Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 September tsamba 14-19
  • Muzilemekeza Anthu Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilemekeza Anthu Ena
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI KULEMEKEZA ENA N’KUTANI?
  • MUZILEMEKEZA ANTHU A M’BANJA LANU
  • MUZILEMEKEZA AKHRISTU ANZANU
  • TIZILEMEKEZA ANTHU OMWE SI AKHRISTU ANZATHU
  • Kodi Ulemu Unapita Kuti?
    Galamukani!—2024
  • Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Ndingawapangitse Motani Ena Kundipatsa Ulemu?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 September tsamba 14-19

NKHANI YOPHUNZIRA 38

NYIMBO NA. 120 Tikhale Ofatsa Ngati Khristu

Muzilemekeza Anthu Ena

“Kulemekezedwa nʼkwabwino kuposa siliva ndi golide.”—MIY. 22:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kulemekeza anthu ena komanso mmene tingachitire zimenezo ngakhale pamene zinthu zavuta.

1. N’chifukwa chiyani anthu amayamikira akamalemekezedwa? (Miyambo 22:1)

KODI inuyo mumamva bwanji anthu ena akamakulemekezani? N’zosachita kufunsa kuti mumayamikira. Munthu aliyense amafuna kulemekezedwa. Tonsefe timasangalala tikamalemekezedwa. M’pake kuti Baibulo limanena kuti “kulemekezedwa nʼkwabwino kuposa siliva ndi golide.”—Werengani Miyambo 22:1.

2-3. N’chifukwa chiyani nthawi zina zimakhala zovuta kulemekeza ena, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Kulemekeza anthu ena kumakhala kovuta nthawi zina. Chifukwa chimodzi n’chakuti timaona zimene anthu omwe timakhala nawo pafupi amalakwitsa. Komanso anthu ambiri masiku ano ndi opanda ulemu. Ndiye n’chifukwa chiyani tiyenera kumalemekeza anthu ena? Chifukwa chakuti Yehova amafuna kuti tizilemekeza “anthu amitundu yonse.”—1 Pet. 2:17.

3 Munkhaniyi tikambirana zimene kulemekeza anthu ena kumatanthauza komanso mmene tingaperekere ulemu kwa (1) anthu a m’banja lathu, (2) Akhristu anzathu ndiponso (3) anthu amene si a Mboni. Tionanso mmene tingaperekere ulemu kwa ena ngakhale pa nthawi imene zingakhale zovuta kuchita zimenezi.

KODI KULEMEKEZA ENA N’KUTANI?

4. Kodi kulemekeza ena kumatanthauza chiyani?

4 Kodi kulemekeza ena kumatanthauza chiyani? Mawu akuti “kulemekeza” ena amanena za mmene timaonera komanso mmene timachitira zinthu ndi ena. Tikaona kuti munthu ali ndi makhalidwe enaake abwino, wachita zinazake zabwino kapenanso ali ndi udindo, timamulemekeza. Tikamalemekeza ena timachita nawo zinthu m’njira yakuti azidzimva kuti ndi amtengo wapatali komanso amayamikiridwa. Koma ulemu weniweni uyenera kuchokera mumtima.—Mat. 15:8.

5. N’chiyani chingatithandize kuti tizilemekeza ena?

5 Yehova amafuna kuti tizilemekeza anthu ena ndipo Mawu ake amatilimbikitsa kuti tizilemekeza “olamulira akuluakulu.” (Aroma 13:​1, 7) Koma munthu wina anganene kuti, “Ine ndimapereka ulemu kwa anthu oyenera kuwalemekeza.” Kodi maganizo amenewa ndi abwino? Atumiki a Yehovafe sitimalemekeza anthu chifukwa cha zochita zawo zokha. Timalemekeza anthu chifukwa chakuti timakonda Yehova ndipo timafuna kumusangalatsa.—Yos. 4:14; 1 Pet. 3:15.

6. Kodi n’zotheka kulemekeza munthu amene sakulemekezani? Fotokozani. (Onaninso chithunzi.)

6 Ena angafunse kuti, ‘Kodi n’zotheka kulemekeza munthu yemwe satilemekeza?’ Inde n’zotheka. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo. Mfumu Sauli inachititsa manyazi mwana wake Yonatani pagulu la anthu. (1 Sam. 20:​30-34) Koma Yonatani ankalemekezabe bambo ake ndipo ankawathandiza pankhondo mpaka tsiku limene bambo akewo anamwalira. (Eks. 20:12; 2 Sam. 1:23) Mkulu wansembe dzina lake Eli ananena kuti Hana waledzera. (1 Sam. 1:​12-14) Koma Hana analankhula mwaulemu kwa Eli ngakhale kuti Eliyo ankadziwika mu Isiraeli monse kuti sanali bambo komanso mkulu wansembe wabwino. (1 Sam. 1:​15-18; 2:​22-24) Anthu a ku Atene ananyoza Paulo ndipo ankanena kuti anali “wobwetuka.” (Mac. 17:18) Ngakhale zinali choncho, Paulo anawalankhula mwaulemu. (Mac. 17:22) Apa n’zoonekeratu kuti kukonda Yehova komanso kupewa kumukhumudwitsa kungatilimbikitse kuti tizilemekeza ena ngakhale pamene kuchita zimenezo n’kovuta. Tiyeni tikambirane za anthu amene tiyenera kuwalemekeza komanso zifukwa zake.

Yonatani, Sauli ndi asilikali a Chiisiraeli akumenya nkhondo atanyamula malupanga, mikondo ndi zishango.

Ngakhale kuti bambo ake ankamuchititsa manyazi, Yonatani anapitirizabe kuwathandiza pa nthawi yonse imene bambo akewo anali mfumu (Onani ndime 6)


MUZILEMEKEZA ANTHU A M’BANJA LANU

7. N’chifukwa chiyani zingamativute kulemekeza achibale athu?

7 Vuto limene limakhalapo. Popeza kuti nthawi zambiri timakhala ndi achibale athu, timadziwa zimene amachita bwino komanso zimene amalakwitsa. Ena angakhale ndi matenda omwe angachititse kuti zikhale zovuta kuwasamalira kapenanso angakhale kuti ali ndi nkhawa kwambiri. Enanso angalankhule kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa. M’malo mochititsa kuti pakhomo pawo pakhale mtendere, ena amayambitsa mavuto posalemekeza achibale awo. Zikatero banjalo silikhalanso logwirizana. Mofanana ndi nyamakazi yomwe imachititsa kuti mbali zina za thupi zisamagwire bwino ntchito, kulephera kulemekeza achibale kungachititse kuti anthu asamagwirizane. Koma mosiyana ndi nyamakazi yomwe sitingathe kupeza mankhwala ake, n’zotheka kuti anthu apachibale aphunzire kulemekezana.

8. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizilemekeza achibale athu? (1 Timoteyo 5:​4, 8)

8 Chifukwa chake tiyenera kuwalemekeza. (Werengani 1 Timoteyo 5:​4, 8.) M’kalata imene analembera Timoteyo, Paulo anafotokoza zimene anthu m’banja angachite kuti azithandizana. Iye anafotokoza kuti tiyenera kulemekeza anthu a m’banja lathu pofuna kusonyeza kuti ndife “odzipereka kwa Mulungu,” osati pongofuna kukwaniritsa udindo wathu. Mawu akuti kudzipereka kwa Mulungu akutanthauza kumulambira komanso kumutumikira mokhulupirika. Yehova ndi amene anayambitsa banja. (Aef. 3:​14, 15) Choncho tikamalemekeza anthu a m’banja lathu timakhala tikulemekeza Yehova yemwe anayambitsa banja. (1 Tim. 5:4) Chimenechitu ndi chifukwa champhamvu chotichititsa kuti tizilemekeza anthu a m’banja lathu.

9. Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti azilemekezana? (Onaninso zithunzi.)

9 Mmene tingasonyezere ulemu. Mwamuna amalemekeza mkazi wake akamamusonyeza kuti ndi wamtengo wapatali akakhala kwaokha kapenanso pagulu. (Miy. 31:28; 1 Pet. 3:7) Iye samenya mkazi wakeyo, kumuchititsa manyazi kapenanso kumuchititsa kuti azidziona ngati wachabechabe. Ariel,a yemwe amakhala ku Argentina ananena kuti: “Mkazi wanga amadwala matenda enaake omwe nthawi zina amachititsa kuti azilankhula zinthu zimene zimandikhumudwitsa. Zikatero ndimadzikumbutsa kuti zimene walankhulazo si zimene amafuna kulankhula. Ndimakumbukiranso zimene zili pa 1 Akorinto 13:​5, zomwe zimandilimbikitsa kuti ndizimulankhula mwaulemu osati kumunyoza.” (Miy. 19:11) Mkazi amalemekezanso mwamuna wake akamalankhula zabwino zokhudza mwamunayo. (Aef. 5:33) Iye amapewa kulankhula mawu achipongwe ndi onyoza kapenanso kumutchula mayina amwano. Amazindikira kuti makhalidwe amenewa ali ngati dzimbiri lomwe likhoza kuwononga ukwati wawo. (Miy. 14:1) Mlongo wina wa ku Italy, yemwe mwamuna wake amavutika ndi nkhawa, ananena kuti: “Nthawi zina ndimangoona ngati mwamuna wanga amakokomeza zinthu. Poyamba, mawu komanso nkhope yanga zinkasonyeza kuti sindimulemekeza. Koma kucheza ndi anthu amene amalemekeza ena kunandithandiza kuti ndizilemekeza kwambiri mwamuna wanga.”

Zithunzi: Mwamuna ndi mkazi akuchita zinthu zosonyeza kuti amalemekezana. 1. Mwamuna akulankhula ndi mkazi wake mokoma mtima uku akukonza chakudya kukhitchini. 2. Mkazi akuyamikira mwamuna wake pamaso pa alendo pamene mwamunayo akupereka chakudya kwa m’bale wachikulire.

Tikamasonyeza ulemu kwa anthu a m’banja lathu, timalemekeza Yehova yemwe anayambitsa banja (Onani ndime 9)


10. Kodi ana angasonyeze bwanji kuti amalemekeza makolo awo?

10 Ananu, muzimvera malamulo amene makolo anu anakhazikitsa. (Aef. 6:​1-3) Muzilankhula mwaulemu ndi makolo anu. (Eks. 21:17) Pamene makolo anu akukalamba azifunika kuti muziwathandiza. Muzichita zonse zimene mungathe powasamalira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi María, yemwe bambo ake si a Mboni za Yehova. Bambo akewo atadwala sankachita naye zinthu mokoma mtima, zomwe zinkachititsa kuti azivutika kuwasamalira. Iye anati: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kuti ndizilankhula komanso kuchita nawo zinthu mwaulemu. Ndinazindikira kuti ngati Yehova anandiuza kuti ndizilemekeza makolo anga, ndiye kuti akhoza kundipatsa mphamvu zochitira zimenezo. Panopa ndaphunzira kuti ndiyenera kulemekezabe bambo anga ngakhale atapanda kusintha khalidwe lawo.” Tikamalemekeza anthu a m’banja lathu ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina, timasonyeza kuti timalemekeza Yehova yemwe anayambitsa banja.

MUZILEMEKEZA AKHRISTU ANZANU

11. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingativute kulemekeza Akhristu anzathu?

11 Vuto limene limakhalapo. Akhristu anzathu amatsatira mfundo za m’Baibulo koma nthawi zina sangachite nafe zinthu mokoma mtima, angatiganizire zoipa kapenanso kutikhumudwitsa. Ngati Mkhristu “ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake,” zingamuvute kuti azimulemekeza. (Akol. 3:13) Ndiye n’chiyani chingatithandize kupitiriza kulemekeza Akhristu anzathu?

12. N’chifukwa chiyani kulemekeza Akhristu anzathu n’kofunika? (2 Petulo 2:​9-12)

12 Chifukwa chake tiyenera kuwalemekeza. (Werengani 2 Petulo 2:​9-12.) M’kalata yake yachiwiri, Petulo anatchula za Akhristu ena mumpingo amene ankalankhula mopanda ulemu za ‘anthu amene Mulungu anawapatsa ulemerero,’ kapena kuti akulu. Kodi angelo, omwe ankaona zimenezi zikuchitika, anachita chiyani? “Chifukwa angelowo amalemekeza Yehova” sanalankhule mawu onyoza kwa anthu amenewa. Zimenezitu n’zochititsa chidwi. Angelowa, omwe ndi angwiro, sanalankhule mwaukali zokhudza anthu odzikuzawa. M’malomwake anasiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova kuti awadzudzule komanso kuwaweruza. (Aroma 14:​10-12; yerekezerani ndi Yuda 9.) Tingaphunzirepo kanthu kuchokera kwa angelowa. Ngati timafunika kuchita zinthu mwaulemu ndi anthu otsutsa, kuli bwanji Akhristu anzathu? Choncho ‘tiziyamba ndi ifeyo’ kulemekeza anthu ena. (Aroma 12:10) Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti timalemekeza Yehova.

13-14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza anthu mumpingo? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)

13 Mmene tingasonyezere ulemu. Akulu amayesetsa kulangiza anthu ena mwachikondi. (Filim. 8, 9) Mukafuna kupereka malangizo kwa munthu muzichita zimenezo mokoma mtima, osati mutakhumudwa. Alongo akhoza kuthandiza kuti anthu mumpingo azilemekezana ngati amapewa miseche. (Tito 2:​3-5) Tonsefe tikhoza kusonyeza kuti timalemekeza akulu mumpingo pogwirizana nawo, komanso kuwayamikira pa ntchito zimene amagwira monga kutsogolera pamisonkhano ndi mu utumiki ndiponso kuthandiza anthu amene ayamba kulowera “njira yolakwika.”—Agal. 6:1; 1 Tim. 5:17.

14 Mlongo wina dzina lake Rocío ankavutika kusonyeza ulemu kwa mkulu wina yemwe anamupatsa malangizo. Iye anati: “Ndinkaona kuti mkuluyo sanandilankhule bwino. Ndikakhala kunyumba ndinkalankhula zoipa zokhudza mkuluyo. Ngakhale kuti sindinkaonetsera, mumtimamu ndinkakayikira zolinga zake ndipo ndinkaona kuti malangizo ake ndi osathandiza.” Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza Rocío? Iye anati: “Ndikuwerenga Baibulo ndinapeza lemba la 1 Atesalonika 5:​12, 13. Nditazindikira kuti sindinkasonyeza ulemu kwa m’baleyo, chikumbumtima chinayamba kundivutitsa. Ndinapemphera kwa Yehova komanso kufufuza m’mabuku athu nkhani zimene zingandithandize kusintha maganizo anga. Kenako ndinazindikira kuti vuto silinali m’baleyo koma kuti ineyo ndinali ndi mtima wonyada. Ndazindikiranso kuti kudzichepetsa ndi kumene kungandithandize kuti ndizilemekeza ena. Ndikufunikabe kusintha, koma ndaona kuti ndikamayesetsa kusonyeza ena ulemu ndimakhala ndikusangalatsa Yehova.”

Zithunzi: Mlongo wachikulire akuwerenga Baibulo ndipo akuganizira ntchito zosiyanasiyana zimene akulu amagwira mwakhama. 1. Mkulu akukamba nkhani m’Nyumba ya Ufumu. 2. Akuthandiza m’bale amene ali pa njinga ya olumala. 3. Akuchotsa sinowo panja pa Nyumba ya Ufumu.

Tonsefe tingasonyeze ulemu kwa akulu mumpingo pochita zinthu mogwirizana nawo komanso kuwayamikira pa ntchito zimene amagwira (Onani ndime 13-14)


TIZILEMEKEZA ANTHU OMWE SI AKHRISTU ANZATHU

15. N’chifukwa chiyani tikhoza kuvutika kulemekeza anthu omwe si Akhristu anzathu?

15 Vuto limene limakhalapo. Nthawi zambiri tikalowa mu utumiki timakumana ndi anthu amene sakonda Mulungu kapena Baibulo. (Aef. 4:18) Ndipo anthu ena amakana kumvetsera uthenga wathu chifukwa cha zimene anaphunzitsidwa ali ana. Mwina kumene timagwira ntchito kuli mabwana kapena anthu ena ovuta, ndipo ngati timapita kusukulu mwina kuli aphunzitsi kapena ana enanso ovuta. Pakapita nthawi tingasiye kulemekeza anthu ngati amenewa kapenanso sitingawachitire zinthu zimene timafuna kuti anthu ena atichitire.

16. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizilemekeza anthu amene sanayambe kutumikira Yehova? (1 Petulo 2:12; 3:15)

16 Chifukwa chake tiyenera kuwalemekeza. Kumbukirani kuti Yehova amaona mmene timachitira zinthu ndi anthu amene si Akhristu anzathu. Mtumwi Petulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti khalidwe lawo lingachititse kuti anthu ena ‘atamande Mulungu.’ Choncho anawalimbikitsa kuti azifotokozera ena zimene amakhulupirira “mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (Werengani 1 Petulo 2:12; 3:15.) Kaya akuimbidwa mlandu kapena akungofotokozera ena zimene amakhulupirira, Akhristuwo ankafunika kuchita zimenezo ngati ali pamaso pa Mulungu. Paja Yehova amamva zimene tikulankhula ndiponso kuona mmene tikuzilankhulira. Chimenechitu ndi chifukwa chachikulu kwambiri chotichititsa kuti tizilemekeza anthu omwe si Akhristu anzathu.

17. Kodi tingasonyeze bwanji ulemu kwa anthu omwe si a Mboni?

17 Mmene tingasonyezere ulemu. Tikakhala mu utumiki, tizipewa kunyoza anthu omwe sadziwa mfundo za m’Baibulo. M’malomwake, tiziona kuti anthu ena ndi amtengo wapatali kwa Mulungu komanso ndi otiposa. (Hag. 2:7; Afil. 2:3) Mwachitsanzo, munthu akatinyoza chifukwa cha zimene timakhulupirira tizipewa kubwezera kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti ndife anzeru kuposa iyeyo. (1 Pet. 2:23) Ngati simunalankhule bwino muzipepesa nthawi yomweyo. Kodi mungasonyeze bwanji ulemu kwa anthu amene mumagwira nawo ntchito? Muzigwira ntchito mwakhama ndipo muzisonyeza khalidwe labwino kwa anthu amene mumagwira nawo ntchito komanso mabwana anu. (Tito 2:​9, 10) Kaya ena asangalala kapena sasangalala chifukwa chakuti mumagwira ntchito mwakhama, moona mtima komanso modzipereka, Mulungu adzasangalala nanu.—Akol. 3:​22, 23.

18. Kodi kulemekeza ena n’kofunika bwanji?

18 Munkhaniyi, takambirana zifukwa zotilimbikitsa kusonyeza ulemu kwa ena. Taona kuti tikamalemekeza anthu a m’banja lathu, timalemekeza Yehova yemwe anayambitsa banja. Taonanso kuti tikamalemekeza abale ndi alongo athu timalemekeza Atate wathu wakumwamba. Ndipo tikamalemekeza anthu omwe si Akhristu anzathu, zimachititsa kuti azilemekeza Mulungu wathu wamkulu. Ngakhale anthu ena asatilemekeze, ife tiyenerabe kuwalemekeza. Tikutero chifukwa Yehova adzatidalitsa. Iye amalonjeza kuti: “Amene akundilemekeza ndidzawalemekeza.”—1 Sam. 2:30.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi tingasonyeze bwanji ulemu kwa anthu a m’banja lathu?

  • Kodi tingalemekeze bwanji Akhristu anzathu?

  • Kodi tingalemekeze bwanji anthu omwe si Akhristu anzathu?

NYIMBO NA. 129 Tipitirizebe Kupirira

a Mayina ena asinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena