NKHANI YOPHUNZIRA 23
NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndi Yehova
Dzina la Yehova Ndi Lofunika Kwambiri kwa Ife
“‘Inu ndinu Mboni zanga,’ akutero Yehova.”—YES. 43:10.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zimene tingachite posonyeza kuti Yehova ndi woyera komanso zonse zimene Satana wakhala akumuneneza ndi zabodza.
1-2. Kodi tikudziwa bwanji kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa Yesu?
DZINA la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa Yesu. Palibe munthu wina amene anathandiza anthu kudziwa za Yehova kuposa Yesu. Munkhani yapita ija tinaona kuti Yesu anali wokonzeka kufa posonyeza kuti Yehova ndi woyera komanso njira zake zonse ndi zolungama. (Maliko 14:36; Aheb. 10:7-9) Ndipo pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu adzabwezera mphamvu zonse kwa Atate wake kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. (1 Akor. 15:26-28) Kodi zonse zimene Yesu wachita poyeretsa dzina la Mulungu zikutiphunzitsa chiyani? Zikusonyeza kuti iye amakonda kwambiri Yehova.
2 Yesu anabwera padziko lapansi m’dzina la Atate wake. (Yoh. 5:43; 12:13) Iye anathandiza otsatira ake kudziwa dzina la Atate wake. (Yoh. 17:6, 26) Iye akamaphunzitsa komanso kuchita zodabwitsa, ankathandiza anthu kudziwa kuti Yehova ndi amene akumupatsa nzeru komanso mphamvu. (Yoh. 10:25) Ndipotu Yesu anapempha Yehova kuti ayang’anire ophunzira ake “chifukwa cha dzina [la Yehovayo].” (Yoh. 17:11) Choncho ngati Yesu ankaona chonchi dzina la Atate wake, n’zosamveka kuti munthu anene kuti ndi wotsatira wa Khristu koma osadziwa kapena kugwiritsa ntchito dzinali.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Akhristufe timatsanzira Yesu ndipo timakonda ndi kulemekeza dzina la Yehova. (1 Pet. 2:21) Munkhaniyi, tiona chifukwa chake Yehova wapereka dzina lake kwa anthu amene amalalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mat. 24:14) Tikambirananso kufunika kwa dzina la Yehova kwa aliyense payekha.
“ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LAKE”
4. (a) Kodi Yesu asanapite kumwamba analamula ophunzira ake kuti achite chiyani? (b) Kodi lamulo limeneli likutichititsa kufunsa funso liti?
4 Atangotsala pang’ono kubwerera kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukadzalandira mzimu woyera mudzakhala ndi mphamvu. Ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Choncho uthenga wabwino unayenera kulalikidwa kulikonse osati ku Isiraeli kokha. Anthu a mitundu yonse anafunika kupatsidwa mwayi wokhala otsatira a Yesu. (Mat. 28:19, 20) Koma Yesu ananena kuti “mudzakhala mboni zanga.” Kodi ophunzira atsopanowa ankafunika kudziwa dzina la Yehova, kapena kungokhala mboni za Yesu? Nkhani ya pa Machitidwe chaputala 15 imatithandiza kupeza yankho la funsoli.
5. Kodi atumwi ndi akulu a ku Yerusalemu anasonyeza bwanji kuti anthu onse afunika kudziwa dzina la Yehova? (Onaninso chithunzi.)
5 Mu 49 C.E., atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anakumana kuti akambirane zimene anthu osadulidwa amitundu ina anayenera kuchita kuti akhale Akhristu. Kumapeto kwa zokambiranazo, Yakobo, yemwe anali mchimwene wake wa Yesu ananena kuti: “[Petulo] wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu odziwika ndi dzina lake.” Kodi pamenepa Yakobo ankanena za dzina la ndani? Mogwirizana ndi zimene mneneri Amosi analemba, Yakobo anati: “Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova.” (Mac. 15:14-18) Ophunzira atsopanowa anafunika kuphunzira za Yehova komanso ‘kudziwika ndi dzina lake.’ Izi zikutanthauza kuti iwo anafunika kuuza anthu ena za dzina la Mulungu ndipo anthuwo aziwadziwa monga oimira dzinalo.
Pamsonkhano wa bungwe lolamulira mu nthawi ya atumwi, amuna okhulupirikawa anazindikira kuti Akhristu ayenera kukhala anthu odziwika ndi dzina la Mulungu (Onani ndime 5)
6-7. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padzikoli? (b) Kodi chifukwa china chachikulu chimene iye anabwerera n’chiyani?
6 Dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova ndi Chipulumutso,” ndipo Yesu ndi njira imene Yehova akugwiritsa ntchito populumutsa anthu amene asonyeza chikhulupiriro. Yesu anabwera padzikoli kudzapereka moyo wake kuti apulumutse anthu. (Mat. 20:28) Dipo limene anapereka linatsegula mwayi kuti anthu apulumuke n’kudzapeza moyo wosatha.—Yoh. 3:16.
7 Koma n’chifukwa chiyani anthu anafunika kupulumutsidwa? Ankafunika kupulumutsidwa chifukwa cha zimene zinachitika m’munda wa Edeni. Munkhani yapita ija, tinaona kuti makolo athu oyambirira Adamu ndi Hava, sanamvere Yehova ndipo izi zinachititsa kuti ataye mwayi wokhala ndi moyo wosatha. (Gen. 3:6, 24) Koma pali nkhani inanso yomwe inayambitsidwa, yomwe ndi yaikulu kuposa kupulumutsidwa kwa anthu. Satana ananena mabodza oipa kwambiri okhudza Yehova. (Gen. 3:4, 5) Choncho kupulumutsidwa kwa mbadwa za Adamu ndi Hava kukugwirizana ndi nkhani yaikulu yomwe ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. Popeza Yesu ankaimira Yehova ndiponso ankadziwika ndi dzina lake iye anathandiza kwambiri poyeretsa dzinali.
N’zosamveka kuti munthu anene kuti ndi wotsatira wa Khristu koma osadziwa kapena kugwiritsa ntchito dzina la Atate wake
8. Kodi anthu onse amene amakhulupirira Yesu ayenera kuzindikira chiyani?
8 Otsatira onse a Yesu, kaya ndi Ayuda kapena anthu amitundu ina, anafunika kudziwa kuti amene akuwapulumutsa ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate wake wa Yesu. (Yoh. 17:3) Ndipo mofanana ndi Yesu, nawonso ankayenera kudziwika ndi dzina la Yehova. Ankafunikanso kuzindikira kuti kuyeretsedwa kwa dzinali ndi kofunika kwambiri. Kudziwa zimenezi ndi komwe kukanathandiza kuti adzapulumuke. (Mac. 2:21, 22) Otsatira onse okhulupirika a Yesu anafunika kuphunzira za Yehova komanso Yesu. M’pake kuti Yesu anamaliza pemphero lake la pa Yohane chaputala 17 ndi mawu akuti: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti iwonso azisonyeza chikondi ngati chimene inu munandisonyeza, kuti inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yoh. 17:26.
“INU NDINU MBONI ZANGA”
9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa ife?
9 N’zoonekeratu kuti otsatira onse a Yesu ayenera kuyesetsa kuyeretsa dzina la Yehova. (Mat. 6:9, 10) Ayenera kuona kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kuposa china chilichonse. Ndipo zimenezi zizionekera mu zochita zawo. Koma kodi tingathandize bwanji kuyeretsa dzina la Yehova kapena kutsutsa mabodza amene Satana anamuneneza?
10. Kodi pa Yesaya 42 mpaka 44 pamafotokoza za mlandu uti? (Yesaya 43:9; 44:7-9) (Onaninso chithunzi.)
10 Buku la Yesaya, chaputala 42 mpaka 44, likusonyeza udindo umene tili nawo poyeretsa dzina la Yehova. Machaputalawa amafotokoza mophiphiritsira za mlandu wokhudza milungu umene uli mukhoti. Yehova amauza aliyense amene amati ndi mulungu kuti apereke umboni wakuti ndi mulungudi. Iye amapemphanso mboni kuti zibwere kudzatsimikizira ngati imeneyo ili milungu yeniyeni. Koma palibe amene angapereke umboniwu.—Werengani Yesaya 43:9; 44:7-9.
Timayankha m’njira zambiri pa mlandu umene umatikhudza (Onani ndime 10-11)
11. Mogwirizana ndi Yesaya 43:10-12, kodi Yehova anauza chiyani anthu ake?
11 Werengani Yesaya 43:10-12. Ponena za anthu ake, Yehova akuti: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndipo ine ndine Mulungu.” Kenako Yehova akuwafunsa kuti: “Kodi palinso Mulungu wina kupatulapo ine?” (Yes. 44:8) Choncho ifeyo tili ndi mwayi woyankha funso limeneli. Zolankhula komanso zochita zathu ziyenera kutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu woona. Dzina lake ndi lapamwamba kuposa dzina lililonse. Zochita zathu zizisonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova ndipo tidzakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale Satana atatipanikiza kwambiri. Tikatero tidzathandiza kuyeretsa dzina lake.
12. Kodi ulosi wa pa Yesaya 40:3, 5 unakwaniritsidwa bwanji?
12 Tikamayeretsa dzina la Yehova kapena mbiri yake, timakhala tikutsanzira Yesu Khristu. Yesaya analosera kuti munthu wina ‘adzakonza njira ya Yehova.’ (Yes. 40:3) Kodi mawu amenewa anakwaniritsidwa bwanji? Yohane M’batizi anakonza njira ya Yesu amene anabwera m’dzina la Yehova ndiponso kulankhula m’dzina la Yehova. (Mat. 3:3; Maliko 1:2-4; Luka 3:3-6) Ulosi womwewo unanenanso kuti: “Ulemerero wa Yehova udzaonekera.” (Yes. 40:5) Kodi ulemererowo unaonekera bwanji? Yesu atabwera padzikoli ankachita zinthu ndendende ngati Yehova moti zinali ngati ndi Yehova mwiniwakeyo amene wabwera padziko lapansi.—Yoh. 12:45.
13. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?
13 Mofanana ndi Yesu, ife ndife Mboni za Yehova. Timadziwika ndi dzina la Yehova ndipo timauza ena za ntchito zake zodabwitsa. Koma kuti zimenezi zitheke, tiyeneranso kuthandiza anthu kudziwa udindo wa Yesu poyeretsa dzina la Mulungu. (Mac. 1:8) Yesu ndi Mboni yokhulupirika ya Yehova ndipo ife timatengera chitsanzo chake. (Chiv. 1:5) Koma kodi tingasonyezenso bwanji kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa ife?
MMENE TINGASONYEZERE KUTI DZINA LA YEHOVA NDI LOFUNIKA KWAMBIRI
14. Mogwirizana ndi Salimo 105:3, kodi timamva bwanji tikaganizira za dzina la Yehova?
14 Timanyadira kudziwika ndi dzina la Yehova. (Werengani Salimo 105:3.) Yehova amasangalala kwambiri tikamanyadira dzina lake. (Yer. 9:23, 24; 1 Akor. 1:31; 2 Akor. 10:17) ‘Kudzitama mwa Yehova’ kumatanthauza kunyadira kuti Yehova ndi Mulungu wathu. Timaona kuti umenewu ndi mwayi wolemekeza dzina lake komanso kuyeretsa mbiri yake. Sitiyenera kuchita manyazi kuuza anzathu kuntchito, kusukulu, maneba athu kapena anthu ena kuti ndife a Mboni za Yehova. Mdyerekezi amafuna kuti tisiye kuuza anthu ena zokhudza dzina la Yehova. (Yer. 11:21; Chiv. 12:17) Ndipo Satana ndi aneneri ake abodza amafuna kuti anthu aiwale dzina la Yehova. (Yer. 23:26, 27) Koma kukonda dzina la Yehova kumachititsa kuti tizisangalala “tsiku lonse.”—Sal. 5:11; 89:16.
15. Kodi kuitana pa dzina la Yehova kumatanthauza chiyani?
15 Timapitiriza kuitana pa dzina la Yehova. (Yow. 2:32; Aroma 10:13, 14) Kuitana pa dzina la Yehova sikumangotanthauza kudziwa dzinalo n’kumaligwiritsa ntchito. Kumatanthauza kudziwa zoti Mulungu aliko, kumukhulupirira komanso kumudalira kuti azitithandiza ndiponso kutitsogolera. (Sal. 20:7; 99:6; 116:4; 145:18) Timathandiza anthu ena kudziwa dzina la Mulungu komanso makhalidwe ake abwino. Timawalimbikitsanso kuti alape n’kuchita zinthu zimene zingathandize kuti Yehova azisangalala nawo.—Yes. 12:4; Mac. 2:21, 38.
16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti Satana ndi wabodza?
16 Timalolera kuvutika chifukwa cha dzina la Yehova. (Yak. 5:10, 11) Tikakhalabe okhulupirika pamene tikukumana ndi mavuto timasonyeza kuti Satana ndi wabodza. M’nthawi ya Yobu, Satana ananeneza anthu onse amene amatumikira Yehova kuti: “Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Satana ananena kuti anthu angatumikire Yehova pokhapokha ngati zinthu zikuwayendera bwino koma ngati atakumana ndi mavuto, angasiye kumutumikira. Yobu anakhala wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti zimenezi ndi zabodza. Ifenso tili ndi mwayi wosonyeza kuti kaya Satana atichitire zotani, sitingasiye kutumikira Yehova. Tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova azitiyang’anira chifukwa cha dzina lake.—Yoh. 17:11.
17. Mogwirizana ndi 1 Petulo 2:12, kodi tingalemekeze bwanji dzina la Yehova?
17 Timalemekeza dzina la Yehova. (Miy. 30:9; Yer. 7:8-11) Popeza timaimira Yehova komanso kudziwika ndi dzina lake, tikhoza kutamanda dzinalo kapena kulinyozetsa. (Werengani 1 Petulo 2:12.) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti zolankhula komanso zochita zathu zizitamanda Yehova. Tikamachita zimenezi, ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kulemekeza dzina la Yehova.
18. Kodi tingasonyezenso bwanji kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa ife? (Onaninso mawu a m’munsi.)
18 Timaona kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kuposa mmene anthu amationera. (Sal. 138:2) N’chifukwa chiyani kukhala ndi maganizo amenewa n’kofunika kwambiri? Anthu ena akhoza kumatinyoza chifukwa chakuti timakonda dzina la Yehova.a Yesu analolera kufa imfa yochititsa manyazi ngati chigawenga chifukwa chofuna kulemekeza dzina la Yehova. Iye “sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira,” kutanthauza kuti sankadera nkhawa kwambiri za mmene anthu ena azimuonera. (Aheb. 12:2-4) Iye ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu.—Mat. 26:39.
19. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za dzina la Yehova? Perekani chifukwa.
19 Timanyadira dzina la Yehova ndipo timaona kuti ndi mwayi waukulu kudziwika kuti ndife Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi timakhala ofunitsitsa kupitiriza kutamanda dzina la Yehova ngakhale anthu ena azitinyoza. Dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa ifeyo kuposa mmene anthu ena amationera. Choncho kaya Satana atichitire zotani, tiyeni tipitirize kutamanda dzina la Yehova. Tikatero tidzasonyeza kuti dzina la Yehova ndi lofunika kwambiri kwa ife ngati mmene Yesu Khristu amalionera.
NYIMBO NA. 10 Tamandani Yehova Mulungu Wathu
a Ngakhale Yobu, yemwe anali wokhulupirika, anasokonezeka ataganizira mmene anzake atatu ankamuonera. Poyamba, ana ake onse atamwalira komanso katundu wake yense atawonongeka, “Yobu sanachimwe kapena kuimba Mulungu mlandu woti wachita zinthu zoipa.” (Yobu 1:22; 2:10) Koma pambuyo pake, anzakewo atamunena kuti Yobu wachita zinazake zoipa, anayamba ‘kulankhula mosaganiza bwino.’ Iye ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kuteteza mbiri yake kuposa kuyeretsa dzina la Mulungu.—Yobu 6:3; 13:4, 5; 32:2; 34:5.