Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 3/8 tsamba 30-31
  • Kodi Mulungu Ali Chinsinsi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Ali Chinsinsi?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingadziŵe Zonse Ponena za Mulungu?
  • Kodi Ndichinsinsi Chopambanitsa?
  • Zinsinsi—Zachikunja ndi Zachikristu
  • Kulambira Mulungu M’chowonadi
  • Gawo 1—Kodi Yesu ndi Ophunzira Ake Anaphunzitsa Chiphunzitso cha Utatu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana Ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • “Utatu Wodalitsidwa”—Kodi Uli mu Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Bodza Lachiwiri: Mulungu ndi Wosamvetsetseka
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 3/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Ali Chinsinsi?

“Kodi chinsinsi nchiyani? Kwakukulukulu, chinsinsi ndicho chowonadi chimene mwachibadwa sichotheka kuchimvetsetsa kapena kupereka umboni wake. . . . Kodi chinsinsi chachipembedzo nchiyani? Ndichowonadi chinachake cha Mulungu chimene tiyenera kuchikhulupirira, ngakhale kuti sitingathe kuchimvetsetsa kapena kupereka umboni wake. Kodi zinsinsi zazikulu zachipembedzo nzotani? Izi ndizinsinsi za Utatu Wopatulika, Kubadwa m’Thupi Lina ndi Kuwomboledwa.”—Abrégé de l’exposition de la doctrine chrétienne, 1901 (Kulongosola Kwachidule kwa Chiphunzitso Chachikristu)

MAWU apamwambaŵa ndiamene bukhu lolembedwa kuchiyambi kwa zaka za zana la 20 linafotokozera mwachidule lingaliro la Tchalitchi cha Roma Katolika la chinsinsi. Ndiponso, Guide des difficultés de la foi catholique (Chothandizira Mavuto a Chikhulupiriro Chachikatolika, 1989) lofalitsidwa posachedwapa limasonyeza kuti mfundo zachiphunzitso zoterozo nzofunikirabe pamene linati: “Sikukopeka ndi zenizeni zosadziŵika kokha kumene kumapangitsa Mkristu kuvomereza kukhalako kwa zinsinsi za Chiphunzitso cha chipembedzo chake. Ngati azikhulupirira izo, chikhulupiriro chake chimazikidwa kotheratu pa Mawu a Mulungu.” Koma kodi “Mawu a Mulungu” amanenanji? Kodi Mulungu ndichinsinsi?

Kodi Tingadziŵe Zonse Ponena za Mulungu?

Baibulo limatipatsa tsatanetsatane wochuluka ponena za Mulungu monga Munthu, ponena za mikhalidwe yake ndi ponena za mmene amachitira ndi mtundu wa anthu. Koma limalongosolanso kuti nkosatheka kwa munthu kumvetsetsa nzeru zake ndi luntha lake. Chifukwa chake, mneneri Yesaya akunena kuti njira za Mulungu ndi malingaliro zipambana za munthu.—Yesaya 55:8, 9.

Kusakhoza kudziŵa zonse za Mulungu sikuyenera kutidabwitsa. Mwachitsanzo, ngakhale kuti chidziŵitso chathu cha thambo lachilengedwe chikuwonjezereka nthaŵi zonse, asayansi akuvomereza kuti mwinamwake sadzakhoza konse kumvetsetsa mokwanira zinsinsi za tinthu tatingo’ono koposa kapena zazikulu koposa. Motero kodi ndimotani mmene cholengedwa chirichonse chingadziŵire kotheratu kuya kwa nzeru za Mulungu, amene ndiye Mlengi? Yobu anavomereza kwa Yehova kuti: ‘Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, zondidabwitsa, zosazidziŵa ine.’ (Yobu 42:3; yerekezerani ndi Aroma 11:33.) Chotero, kumdziŵa Mulungu kotheratu, m’mbali zina, nkosatheka ndi nzeru zathu zochepa. Komabe, ziphunzitso za matchalitchi ambiri zimapitirira malire a mawu omvekera bwino ameneŵa.

Kodi Ndichinsinsi Chopambanitsa?

Bukhu lanazonse Lachikatolika lofalitsidwa posachedwapa lotchedwa Théo limati: “M’ziphunzitso za tchalitchi, liwu lakuti chinsinsi likhoza kutanthauzanso chimene Mulungu wavumbula ponena za iyemwini, mwachitsanzo, kukhalapo kwake monga utatu.” Monga momwe ziriri m’mabuku azaumulungu ambiri, lingaliro loyambitsidwa kotheratu panopa nlakuti ‘popeza kuti kumdziŵa Mulungu kuli chinsinsi chosakanika, siziyenera kutidabwitsa kuti Mulungu ali Utatu ndikuti Utatu umenewu ndichinsinsi.’ Kodi kulingalira koteroko nkwamaziko owona?

Choyamba, mabuku ambiri amavomereza, monga momwe imachitira The New Encyclopædia Britannica, kuti “liwu lakuti Utatu, ngakhale chiphunzitso choterocho, mulibemo mu Chipangano Chatsopano.” Ndiponso, mbiri ya chiphunzitsochi imasonyeza kuti chaphatikiza pamodzi malingaliro ambirimbiri otengedwa ku nthanthi zachikunja zimene zinaloŵetsedwa m’ziphunzitso za tchalitchi zaka makumi ambiri pambuyo pa kufa kwa atumwi. Chotero, palibe umboni weniweni wakuti chinsinsi cha Utatu chimapezeka m’Baibulo.a

Talingalirani: Popeza kuti nkosatheka kudziŵa zonse ponena za Mulungu, kodi kukakhala kwanzeru kwa Mulungu kubisa amene iye ali? Ayi, iye afuna kuti anthu onse amdziŵe. (Yohane 17:3; yerekezerani ndi Ahebri 8:11.) Ndipo kodi kukakhala kwanzeru kwa awo amene amafunadi kumkondweretsa iye kubisa amene iye ali? Tifotokoze mwafanizo: Ngati mwaŵi wokha umene wina ali nawo wowonera malo okongola akunja kwamzinda ndikupyolera pazenera, kodi kukakhala kwanzeru kuphimba zeneraro, akunena kuti: ‘Ziri bwino ngakhale ataliphimba pakuti satha kuwona zonse ziri pamalo apataliwo?’ Ndithudi ayi! Baibulo ndiponso kulingalira kwabwino zimasonyeza kuti chidziŵitso chathu cha Mulungu nchochepa mokhala ndi chifuno. Koma malire ameneŵa samalungamitsa kutembenuza chidziŵitso chathu cha Mulungu kukhala chiphunzitso chachinsinsi, monga Utatu, chimene chimangosokoneza kummvetsetsa kwathu iye.

Zinsinsi—Zachikunja ndi Zachikristu

Ndiponso, pamene liwu lakuti “chinsinsi” lipezeka m’Malemba, silimatanthauza “chidziŵitso chobisidwa,” monga momwe limatengedwera nthaŵi zonse. Ziri monga momwe Théo ikutikumbutsira moyenera kuti: “Liwu lakuti chinsinsi silimatanthauza zimodzimodzizo panopa. Kwa Akristu limatanthauza chinachake chimene mwachibadwa nchobisika kapena chosapezeka, koma chimene Mulungu afuna kuwauza . . . nafunanso kuti akhale nacho.”

Liwu Lachigiriki my·steʹri·on (“chinsinsi,” kapena “chinsinsi chopatulika”) linagwiritsiridwa ntchito kwanthaŵi 20 ndi mtumwi Paulo m’lingaliro linalake. Iye analigwiritsira ntchito kutanthauza chinsinsi chopatulika chimene chakhala chobisika kwa nthaŵi yaitali koma chimene Mulungu anachivumbula pamene Anatuma Yesu padziko lapansi. Yesu Kristu, mphulumutsi wa mtundu wa anthu, anali mbali yofunika ya “mbewu” yolonjezedwa imene Mulungu akagwiritsira ntchito kuwombola mtundu wa anthu, Amene ‘kupyolera mwa iye mitundu yonse yapadziko ikadalitsidwa’ ndiamene akakhala ndi oloŵa naye nyumba kumwamba. (Genesis 3:15; 22:18; Aroma 8:17) Mbali zobisika zimenezi, kapena zinsinsi, zinali zobisika kwa atumiki a Mulungu okhalako Chikristu chisanafike koma zinavumbulidwa ndi Yehova panthaŵi yoyenera. (Aefeso 1:9; Akolose 1:26) Mwachimwemwe, chidziŵitso chimenechi sichinasungidwire oŵerengeka osankhidwa okha—monga momwe ziriri ndi zinsinsi zazipembedzo zina—koma ziyenera kulengezedwa kwa anthu ambiri monga momwe kungathekere popanda tsankhu.—Aefeso 6:19, 20.

Kulambira Mulungu M’chowonadi

Baibulo liri ndi chidziŵitso chokwanira chakuti timlambire nacho Mulungu m’njira imene amaivomereza. Kutalitali ndi kuphunzitsa Utatu, ilo limavumbula momvekera bwino ukulu wa Mulungu ndi malo a Yesu wogonjera kwa iye. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: ‘Atate ali wamkulu kwa ine.’ (Yohane 14:28; 1 Akorinto 15:28) Baibulo limasonyezanso kuti mzimu woyera uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, imene imatsogolera atumiki ake okhulupirika.—Machitidwe 2:1-4.

Polankhula ndi mkazi Wachisamariya, Yesu anasonyeza kuti, kuti munthu akondweretse Mulungu, ayenera kulambira Iye ‘mumzimu ndi m’chowonadi.’ Iye anawonjezera kuti ‘Atate afuna otere akhale olambira ake.’ (Yohane 4:21-24) Ziri kwa aliyense wa ife kufunafuna chidziŵitso cholongosoka chimenechi chimene chidzatibweretsera madalitso ngati tidalira pa Mawu a Mulungu mmalo molandira miyambo yachinsinsi yopangidwa ndi anthu, imene imachitsamwitsa icho.

[Mawu a M’munsi]

a Onani brosha yakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 1990.

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

All rights reserved

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena