:21-23.
Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu zoipa zonse zimene zayamba chifukwa cha nkhondo. Zimenezi sizikutanthauza mabala okha, koma zikuphatikizaponso kuthetseratu ululu wamumtima umene anthu amakhala nawo chifukwa cha zinthu zoipa zimene zimachitika pa nthawi ya nkhondo. Nawonso anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padzikoli. (Yesaya 25:8; 26:19; 35:5, 6) Anthu adzalandiranso achibale awo amene anamwalira ndipo nkhanza zoipa zomwe zinachitika pa nthawi ya nkhondo zidzakhala mbali ya zinthu ‘zakale’ zomwe zidzaiwalike.—Chivumbulutso 21:4.
MULUNGU ADZACHOTSERATU UCHIMO
Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu kukhala ogwirizana polambira Mulungu woona Yehova,c “Mulungu amene ndi wachikondi komanso wamtendere.” (2 Akorinto 13:11) Anthu adzaphunzira kukhala limodzi mogwirizana. (Yesaya 2:3, 4; 11:9) Anthu onse amene azidzagwiritsira ntchito mfundo zomwe azidzaphunzira, adzakhala omasuka ku uchimo ndipo adzakhala angwiro.—Aroma 8:20, 21.
MULUNGU ADZACHOTSERATU SATANA NDI ZIWANDA ZAKE
Ufumu wa Mulungu udzawononga amene amayambitsa nkhondo, omwe ndi Satana ndi ziwanda zake. (Chivumbulutso 20:1-3, 10) Popeza kuti sadzakhalaponso, padziko lonse “padzakhala mtendere wochuluka.”—Salimo 72:7.
Musakayikire kuti zimene Mulungu analonjeza kuti adzathetsa nkhondo komanso zachiwawa zidzachitikadi. Iye ali ndi mphamvu komanso ndi wofunitsitsa kuthetsa nkhondo.
Mulungu ali ndi nzeru komanso mphamvu zomwe zikufunikira kuti nkhondo ndi zachiwawa zithetsedwe. (Yobu 9:4) Palibe chimene angalephere kukwaniritsa.—Yobu 42:2.
Mulungu sasangalala kuona anthu akuvutika. (Yesaya 63:9) Komanso iye “amadana ndi aliyense amene amakonda chiwawa.”—Salimo 11:5.
Nthawi zonse Mulungu amachita zimene wanena; iye sanganame.—Yesaya 55:10, 11; Tito 1:2.
Mulungu adzabweretsa mtendere weniweni komanso wamuyaya.
Mulungu adzathetsa nkhondo
a Werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” pa jw.org.
b Onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? pa jw.org.
c Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.