Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingawapangitse Motani Ena Kundipatsa Ulemu?
“Nthaŵi zina pamene ulankhula ndi achikulire, umachita ngati ukulankhula ndi khoma.”—Paul.
“Zimandinyansa pamene achikulire samandikhulupirira.”—Matt.
“Makolo anga amandinyalanyaza kapena amayerekezera kumvetsera, pamene sakutero. Umangolankhula ndiyeno utawafunsa kuti, ‘Kodi mwamva?’ mpamene amati, ‘Mm!’ Osadziŵa zimene wanena.”—Paula.
ULEMU—kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kuchititsa ena kukupatsani ulemu ngakhale wochepa? Mumafuna kumvedwa, kutengedwa mosamala. Choncho pamene achikulire—makamaka makolo anu—ndi anzanu akunyalanyazani, kuwona malingaliro anu kukhala osafunika, kulankhula nanu monga ngati ndinu buluthu, kapena kukuuzani kuti ndinu wachichepere, kungakhaledi kopweteka.
Kufuna kulemekezedwa ndi ena kuli kwachibadwa. Baibulo lenilenilo limatilimbikitsa ‘kupeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.’ (Miyambo 3:4) Ndipo achichepere opembedza m’nthaŵi za Baibulo anatero. Mwachitsanzo, mnyamata wotchedwa Timoteo anali ndi mwaŵi wakutsagana ndi mtumwi Paulo pamaulendo ake aumishonale. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ‘anamchitira umboni wabwino abale,’ pokhala anadzipezera ulemu kwa iwo. (Machitidwe 16:1, 2) Ndipo palinso Yesu mwiniyo, yemwe monga wachichepere ‘anakulabe m’nzeru ndi mumsikhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.’—Luka 2:52.
Zowona, inu sindinu Yesu. Ndipo kupatsidwa ulemu ndi ena nkovuta pamene muli wachichepere. Kunena zowona, Baibulo limagwirizanitsa unyamata ndi ‘chibwana’ ndi mphamvu zosalamulirika; chidziŵitso ndi nzeru zimadza munthu atakula. (Miyambo 1:4; 20:29; Yobu 32:6, 7) Chotero, anthu kaŵirikaŵiri samapatsa achichepere ulemu wofanana ndi umene amapatsa achikulire. Kodi nkuchita mokondera akulu? Mwinamwake. Koma zimachitikadi m’moyo ndipo muyenera kuchita nazo. Ndiponso, achichepere ambiri adzipangira mbiri yoipa. Motero, achikulire ena amalingalira molakwa kuti achichepere onse “ngopanduka,” “amwano,” kapena “opusa.”
M’maiko ena, zikhulupiriro zofala, miyambo, ndi kusintha kwakukulu kwa kakhalidwe ka anthu zakuza mpata pakati pa achichepere ndi achikulire. Mwachitsanzo, achichepere ambiri mu Afirika ali ndi mwaŵi wakuphunzira umene makolo awo analibe. Ndiponso, amakhala m’mikangano yosatha ndi akulu awo amene amatsatira miyambo yakale. Kaŵirikaŵiri achikulire amakwiya kwambiri ndi zimene amawona mwa achichepere kukhala kupanda ulemu kapena kupanduka.
Mosasamala kanthu ndi mmene mkhalidwe wanu ungakhalire, mudzafunikiradi kuchitapo kanthu ndi kulimbikira kuti mupeze ulemu kwa ena. Koma mukhozadi kuupeza.
Sumabwera Wokha
Choyamba, muyenera kuzindikira kuti ulemu umapatsidwa kwa inu osati pachifukwa chakuti mumaufuna, ndipo simungangopangitsa munthu wina kukupatsani ulemu. Ulemu ndichinthu chimene mungadzipezere. M’nthaŵi za Baibulo mwamuna wotchedwa Yobu anali wolemekezedwa kwambiri m’chitaganya chake. “Anyamata anaima pambali atangondiwona,” anakumbukira motero Yobu, “ndipo okalamba anandinyamukira kundichitira ulemu.” Komabe, Yobu mowonekeratu anangodzipezera ulemu woterowo. “Aliyense amene anandiwona kapena kumva za ine anali ndi zabwino zoti anene ponena za zimene ndidachita,” anafotokoza tero Yobu. Inde, Yobu anali ndi mbiri yosasintha ya mkhalidwe wolungama.—Yobu 29:7-17, Today’s English Version.
Kodi ndimbiri yotani imene mwadzipangira inu eni? Kodi mwagwiritsira ntchito uphungu wopatsidwa kwa Timoteo? “Munthu asapeputse ubwana wako,” anatero Paulo. ‘Komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.’ (1 Timoteo 4:12) Nanunso mungkhale chitsanzo chabwino choyenera ulemu. Kuphunzira Mawu a Mulungu kudzakuthandizani kutero. Wamasalmo anati: ‘Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; . . . Ndiri nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu.’—Salmo 119:97, 99, 100.
Akristu anzanu adzakupatsani ulemu ngati mukulitsa nzeru yauzimu yotero. Komabe, onani kuti muyeneranso ‘kusunga,’ kapena kugwiritsira ntchito, uphungu wa Baibulo. Wachichepere Wachiafirika wotchedwa Charles analitenga mwamphamvu lamulo la Baibulo la “kupanga ophunzira” nakhala mlaliki wanthaŵi zonse pausinkhu wazaka 16 ndipo tsopano amatumikira paofesi yanthambi ya Watch Tower Society. (Mateyu 28:19, 20, NW) Chitsanzo chake chakunena mokhulupirika chapangitsa ena kumpatsa ulemu ndipo chamdzetsera chimwemwe chaumwini chochuluka. Iye akuti: “Moyo muutumiki umenewu ngwosangalatsa ndithu. Kugwira ntchito pakati pa anthu opembedza amene ali ndi chidziŵitso chochuluka kwandimangiriradi. Kwandidzetsera chimwemwe chosayerekezereka.”
Njira Zopezera Ulemu
Njira ina yofunika yopezera ulemu ndiyo kukhala chitsanzo chabwino m’makhalidwe. Salome, Mboni yachichepere Yachiafirika, akukumbukira ubwana wake kuti: “Sindinatsatire zimene ambiri ankachita. Mmalomwake, ndinalimbikira kusunga malamaulo amakhalidwe abwino Achikristu nthaŵi zonse. Ndinayesayesa kukhala wochita zinthu mosamala, wodzisungira, ndi waulemu kwa ena—ngakhale tiana.” Zowonadi, munganyodoledwe ndi kusekedwa chifukwa chokhala wosiyana. (1 Petro 4:4) Koma monga momwe zinachitikira kwa Salome, ena adzakupatsani ulemu mokakamizika kaamba ka zimenezo.
Onaninso kuti Salome anayesayesa kukhala waulemu kwa ena. Ulemu umabala ulemu unzake. Chifukwa chake Aroma 12:10 amati: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina [ndi] mnzake ulemu.” Kunama ndi kukhotetsa chowonadi, kuseka ena koipa, kunyodola anthu ena, kudzikudza kapena kuvuta ena—sindizo njira zochitira ena ulemu. Mkupita kwa nthaŵi, zimasukuluza ulemu umene ena amakupatsani.
Kwenikweni nkofunika kulemekeza ndi kupatsa ulemu amene ali ndi malo audindo. (1 Petro 2:17) Mwachitsanzo, wapolisi wina anati: “Ana lerolino samanena kuti ‘Bwana’ kaŵirikaŵiri.” Kodi mumawachitira motani amene ali ndi udindo—aphunzitsi, apolisi, ndi oyanga’anira sukulu? Ngati muli ndi mbiri yabwino yakupatsa ulemu anthu amene ali ndi udindo, nkothekera kwenikweni kuti anthu oterowo adzakuchitirani ulemu wakutiwakuti.—Yerekezerani ndi Mateyu 7:2.
Kupatsa Achikulire Ulemu
M’madera ena muli malamulo achikhalire a makhalidwe amene wachichepere amayembekezeredwa kuwatsatira. Mwachitsanzo, achikulire ambiri ku Ghana amada wachichepere amene amalankhula kwa iwo manja ali m’thumba kapena amene amawalankhuza ndi dzanja lamanzere. Miyambo yakakhalidwe yotero imawoneka yachilendo ndi yachikale kwa anthu Akumadzulo ndi achichepere ena Achiafirika, koma simatsutsidwa ndi Akristu. Ndithudi, Baibulo limatilimbikitsa kupeŵa kukwiitsa ena mosayenera.—2 Akorinto 6:3.
Mwambi wofala ku Ghana ngwakuti: “Mwana ayenera kusenda nkhono sikamba ayi.” M’mawu ŵena, ntchito zina ziyenera kuchitidwa ndi achikulire, osati achichepere. Inu mungaziwone zimenezi kukhala zopanda chilungamo ndi zokuchepsani. Koma amene amatsutsa mwambo mwakudzitengera ukumu wa akulu nthaŵi zonse amalingaliridwa kukhala wachipongwe. Mudzadzipezera ulemu waukulu kwa ena ngati mumazindikira malo anu otsika ndi kuphunzira kuchita nayo.
Pa Levitiko 19:32, Baibulo limati: ‘Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; ine ndine Yehova.’ Mukamayenda pabasi kapena zoyendera zina, kodi mofunitsitsa mumapereka mpando wanu kwa achikulire kuti akhalepo? Polankhula, kodi mumasamala ndi kalankhulidwe kanu? Kodi mumamvetsera mwaulemu?
Kupeza Ulemu wa Zikhulupiriro Zanu
Komabe, bwanji ngati ena samakupatsani ulemu chifukwa cha zikhulupiririo zanu zachipembedzo? Mwachitsanzo, achichepere amene ali amodzi a Mboni za Yehova amakakamizidwa ndi aphunzitsi ndi anzawo kutenga mbali m’madzoma akukonda dziko lawo ndi machitachita achipembedzo amene amalakwira malamulo a Baibulo. Pokhala osamvetsetsa chifukwa chake Mboni zachichepere zimatenga kaimidwe kolimbikira kotero, ena angaipidwe ndi zikhulupiriro zawo. Mwina Mboni zachichepere zingakhaledi zodedwa.
Ngakhale nditero, talingalirani mmene wachichepere Wachiafirika amene tidzamutcha Kwasi anadzisungira. “Sindinathaŵepo m’kalasi,” akufotokoza tero, “ndipo ndinachirikiza machitachita amene sanalakwire chikumbumtima changa. Chofunika koposa, ndinadziŵikitsa bwino lomwe kaimidwe kanga monga mmodzi wa Mboni za Yehova kuyambira poyamba penipeni.” Kuwona mtima kwa Kwasi, kutsimikiza, ndi miyezo yake yolimba zinapangitsa aphunzitsi ndi ophunzira omwe kumkonda. Iye awonjezera kuti: “Nthaŵi zina ndinakafotokoza kaimidwe kanga—kamodzi kwa ahedimasitala ndi gulu la aphunzitsi onse—koma zikhulupiriro zanga zinalemekezedwa nthaŵi zonse.”
Inde, dzisungireni inumwini m’njira imene imachititsa ena kukupatsani ulemu. Popanda kukakamiza ena kulandira zikhulupiriro zanu, khalani ‘okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.’ (1 Petro 3:15) Peŵani kudzisungira m’njira imene ikachititsa ‘mawu a Mulungu kuchitidwa mwano.’ (Tito 2:5) Kuteroko kumaphatikizapo kupeŵa mavalidwe ndi mapesedwe a masitayelo opambanitsa ndi kutengera mzimu wodzigangira kapena wachipanduko.
Ndithudi, Baibulo limakulimbikitsani ‘kukondwera ndi unyamata wanu,’ ndipo palibe amene amakuyembekezerani kuchita monga munthu wokalamba. (Mlaliki 11:9) Koma mwakukhala chitsanzo chabwino m’kalankhulidwe ndi m’mayendedwe anu, mukhoza kupeza ulemu ndi kudaliridwa ndi ena.
[Chithunzi patsamba 29]
Kunyamulira wachikulire katundu kuli njira yotsimikizirika yopezera ulemu