NKHANI YOPHUNZIRA 37
NYIMBO NA. 114 “Khalani Oleza Mtima”
Kodi Tingatani Ngati Pachitika Zopanda Chilungamo?
“Iye ankayembekezera chilungamo, koma pankachitika zinthu zopanda chilungamo.”—YES. 5:7.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana mmene chitsanzo cha Yesu chingatithandizire kuti tizisangalatsabe Yehova tikakumana ndi zinthu zopanda chilungamo.
1-2. Kodi anthu ambiri amatani akakumana ndi zinthu zopanda chilungamo, nanga tingadzifunse mafunso ati?
TIKUKHALA m’dziko lopanda chilungamo. Anthu ambiri amachitiridwa zinthu zopanda chilungamo pa zifukwa zosiyanasiyana monga kusauka, mtundu wawo komanso chifukwa choti ndi amuna kapena akazi. Ambiri amavutikanso chifukwa chakuti anthu olemera omwe amachita bizinesi komanso akuluakulu aboma adyera amangoganizira zopeza ndalama. Zinthu ngati izi zingachititse ifeyo kapena anthu ena amene tikuwadziwa kuti azivutika.
2 N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amakwiya chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika m’dzikoli. Tonsefe timafuna kumachitiridwa zinthu mwachilungamo komanso kumadzimva kuti ndife otetezeka. Anthu ena amachita zinthu zofuna kusintha zinthu m’dziko lawo. Amasaina zikalata, kuchita zionetsero komanso kuthandiza atsogoleri andale omwe amalonjeza kuti adzathetsa zopanda chilungamo. Koma Akhristufe timaphunzitsidwa kuti ‘tisamakhale mbali ya dziko,’ ndipo timayembekezera kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa zopanda chilungamo zonse. (Yoh. 17:16) Komabe, timakhumudwa kapena kukwiya tikaona munthu wina akuchitiridwa zopanda chilungamo. Mwina tingamadzifunse kuti: ‘Kodi ndizitani zoterezi zikachitika? Kodi pali zimene ndingachite panopa pa nkhaniyi?’ Kuti tiyankhe mafunsowa, tiyeni tikambirane mmene Yehova ndi Yesu amaonera zinthu zopanda chilungamo.
YEHOVA NDI YESU AMADANA NDI ZOPANDA CHILUNGAMO
3. N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti timakwiya ndi zinthu zopanda chilungamo? (Yesaya 5:7)
3 Baibulo limafotokoza chifukwa chake timakwiya tikaona zinthu zopanda chilungamo. Limanena kuti Yehova anatilenga m’chifaniziro chake komanso kuti iye “amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.” (Sal. 33:5; Gen. 1:26) Sachita zinthu zopanda chilungamo ndipo safuna anthu azichita zimenezo. (Deut. 32:3, 4; Mika 6:8; Zek. 7:9) Mwachitsanzo, mu nthawi ya Yesaya, Yehova anamva Aisiraeli ‘akulira chifukwa chozunzidwa’ ndi Aisiraeli anzawo. (Werengani Yesaya 5:7.) Iye anachitapo kanthu polanga anthu omwe mobwerezabwereza ankanyalanyaza Chilamulo n’kumachitira ena zopanda chilungamo.—Yes. 5:5, 13.
4. Kodi Yesu amamva bwanji ndi zopanda chilungamo? (Onaninso chithunzi.)
4 Mofanana ndi Yehova, Yesu amadana ndi zopanda chilungamo. Tsiku lina Yesu ataona munthu wolumala dzanja anamva chisoni ndipo ankafuna kumuchiritsa. Koma atsogoleri achipembedzo ouma mtima anakwiya ndi zimenezi. Iwo ankaona kuti Yesu akuphwanya Sabata ndipo analibe nazo ntchito kuti munthuyo apeza bwino. Kodi Yesu anamva bwanji chifukwa cha zimene atsogoleri a chipembedzowo anachita? Iye “anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.”—Maliko 3:1-6.
Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda ankachitira nkhanza anthu, koma Yesu ankawachitira chifundo (Onani ndime 4))
5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhalabe okwiya pakachitika zopanda chilungamo?
5 Yehova ndi Yesu amakwiya ndi zopanda chilungamo, choncho sikulakwa ngati nafenso timakwiya. (Aef. 4:26) Komabe tizikumbukira kuti ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka, mkwiyowo sungakonze zopanda chilungamozo. Ndipotu kukwiya kwa nthawi yaitali kungachititse kuti tisokonezeke maganizo kapena tidwale. (Sal. 37:1, 8; Yak. 1:20) Ndiye kodi tizitani pakachitika zopanda chilungamo? Tiyeni tione zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Yesu.
ZIMENE YESU ANACHITA ATAKUMANA NDI ZOPANDA CHILUNGAMO
6. Kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zinkachitika Yesu ali padziko lapansi? (Onaninso chithunzi.)
6 Yesu ali padzikoli ankaona zinthu zambiri zopanda chilungamo. Ankaona anthu wamba akuponderezedwa ndi atsogoleri achipembedzo. (Mat. 23:2-4) Ankaonanso nkhanza zimene olamulira a Chiroma ankachitira anthu. Ayuda ambiri ankafuna kumasulidwa ku ulamuliro wa Aroma ndipo ena anapanga magulu omwe ankamenyana ndi Aromawo. Koma Yesu sankayambitsa kapena kulimbikitsa magulu ofuna kusintha zinthu. Atadziwa kuti anthu akufuna kumuveka ufumu, anathawa.—Yoh. 6:15.
Yesu akuchoka pa gulu la anthu amene akufuna kuti akhale wolamulira wawo (Onani ndime 6)
7-8. N’chifukwa chiyani Yesu sanayese kuthetsa zinthu zopanda chilungamo ali padzikoli? (Yohane 18:36)
7 Yesu ali padzikoli sanagwirizane ndi andale pofuna kuthetsa zopanda chilungamo. Iye ankadziwa kuti anthu alibe mphamvu kapena udindo wodzilamulira okha. (Sal. 146:3; Yer. 10:23) Anthu sangathenso kuthetsa vuto lenileni limene limayambitsa zopanda chilungamo. Dzikoli likulamulidwa ndi Satana, yemwe ndi wakupha komanso amene amayambitsa zopanda chilungamo. (Yoh. 8:44; Aef. 2:2) Popeza anthufe si angwiro, ngakhale anthu amaganizo abwino sangachite zinthu zachilungamo nthawi zonse.—Mlal. 7:20.
8 Yesu ankadziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene ungathetse zopanda chilungamo. Choncho ankagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake ‘polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ (Luka 8:1) Iye anatsimikizira ‘anthu amene ankamva njala ndi ludzu la chilungamo’ kuti zachinyengo zidzatha. (Mat. 5:6; Luka 18:7, 8) Koma izi zidzatheka ndi boma la Mulungu lomwe ‘silili mbali yadzikoli,’ osati chifukwa cha zimene anthu akuchita pofuna kusintha zinthu.—Werengani Yohane 18:36.
TIZITSANZIRA YESU TIKAKUMANA NDI ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO
9. N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi womwe udzathetse zopanda chilungamo?
9 Padzikoli pakuchitika zinthu zopanda chilungamo zambiri kuposa m’nthawi ya Yesu. Amene akuyambitsa zonsezi ‘m’masiku otsirizawa’ ndi Satana komanso anthu amene amawalamulira. (2 Tim. 3:1-5, 13; Chiv. 12:12) Mofanana ndi Yesu, timadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse chimene chimayambitsa zopanda chilungamo. Popeza tili kumbali ya Ufumuwu, sitichita nawo zionetsero kapena zinthu zina zimene anthu amachita polimbana ndi zopanda chilungamo. Chitsanzo ndi mlongo wina dzina lake Stacy.a Asanaphunzire choonadi, iye ankachita nawo zionetsero pofuna kusintha zinthu. Koma kenako anayamba kukayikira ngati zimene ankachitazo zinalidi zothandiza. Iye anati: “Ndikakhala kuzionetsero ndinkadzifunsa ngati ndikuchitadi zoyenera. Popeza panopa ndili kumbali ya Ufumu wa Mulungu, ndimadziwa kuti ndinasankha bwino ndipo Yehova adzathandiza anthu onse amene amachitiridwa zopanda chilungamo kuposa mmene ineyo ndingachitire.”—Sal. 72:1, 4.
10. N’chifukwa chiyani zimene anthu amachita pofuna kusintha zinthu sizigwirizana ndi malangizo a Yesu a pa Mateyu 5:43-48? (Onaninso chithunzi.)
10 Zimene anthu amachita pofuna kusintha zinthu, amazichita chifukwa chokwiya kapena kusafuna kutsatira malamulo. Koma izi n’zosiyana ndi zimene Yesu ankachita komanso kuphunzitsa. (Aef. 4:31) M’bale wina dzina lake Jeffrey ananena kuti: “Ndikudziwa kuti zionetsero zooneka zamtendere zikhoza kusintha m’kanthawi kochepa anthu n’kuyamba kuchita ziwawa komanso kuba zinthu.” Komatu Yesu anaphunzitsa kuti tizikonda anthu onse, ngakhale amene akutitsutsa kapena kutizunza. (Werengani Mateyu 5:43-48.) Akhristufe timapewa chilichonse chosemphana ndi zimene Yesu anatiphunzitsa.
Pamafunika khama kuti tisalowerere ndale komanso kuti tisalowe m’magulu ofuna kusintha zinthu (Onani ndime 10)
11. N’chiyani chingatithandize kuti tisalowe m’magulu ofuna kusintha zinthu?
11 Ngakhale kuti tikudziwa kuti Ufumu wa Mulungu udzathetseratu zinthu zopanda chilungamo, zikhoza kutivuta kutsanzira Yesu ngati tachitiridwa zinthuzi. Umu ndi mmene anamvera Janiya, yemwe ankasalidwa chifukwa cha mtundu wake. Janiya anati: “Ndinapsa mtima moti ndinkafuna kubwezera. Ndiye ndinalowa gulu limene linkalimbana ndi kusankhana mitundu. Ndinkaganiza kuti izi zithandiza kuti mtima wanga ukhaleko m’malo.” Koma patapita nthawi Janiya anazindikira kuti ankafunika kusintha. Iye anati: “Ndinkalola kuti anthu ena azisokoneza maganizo anga komanso kuti ndizidalira kwambiri anthu m’malo modalira Yehova. Choncho ndinaganiza zotuluka m’gululo.” Tiyenera kusamala kuti tisamalowerere ndale kapena magulu ofuna kusintha zinthu ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka.—Yoh. 15:19.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala ndi zimene timawerenga, kumvetsera komanso kuonera?
12 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisakwiye kwambiri tikaona zopanda chilungamo? Ambiri amaona kuti chimene chimawathandiza ndi kusankha bwino zimene amawerenga, kumvetsera komanso kuonera. Nthawi zambiri pa intaneti pamaikidwa zinthu zimene zimalimbikitsa anthu kukwiya ndi zopanda chilungamo kapenanso kuukira boma. Ndiponso olemba nkhani amazilemba moikira kumbuyo winawake. Ngakhale zitakhala zoona kuti pachitikadi zopanda chilungamo, kodi kumangoziganizira kungatithandizedi? Kuganizira zinthu ngati izi kwa nthawi yaitali kungachititse kuti tikhumudwe kwambiri. (Miy. 24:10) Ndipo choopsa n’chakuti tingayambe kuiwala kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse zopanda chilungamo zonse.
13. Kodi kuwerenga Baibulo kungatithandize bwanji kuti tiziona moyenera zinthu zopanda chilungamo?
13 Kuwerenga Baibulo nthawi zonse komanso kuganizira zimene tawerenga kungatithandize tikaona zopanda chilungamo. Mlongo wina dzina lake Alia anakhumudwa ataona kuti anthu a m’dera lake ankaponderezedwa. Zinkaoneka kuti amene ankapondereza anzawowo sankalangidwa. Alia anati: “Tsiku lina ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova adzathetsadi mavuto onsewa?’ Pa nthawiyi ndinawerenga Yobu 34:22-29. Mavesiwa anandikumbutsa kuti palibe angabisale kuti Yehova asamuone. Iye ndi wachilungamo kwambiri ndipo angathe kukonza zinthu.” Pamene tikuyembekezera kuti Ufumu wa Mulungu udzabweretse chilungamo chenicheni, tizichita zinthu mwanzeru tikaona zopanda chilungamo. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
ZIMENE TINGACHITE TIKAONA ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO
14. Kodi tingatani kuti tisamachite nawo zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika m’dzikoli? (Akolose 3:10, 11)
14 Sitingaletse ena kuchita zopanda chilungamo koma ifeyo tikhoza kukhala odziletsa. Monga tanena kale, tiyenera kutsanzira Yesu posonyeza chikondi. Chikondi chingatilimbikitse kuchita zinthu mwaulemu, ngakhale kwa anthu amene amachita zopanda chilungamo. (Mat. 7:12; Aroma 12:17) Yehova amasangalala tikamachita zinthu mokoma mtima komanso mwachilungamo kwa aliyense.—Werengani Akolose 3:10, 11.
15. Kodi kuphunzitsa ena Baibulo n’kothandiza bwanji?
15 Njira yabwino yothandizira anthu pa nkhani ya zinthu zopanda chilungamo ndi kuwaphunzitsa Baibulo. Tikutero chifukwa ‘kudziwa Yehova’ kungathandize munthu yemwe anali waukali ndi wachiwawa kuti akhale wokoma mtima komanso wokonda mtendere. (Yes. 11:6, 7, 9) Asanaphunzire choonadi, bambo wina dzina lake Jemal analowa gulu lolimbana ndi boma lomwe iye ankaliona kuti ndi lopondereza. Jemal anati: “Simungakakamize anthu kuti asinthe. Ine sindinakakamizidwe kuti ndisinthe, ndinasintha chifukwa cha mfundo za m’Baibulo zimene ndinkaphunzira.” Zimene Jemal anaphunzira zinamuthandiza kuti asiye kumenya nkhondo. Choncho ngati anthu ambiri ataphunzira Baibulo n’kusintha, ndi anthu ochepa okha omwe angamachite zinthu zopanda chilungamo.
16. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kuuza ena zimene Ufumu wa Mulungu udzachite?
16 Mofanana ndi Yesu, tikufunitsitsa kuuza anthu kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse zopanda chilungamo. Chiyembekezo chimenechi chikhoza kulimbikitsa anthu amene achitiridwa zopanda chilungamo. (Yer. 29:11) Stacy yemwe tamutchula kale uja anati: “Kuphunzira choonadi kwandithandiza kupirira zinthu zopanda chilungamo. Yehova amalimbikitsa anthu pogwiritsa ntchito uthenga wa m’Baibulo.” Choncho muzikhala okonzeka kulimbikitsa ena pogwiritsa ntchito malonjezo a m’Baibulo. Muzikhulupirira kwambiri mfundo za m’Malemba zomwe takambirana munkhaniyi. Mukatero mudzakhala wokonzeka kukambirana ndi anzanu kuntchito kapena kusukulu zimene Malemba amanena pa nkhani yokhudza zinthu zopanda chilungamo.b
17. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kupirira zinthu zopanda chilungamo?
17 Timadziwa kuti tizikumanabe ndi zinthu zopanda chilungamo m’dzikoli. Pamene tikuyembekezera kuti Satana ‘aponyedwe kunja,’ Yehova amatithandiza komanso kutipatsa chiyembekezo. (Yoh. 12:31) Kudzera m’Malemba, iye amatifotokozera chifukwa chake padzikoli pamachitika zopanda chilungamo komanso mmene amamvera tikamavutika chifukwa cha zinthuzo. (Sal. 34:17-19) Kudzera mwa Mwana wake, Yehova amatiphunzitsa zimene tingachite tikakumana ndi zopanda chilungamo komanso mmene Ufumu wake udzazithetsere. (2 Pet. 3:13) Tiyeni tipitirize kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumuwu pamene tikuyembekezera nthawi imene dziko lonse lidzadzaze ndi anthu “achilungamo ndiponso a mtima wowongoka.”—Yes. 9:7.
NYIMBO NA. 158 “Sadzachedwa”
a Mayina ena asinthidwa.
b Onaninso Zakumapeto A mfundo 24-27 m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa.