Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 3/8 tsamba 24-26
  • Kodi Ndingachite Nawo Motani Umphaŵi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingachite Nawo Motani Umphaŵi?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Msampha wa Kukhumbira
  • Pendani Chuma Chanu
  • Kusawawanya Zinthu Panyumba
  • Ndalama Zowonjezereka
  • Sukulu ndi Umphaŵi
  • Kuyang’ana Mtsogolo
  • Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Banja Lathu Ndi Losauka?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Bwanji Ngati Banja Langa Nlosauka?
    Galamukani!—1992
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 3/8 tsamba 24-26

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingachite Nawo Motani Umphaŵi?

GREGORY, wachichepere wa Kum’maŵa kwa Yuropu, anadziwona kukhala wosauka kwambiri. Anali wosakhoza kugula malaya odula kapena wailesi yamakono mofanana ndi achichepere akumaiko a Kumadzulo. Mkupita kwa nthaŵi, Gregory anagwiritsidwa mwala ndi mikhalidwe ya m’dziko lake, ndipo anasamukira ku Austria.

Pamtunda wamakilomita zikwi zambiri m’dziko lina kum’mwera kwa Afirika munali kukhala Loyiso, wachichepere wakumudzi. Pokhala m’kanyumba kakang’ono ndi banja lake, Loyiso anakhumbira achichepere okhala m’tauni lapafupi amene anali ndi “zinthu zabwino” zodabwitsa—madzi akumpopi ndi magetsi.

Ngakhale nditero, Loyiso ndi Gregory akawonedwa monga olemera ndi wachichepere Wachiafirika wotchedwa Vasco. Powopa nkhondo yachiŵeniŵeni, Vasco anayenda mtunda wamakilomita ambirimbiri kupyola nkhalango zowopsa za Afirika kokha kuti apulumuke.

Chotero liwu la “umphaŵi” limatanthauza zambiri, limatanthauza zinthu zosiyana m’maiko ndi m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Dikishonale ina Yachingelezi imamasulira “umphaŵi” kukhala chirichonse kuyambira “pakusoŵa kwadzawoneni kwa zofunika zamoyo mpaka pakusakhalako kwa zinthu zabwino zakuthupi.” Kuli komvetsa chisoni kuzindikira kuti mosasamala kanthu ndi mmene inuyo mungakhalire osauka, pali ena amene mothekera ali m’kusoŵa kwakukulu. Koma, pamene mulibe malaya abwino ovala kusukulu kapena zinthu zofunika koposa monga madzi akumpopi, sikungakutonthozeni kwenikweni kuuzidwa kuti ena ngosaukiratu kukuposani.

Chotero Baibulo silimapangitsa umphaŵi kuwonekera ngati wabwinopo. Mmalomwake, limavomerezadi mosabisa kuti: ‘Koma umphaŵi wawo uwononga osauka.’ (Miyambo 10:15) Komabe, nkhani yapapitapo inasonyeza kuti wachichepere angapeŵe zina za mbuna za umphaŵi, monga kudzisungira kwaupandu.a Mwakuyesayesa, mukhoza kukulitsa kaimidwe kamaganizo kabwino ndi kukhala ndi chiyembekezo. Komabe, kodi ndinjira zina zotani zimene zilipo zochitira ndi chitsenderezo chatsiku ndi tsiku cha kukhala wosauka?

Msampha wa Kukhumbira

“Zikadakhala bwinopo ngati tonse tinali osauka,” anadandaula motero Zanele, wachichepere Wachiafirika wazaka 17. “Koma pamene uwona ena pa TV kapena kwina kulikonse amene ali ndi zochuluka kukuposa, zimavuta kuvomereza.”

Malingaliro a Zanele ngosadabwitsa konse, makamaka polingalira kusiyana kwakukulu kwa zachuma ndi kakhalidwe kumene kumalekanitsa anthu lerolino. Ndipo powona njira imene zoulutsira nkhani zimasonyezera chuma ndi kukonda zakuthupi mopanda chifundo, mwina nanunso mungavutike ndi kukhumbira pamene muwona mmene achichepere anzanu achuma amakhalira. (Yakobo 4:5) Ngakhale nditero, mwambi Wachijeremani umachenjeza kuti: “Kukhumbira sikumadya kalikonse koma mtima wake.”—Yerekezerani ndi Miyambo 14:30.

Ndithudi, sikolakwa kwenikweni kufuna kukhala m’mikhalidwe yabwinopo. Koma umphaŵi uli chizindikiro cha dongosolo loipa la zinthu la Satana, ndipo ali Mulungu yekha amene angawongolere—ndipo adzatero—kupanda chilungamo kwa dziko. Ngati mumakhala m’dziko losauka m’zachuma, mungakhale wopanda chochita kwenikweni kuwongolera mkhalidwe wanuwo. Ndipo ngakhale ngati pangakhale mpata wakukhupuka, kumbukirani mawu a Solomo pa Mlaliki 4:4 akuti: “Ndachiwonanso chifukwa chimene anthu amalimbikira kugwira ntchito kuti apambane: nchifukwa chakuti amakhumbira kanthu kamene mnansi wawo ali nako. Koma nzachabe. Zimafanana ndi kuwomba mphepo.”—Today’s English Version.

Ngati chonulirapo chanu ndichuma zivute zitani, mungagwere mosavuta m’chiyeso chakulolera molakwa miyezo yanu yamakhalidwe. Ndiponso, mikhalidwe imene simukhoza kuilamulira ingachepetse mofulumira ndalama zanu zopezedwa movutikira—kukusiyani wosauka kwambiri kuposa ndi kalelonse. Chotero Miyambo 23:4, 5 imachenjeza kuti: ‘Usadzitopetse kuti ulemere; . . . Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.’

Pendani Chuma Chanu

Pamenepa, kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kukhala ndi maganizo akuti ‘ife kwathu nkusauka choncho basi’? Ndithudi ayi! Njira imodzi imene mungaitenge ndiyo kusumika maganizo, osati pazosoŵa zanu, koma pachuma chanu. Zowona, mungakhale ndi katundu wochepa. Koma m’bukhu lake lakuti Relationships, Dr. Tony Lake akunena kuti “munthu wosauka m’zandalama angakhale ndi chuma china, monga banja lachikondi, anansi aubwenzi kapena malo abwino okhala.” Ndithudi, chuma chotero nchamtengo wapatali kuposa ndalama! Mwambi umati: ‘Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.’ (Miyambo 15:17) Achichepere Achikristu alinso ndi chuma china chamtengo wapatali: chichirikizo cha “gulu lonse la abale.”—1 Petro 2:17, NW.

Mwina mungayesenso kuwona katundu wanu ndi maganizo abwinopo. Zingakhale zowona kuti, mungadzikhala m’kanyumba wamba, mwina ngakhale kamsasa ndithu. Mungadzivala malaya akale, othaitha, kapena azigamba. Ndipo mungalakalake zakudya zosiyanako. Koma kodi mumafunikiradi malaya amasitayelo kapena nyumba yokongola kuti mukondweretse Mulungu? Kodi mumafunikira zakudya zokhumbirika kuti mukhale ndi moyo ndi thanzi labwino? Ndithudi ayi! Monga momwe mtumwi Paulo ananenera: “Ngati tili nazo zakudya ndi malaya, zimenezo zitikwanire.”—1 Timoteo 6:8, TEV.

Eldred, mwamuna wa ku South Africa yemwe anakulira m’banja losauka, akuti: “Tinazoloŵera kuti banja lathu linali kugwiritsira ntchito mosamala ndalama ndikuti sitikapeza zonse zomwe tinazifuna.” Eldred akukumbukira kuti pamene thalauza lake lakusukulu linang’ambika, amayi ŵake ankangoliphatika chigamba. Mkupita kwa nthaŵi, linakhala ndi zigamba zochuluka kuposa nsalu yake yoyambirira! “Ndinapirira kusekedwa,” anavomereza tero Eldred. “Koma chinthu chachikulu chinali chakuti malaya athu anali aukhondo ndi okhoza kuvalidwa.”

Kusawawanya Zinthu Panyumba

Mungatengenso njira zothandiza kuwongolera mkhalidwe wanu. Baibulo limanena za amene mopusa “amawawanya ndalama atangozilandira.” (Miyambo 21:20, TEV) Pamenepa, chitani mwanzeru mwakukhala osamala kusawononga chakudya, ndalama, kapena chuma chirichonse cha m’nyumba. (Yerekezerani ndi Yohane 6:12.) Kutchova juga, uchidakwa, kusuta—ndizizoloŵezi zimene sizimangowononga ndalama komanso nzotaitsa chiyanjo cha Mulungu. (2 Akorinto 7:1) Ngati ziŵalo zina zabanja zimachita mosayenera m’nkhaniyi, perekani chitsanzo chabwino kwa izo ndi mkhalidwe wanu.—1 Timoteo 4:12.

Njira ina yowonjezerera ubwino wa banja lanu ndiyo kuthandiza makolo anu panyumba. Modzifunira athandizeni kuphika, kuyeretsa, kukonza zinthu, ndi kulimirira pabwalo kapena m’dimba. Kuteroko kudzakupangitsani kukhutira ndi zochita zanu.

Ndalama Zowonjezereka

Achichepere ena amawonjezera pandalama zabanja mwakugwira ntchito yaganyu. Loyiso, wotchulidwa poyambapo, ankagulitsa ndiwo zamasamba; zimene anazilima m’kadimba kakumbuyo kwa nyumba yawo. Dzinthu zolimidwazo zinathandizanso kudyetsa banja lake. ‘Wolima munda wake zakudya zidzamkwanira,’ imatero Miyambo 28:19. Loyiso anapeza mawu ameneŵa kukhala owona.

Achichepere ena achita nzeru kugulita zovala, zakudya, ndi nkhuni. Ena amachita ntchito zosavuta zapanyumba zokonza zinthu, kutumidwa, kapena kulera ana.

Sukulu ndi Umphaŵi

Malinga ndi 1989 Britannica Book of the Year, achichepere ambiri osauka amawona “sukulu kukhala yopanda phindu kwambiri.” Kaŵirikaŵiri sukulu m’maiko ambiri zimakhala zopanda malo ndi ziŵiya zokwanira. Ndipo pamene achichepere ayerekezera ntchito zotsika zimene angadzaloŵe ndi njira zina zoswa lamulo koma zopezera ndalama mofulumira, ena samafuna kupita kusukulu.

Komabe, kusaphunzira kumangoning’itsa msampha wa umphaŵi. Kukhala m’sukulu kumafunadi kudzilanga, koma nkwanzeru! Talingalirani dera la Howrah, shantikompaundi mu Calcutta, India. Kumeneko anthu okwanira 800,000 ali muumphaŵi wowopsa. Ana ambiri amagwira ntchito zaganyu zotsika masana; komabe, ambiri amapita kusukulu zausiku kukaphunzira. Choncho ngakhale ngati kupita kusukulu kuli kovuta, osaleka. Sukulu ingakuthandizeni kukulitsa maluso akulankhula ndi kulingalira—maluso amene tsiku lina adzakuthandizani kupeza ntchito.

Kuyang’ana Mtsogolo

“Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova.” (Miyambo 22:2) Mfundo imeneyo yathandiza achichepere a Mboni za Yehova zikwi zambiri kuchita mwachipambano ndi umphaŵi. Amazindikira kuti chimwemwe chimadalira, osati pakukhala ndi zinthu zakuthupi, koma pakupalana ubwenzi ndi Yehova Mulungu, yemwe amalandira onse ofuna kumtumikira—olemera ndi osauka omwe. Mulungu amapereka chiyembekezo cha moyo m’dziko latsopano lamtsogolo limene silidzakhala ndi umphaŵi wovutitsa uliwonse.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Pakali pano, gwiritsirani ntchito mwanzeru chuma chanu. Yang’anani mtsogolo. Kundikani chuma chauzimu. (Mateyu 6:19-21) Kuwoneni monga chitokoso kuchita ndi umphaŵi—chitokoso chimene mukhoza kuyang’anizana nacho mwachipambano.

[Mawu a M’munsi]

a Onani kope lathu la February 8, 1992.

[Zithunzi patsamba 25]

Kumango khumbira sikudzawongolera mkhalidwe wanu, koma kulimbikira kuchita bwino kusukulu kungatero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena