Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 2/8 tsamba 11-20
  • Bwanji Ngati Banja Langa Nlosauka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Ngati Banja Langa Nlosauka?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuloŵa m’Kamwa mwa Mkango
  • Mkwiyo ndi Kugwiritsidwa Mwala
  • Kusoŵa Chochita ndi Kupanda Chiyembekezo
  • Kukulitsa Ulemu Wanu
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Umphawi
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 2/8 tsamba 11-20

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Bwanji Ngati Banja Langa Nlosauka?

SHANTI tauni ya ku South Africa kumene George anakulira siimamkumbutsa zabwino. “Tinali kukhala m’mukhukhu weniweni—kamsasa kazipinda ziŵiri,” iye akukumbukira motero. Iye anali kugona m’chipinda chimodzi ndi abale ake ndi alongo asanu ndi atatu. M’nyengo yachisanu, ankatuluka kunja mosasamala kanthu za kuzizirako kukatunga madzi kumpopi umodzi umene unatumikira chitaganya chonse. “Koma chimene ndinada kwambiri ponena za kukulira muumphaŵi,” akutero George, “chinali kuwona atate ŵanga akuvutika ndi kugwira ntchito yolimba koma nkungopeza tindalama totisunga amoyo basi. Chinandivuta kwenikweni powona kuti panalibe njira yochitiramo.”

Vuto landalama ndilo khalidwe lamoyo m’maiko osatukuka. Ndipo ngakhale maiko okhupuka a Kumadzulo ali ndi ziŵerengero zodabwitsa za anthu osauka. Mwinamwake ndinu mmodzi wa iwo. Mofanana ndi George mungadziwonedi kukhala m’vuto la umphaŵi. Pamene kuli kwakuti malingaliro oterowo ngomveka, angakupangitseninso kuchita mwanjira zimene zimakulitsa mavuto aumphaŵi mmalo mowachepetsa.

Kuloŵa m’Kamwa mwa Mkango

Achichepere ambiri osauka amayesa kuthaŵa kupweteka kwa umphaŵi mwakugodomalitsa malingaliro awo ndi zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala ogodomalitsa. Malinga ndi wofufuza Jill Swart, ana am’khwalala mumzinda wina wa kummwera kwa Afirika “samangosuta glu kwakukulukulu ‘kuti asangalale’. Amaugwiritsira ntchito . . . kuti apeŵe kuzizira, kusungulumwa ndi njala.”

Koma kodi achichepere ameneŵa amamva motani pamene nzeru zibwereramo ndi kumwerekera kwa mankhwala ogodomalitsa kutatha? Jill Swart anatchula zizindikiro monga “kuchita tondovi kwakukulu,” “chiwawa,” “kukwiya msanga,” “kusawona bwino,” ndi mavuto ena akuthupi ambiri amene sanganenedwe mpang’ono ponse kukhala “njira [yabwino] yothaŵira” umphaŵi.

Mfumu yanzeru Solomo inati: “Wakumwaimwa . . . adzasauka; ndipo kusinza kudzabveka munthu nsanza.” (Miyambo 23:21) Kuyesa kuphimba mkhalidwe weniweni wa umphaŵi mwakusintha kaimidwe ka malingaliro ndi zakumwa zoledzeretsa, glu, kapena mankhwala ogodomalitsa sikudzathetsa vutolo. (Yerekezerani ndi Miyambo 31:7.) Monga momwe Maria, msungwana wazaka 16 wa m’banja losauka la kholo limodzi ku South Africa, ananenera: “Kuyesa kuthaŵa zenizeni kumachititsa mavuto owonjezereka kuposa omwe kumathetsa.” Ndiponso, ndalama zochuluka zotaidwira zizoloŵezi zowononga zotero zimakulitsirako umphaŵi wa munthuwe. Kokha pamene wachichepere wosauka ayang’anizana ndi mkhalidwe wake moyenerera mpamene angayembekezere kuchita nawo mkhalidwewo.

Mkwiyo ndi Kugwiritsidwa Mwala

Pokwiya ndi kukhala kwawo m’chitaganya chosauka, achichepere ambiri amasonyeza mkwiyo wawo mwakuchita chiwawa, kuwononga dala zinthu, kuba, ndi mitundu ina ya maupandu ochitidwa ndi achichepere. The World Book Encyclopedia imanena kuti achichepere otero amawona zimenezo monga “njira yokha yothaŵira kusungulumwa, umphaŵi, ndi mavuto ena.” George, wotchulidwa poyambapo, akukumbukira kuti ausinkhu wake ena anakwiya, kugwiritsidwa mwala, nagwirizana ndi magulu azigaŵenga amene anavuta kwawoko. Akuwonjezera kuti “kwakukulukulu iwo anali kumenya anthu ndi kuba kuti apeze ndalama zochirikiza moyo.” Koma achichepere ena amayesa kugonjetsa umphaŵi mwakudziloŵetsa m’machitachita osaloledwa odzetsa phindu, monga kugulitsa mankhwala ogodomalitsa mwakabisira.

Komabe, mmalo mothetsa umphaŵi, kupulupudza kumangoipitsirako zinthu. Nyonga imene ikanagwiritsiridwa ntchito m’machitachita othandiza—monga kuphunzira luso lina kapena ntchito yothandiza—imataidwa pachabe. Mmalo mowongolera mkhalidwe wake, wachichepere wopulupudzayo amangodzidzetsera mavuto owonjezereka akuthupi ndi amaganizo. Achichepere ena zimaŵagwetsera m’ndende kwa nyengo yaitali—kapena kufa imfa yachiwawa. Monga momwe Mfumu Solomo anachenjezera: “Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa.”—Miyambo 13:18.

Kusoŵa Chochita ndi Kupanda Chiyembekezo

Mwina ziyambukiro zovulaza kwambiri zimene umphaŵi ungakhale nazo pa wachichepere ndizo malingaliro ovutitsa a kudzimva wopanda pake ndi wapansi. Kwa ambiri, mlingo waukulu wa umphaŵi m’mbali zonse za moyo wawachotsera chiyembekezo chirichonse cha kuwongolera mkhalidwe wawo. The World Book Encyclopedia imanena kuti kaŵirikaŵiri achichepere “amakhala ndi malingaliro amodzimodziwo osoŵa chochita ndi kupanda chiyembekezo amene makolo awo akhala nawo.” Mkupita kwa nthaŵi, pamakhala “umoyo wa osauka,” wochititsa mikole yake kungodzipereka ku moyo wa mavuto.

Koma kodi kukulitsa malingaliro akusoŵa chochita ndi kupanda chiyembekezo kudzawongolera mkhalidwe wanu? Ayi! Mosiyana, kuteroko kumangopitiriza umphaŵi. Monga momwe mwambi wakale umanenera: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Ngati mlimi angoganizira zochitika zoipa—mphepo imene ikhoza kuulutsa mbewu zake kapena mvula imene ingavumbwitse dzinthu zake—adzalephera kuchitapo kanthu. Mofananamo, mwakukhala ndi malingaliro oipa, mungalepheretse zoyesayesa zonse zakuwongolera mkhalidwe wanu.

Chotero Mfumu Solomo anapereka uphungu wowonjezereka uwu: ‘Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino.’ (Mlaliki 11:6) Inde, mmalo molefulidwa ndi mantha a kulephera kapena lingaliro lakuti zinthu sizidzasintha, chitanipo kanthu! Pali zinthu zimene mungachite kukuthandizani mwapang’onopang’ono kuchotsa malingaliro oipa ndi kukhala ndi abwino.

Kukulitsa Ulemu Wanu

Talingalirani James wazaka 11. Amakhala ndi amayi ŵake ndi mlongo wake m’shanti kopaundi pafupi ndi Johannesburg, South Africa. Iwo alibe zinthu zakuthupi kwenikweni. Mapeto a mlungu aliwonse James amathandiza kumanga Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kwawoko. Zimenezi sizimangotenga nthaŵi imene akanasungulumwa nayo popanda chochita komanso zimampatsa chikhutiro. James akunena mosekerera kuti: “Tsiku lirilonse pambuyo pa ntchito yakumanga holo, ndimakhala wokhutiritsidwa kwambiri!” Ngakhale kuti wachichepereyu ngwosauka, alinachobe chuma chamtengo wapatali: nthaŵi ndi nyonga.

Ntchito ina yobala zipatso ndiyo kuphunzitsa Baibulo kunyumba ndi nyumba. (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zachichepere zambiri zimaichita ntchitoyo mokhazikika. Mwakutero sizimangopatsa ena chiyembekezo cha moyo wabwinopo mtsogolo komanso zimakulitsa malingaliro awo a kudzilemekeza, kufunika kwawo, ndi ulemu. Zowona, munthu samapeza ndalama mwakuchita ntchito yotero. Koma kumbukirani uthenga umene Yesu anapereka kwa Akristu mumpingo wamakedzana wa Sarde. Iwo anali osauka mwakuthupi, koma chifukwa cha mkhalidwe wawo wauzimu wakuya, Yesu anakhoza kuwauza kuti: ‘Ndidziŵa chisauko chako, ndi umphaŵi wako komatu uli wachuma.’ Kwakukulukulu, chifukwa cha kusonyeza kwawo chikhulupiriro mokangalika m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu, iwo akakhala achuma kwambiri, kulandira korona wa moyo wosatha.—Chivumbulutso 2:9, 10.

Kukulira muumphaŵi sikuli kosavuta. Komabe, palibe chifukwa chochitira manyazi, kudziwona kukhala wopanda chochita, kapena wopanda chiyembekezo ponena za mkhalidwe wanu. Umphaŵi ulipo chifukwa chakuti ‘[munthu, NW] apweteka mnzake pomlamulira.’ (Mlaliki 8:9) Umboni umasonyeza kuti posachedwapa Mulungu adzalanda ulamuliro wa zochitika za padziko lapansi ndi kuchotsapo umphaŵi ndi ziyambukiro zake zosakaza. (Salmo 37:9-11) Mwana wake, Kristu Yesu, adzaloŵetsa mabiliyoni a anthu m’Paradaiso wapadziko lapansi, monga momwedi analonjezera wochita zoipa wosauka amene anasonyeza chikhulupiriro mwa iye pamene iwo anali kufa pamitengo yozunzirapo. (Luka 23:43) Komabe, pakali pano, pali zambiri zokuthandizani zimene mungachite kuti mupirire umphaŵi. Zimenezo zidzapendedwa m’kope lamtsogolo.

[Bokosi patsamba 13]

“Ndinadzimva Kukhala Wogwidwa mu Msampha wa Umphaŵi”

George anali Mfirika wachichepere amene anafunitsitsa kupitiriza sukulu ndi kumaliza mapunziro ake. Analingalira kuti mwakutero akakhoza kupeza ntchito yamalipiro abwino imene ikamchotsa iye ndi banja lake muumphaŵi. Komabe, zinthu sizinakhale tero. Banja lake linaloŵa m’mavuto aakulu andalama moti pambuyo pophunzira kwa zaka zisanu ndi chimodzi zokha, George anakakamizika kuleka sukulu kuti akafune ntchito. Mkupita kwanthaŵi anapeza ntchito yoika mabotolo m’makeleti pakampani yopanga zakumwa, akumalandira marandi 14 okha pamlungu ($5, U.S.). Malipiro ake apamlunguwo anangothera m’kusamalira banja lake.

“Ngakhale kuti ndinadzimva kukhala wogwidwa mu msampha wa umphaŵi,” akutero George, “ndinadzawona kuti kugwirizana ndi gulu lazigaŵenga kapena kuba kuti ndipeze ndalama zochirikiza moyo sikukathandiza. Lerolino, ausinkhu wanga ambiri amene anachita zinthuzo ali olephera opanda chiyembekezo, akapolo a zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala ogodomalitsa, kapena ali m’ndende. Ena anaphedwadi chifukwa cha njira yawo yamoyo.”

Ndiyeno George anagwirizana ndi Mboni za Yehova. “Chimodzi cha zinthu zoyamba zimene ndinawona,” akutero George, “chinali chakuti pamisonkhano Yachikristu, aliyense anadza kwa ine ndi kulankhula nane mwaulemu.” Awonjezera kuti: “Mwapang’onopang’ono ndinapeza chidaliro ndi ulemu wanga zimene ndinalibe kalelo.” George anapezanso chitonthozo chachikulu m’malemba Abaibulo monga Salmo 72:12, 13, limene limati: ‘Pakuti [Mfumu Yaumesiya] idzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; . . . Idzachitira [chisoni, NW] wosauka ndi waumphaŵi, nidzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.’ Malonjezo a Baibulo anamdzaza ndi chikondwerero chatsopano ndi chiyembekezo m’moyo.

Mutamuwona George lero, simungaganizire konse kuti anamenya nkhondo yaikulu motero kuti asinthe malingaliro ake akusoŵa chochita ndi kupanda chiyembekezo kukhala malingaliro abwino. Monga mwamuna wokwatira wachimwemwe, tsopano amatumikira monga woyang’anira wotsogoza mumpingo wa Mboni za Yehova ku Soweto, South Africa.

[Zithunzi patsamba 12]

Kugwiritsira ntchito nthaŵi yanu ndi nyonga kuchita kanthu kena kopindulitsa nkwabwinopo koposa kudzilola inu eni kugwera m’malingaliro opanda chiyembekezo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena