MARCH 16-22, 2026
NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha
N’chifukwa Chiyani Timafunikira Dipo?
“Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli?”—AROMA 7:24.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene dipo limathandizira kuti Yehova azitikhululukira, tikhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wangwiro komanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi iye.
1-2. N’chifukwa chiyani timafunikira winawake kuti atipulumutse? (Aroma 7:22-24) (Onaninso chithunzi.)
TAYEREKEZERANI kuti nyumba yagwa ndipo munthu amene anali m’nyumbayo wakwiririka moti akukanika kutulukamo. Chomwe munthuyo angakwanitse kuchita ndi kukuwa n’kumayembekezera kuti anthu ena amupulumutse basi.
2 Mmenemu ndi mmene zilili ndi tonsefe. Tikutero chifukwa Adamu atasankha kusamvera Yehova, anakhala wochimwa. Kenako anapatsira ana ake uchimowo. Zotsatira zake, anthu tonse tinakwiririka mu uchimo umene tinatengera kwa Adamuyo moti sitingathe kudzipulumutsa tokha. M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anafotokoza bwino za uchimo umene tili nawo. (Werengani Aroma 7:22-24.) Iye anapempha kuti apulumutsidwe ‘ku thupi limene linkamuchititsa kuti afe.’ Zinali ngati Paulo wakwiririka mu uchimo umene mulimonsemo ukanachititsa kuti afe. (Aroma 6:23) Ndi mmene zililinso ndi ife. Timafunikira kupulumutsidwa ku uchimo ndi imfa.
Mofanana ndi munthu yemwe akufunika kupulumutsidwa atakwiririka nyumba itamugwera, ifenso tinakwiririka ndi uchimo ndipo tikufunikira kupulumutsidwa (Onani ndime 1 ndi 2)
3. Kodi dipo limatipulumutsa m’njira ziti?
3 Paulo atafotokoza za uchimo umene ankalimbana nawo, anafotokozanso za zinthu zina zabwino zomwe zimatipatsa chiyembekezo. Iye atafunsa kuti, “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli?” anadziyankha yekha kuti: “Mulungu adzandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) Apa Paulo ankanena za nsembe ya dipoa ya Yesu. Dipoli lingatipulumutse potithandiza kuti (1) machimo athu akhululukidwe, (2) tikhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wangwiro komanso (3) tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wathu. Kukambirana mfundo zitatuzi, kutithandiza kuti tizikonda kwambiri Yehova, “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13) Kutithandizanso kuti tiziyamikira kwambiri Yesu, amene kudzera mwa iye “tinamasulidwa ndi dipo.”—Akol. 1:14.
DIPO LIMATHANDIZA KUTI MACHIMO ATHU AZIKHULULUKIDWA
4-5. N’chifukwa chiyani tonsefe timafunikira dipo? (Mlaliki 7:20)
4 Tonsefe timachimwa, kaya mu zolankhula kapena mu zochita. Choncho timafunikira dipo kuti machimo athu azikhululukidwa. (Werengani Mlaliki 7:20.) Machimo ena amakhala aakulu. Mwachitsanzo, mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, munthu akachita chigololo kapena akapha mnzake, nayenso ankafunika kuphedwa. (Lev. 20:10; Num. 35:30, 31) N’zoona kuti si machimo onse amene ndi aakulu chonchi, komabe tchimo ndi tchimo basi. Chitsanzo ndi zimene Davide ananena kuti: “Ndidzakhala wosamala ndi zochita zanga kuti ndisachimwe ndi lilime langa.” (Sal. 39:1) Izitu n’zoona chifukwa nthawi zina tikhoza kuchimwa pa zimene talankhula.—Yak. 3:2.
5 Taganizirani zimene munalankhulapo kapena kuchita m’mbuyomu. Kodi pali zina zimene mumalakalaka mukanapanda kuzilankhula? Kodi pali zina zomwe munalakwitsa zomwe mumanong’oneza nazo bondo? N’zosachita kufunsa kuti mwayankha kuti inde pa mafunso onsewa. Baibulo limati: “Tikamanena kuti, ‘Tilibe uchimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza ndipo mumtima mwathu mulibe choonadi.”—1 Yoh. 1:8.
6-7. N’chiyani chimachititsa Yehova kuti azitikhululukira machimo athu? (Onaninso chithunzi.)
6 Dipo limachititsa kuti zikhale zotheka kuti Yehova azitikhululukira machimo. (Aef. 1:7) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amangonyalanyaza zimene timalakwitsa ngati kuti alibe nazo ntchito. Yehova safuna kuti tizichimwa. (Yes. 59:2) Chifukwa choti ndi wachilungamo, iye anafunika kuchita chinachake chimene chikanapangitsa kuti zikhale zotheka kuti azitikhululukira.
7 Chilamulo cha Mose chinkanena kuti Aisiraeli ankafunika kupereka nsembe za nyama kuti machimo awo akhululukidwe. (Lev. 4:27-31; 17:11) Nsembezi zinkaimira nsembe yabwino kwambiri ya Yesu komanso madalitso obwera chifukwa cha nsembeyi. Nsembe ya Yesu inachititsa kuti zikhale zotheka kuti Yehova azitikhululukira machimo. Zimene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto zimasonyeza kuti ankamvetsa kufunika kwa nsembe ya Yesu. Atatchula makhalidwe oipa omwe anthuwo ankachita poyamba, anawauzanso kuti: “Mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mukuonedwa ngati olungama mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akor. 6:9-11.
Nsembe za nyama zimene zinkaperekedwa pophimba machimo, zinkaimira nsembe ya Yesu komanso madalitso amene adzabwere chifukwa cha nsembeyi (Onani ndime 6 ndi 7)
8. Kodi n’chiyani chimene mungachiganizire pamene mukukonzekera kudzapezeka pa Chikumbutso cha chaka chino?
8 Mukamakonzekera Chikumbutso cha chaka chino, muziganizira mmene moyo wanu ulili chifukwa choti Yehova amakhululukirani. Mwachitsanzo, chifukwa cha dipo la Yesu simuyenera kumadziimba mlandu pa machimo amene munachita m’mbuyomu ndipo munalapa. Nanga bwanji ngati mumavutika kuvomereza mfundo imeneyi? Mwina mumadziuza kuti, ‘Ndikudziwa kuti Yehova anandikhululukira koma ineyo ndikulephera kudzikhululukira.’ Ngati mumamva choncho, muzikumbukira mfundo iyi: Yehova ndi amene ali ndi udindo wotikhululukira ndipo anapereka udindo woweruza kwa Mwana wake. Yehova sanakupatseni inuyo kapena wina aliyense udindo wosankha amene iyeyo akuyenera kumuchitira chifundo kapena ayi. Baibulo limanena kuti: “Ngati tikuyenda mʼkuwala mofanana ndi mmenenso [Yehova] alili mʼkuwala, . . . magazi a Yesu, yemwe ndi Mwana wake, akutiyeretsa ku machimo onse.” (1 Yoh. 1:6, 7) Tizikhulupirira kwambiri mfundo imeneyi ngati mmenenso timachitira ndi mfundo zonse za m’Baibulo. Dipo linapangitsa kuti zikhale zotheka kuti Yehova azitisonyeza chifundo ndipo Baibulo limanena kuti iye ndi “wokonzeka kukhululuka.”—Sal. 86:5.
DIPO LIMATITHANDIZA KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO CHODZAKHALA NDI MOYO WANGWIRO
9. Kodi m’Baibulo mawu akuti uchimo amaphatikizapo chiyani? (Salimo 51:5 komanso mawu a m’munsi.)
9 M’Baibulo mawu akuti “uchimo” samangonena za kuchita zolakwika koma amanenanso za kupanda ungwiro kumene tonsefe timabadwa nako. (Werengani Salimo 51:5 komanso mawu a m’munsi.) Uchimowu umatichititsa kuti tizifuna kuchita zinthu zolakwika. Umachititsanso kuti matupi athu akhale ofooka ndipo timadwala, timakalamba komanso kufa. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa chifukwa chake ana amene angobadwa kumene, omwe sanachitepo tchimo lililonse amadwala ngakhalenso kufa. Zimatithandizanso kumvetsa chifukwa chake anthu abwino ndi oipa omwe amavutika komanso kumwalira. Tonsefe timakumana ndi mavutowa chifukwa choti tinatengera uchimo kwa Adamu.
10. Kodi Adamu ndi Hava anakhudzidwa bwanji atachimwa?
10 Taganizirani mmene uchimo unakhudzira banja loyambirira. Uchimo unachititsa kuti avutike kwambiri. Atangochimwa, nthawi yomweyo Adamu ndi Hava anayamba kuvutika chifukwa chophwanya lamulo la Mulungu lomwe linali ‘litalembedwa m’mitima mwawo.’ (Aroma 2:15) Iwo anazindikira kuti zinthu zasintha ndipo sizikuyendanso bwino. Anakakamizikanso kuti avale masamba pobisa mbali zina za thupi lawo ndipo anabisala kuti Mulungu asawaone. (Gen. 3:7, 8) Kwa nthawi yoyamba, Adamu ndi Hava anayamba kudziimba mlandu, kukhala ndi nkhawa, kudziona kuti ndi osatetezeka, kumva ululu komanso kuchita manyazi. Iwo ankafunika kulimbana ndi zinthu zimenezi mpaka tsiku limene anamwalira.—Gen. 3:16-19.
11. Kodi uchimo umatikhudza bwanji?
11 Uchimo umatikhudza mofanana ndi mmene unakhudzira banja loyambirira. Uchimo umatichititsa kuti tizimva kupweteka komanso tizikhala ndi nkhawa. Ngakhale titayesetsa kuti tikhale ndi moyo wabwino, pamakhalabe mavuto ena omwe sitingathe kuwathetsa. Zili choncho chifukwa Baibulo limanena kuti anthufe ‘tinaweruzidwa kuti tikhale opanda pake.’ (Aroma 8:20) Mfundo imeneyi imakhudza munthu aliyense payekha komanso anthu onse. Mwachitsanzo, anthu ayesetsa kuti athetse kuwonongeka kwa chilengedwe, zachiwawa, umphawi komanso kukhazikitsa mtendere padziko lonse, komabe zawakanika. Koma chifukwa cha dipo tikuyembekezera kuti zinthu zidzayamba kuyenda bwino.
12. Kodi tikuyembekezera chiyani chifukwa cha dipo?
12 Dipo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo chakuti ‘chilengedwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka.’ (Aroma 8:21) Izi zikutanthauza kuti tikadzakhala angwiro m’Paradaiso sitizidzadwalanso, kuvutika maganizo, kudziimba mlandu, kuchita manyazi, kudzimva kuti ndife osatetezeka, kumva kupweteka kapenanso kuda nkhawa. Kuwonjezera pamenepa “Kalonga Wamtendere,” Yesu, amene anapereka dipo chifukwa cha ife, ndi amene azidzalamulira. Iye adzathandiza anthu kuti athetse mavuto amene sangathe kuwathetsa paokha.—Yes. 9:6, 7.
13. Kodi chinanso n’chiyani chimene mungachiganizire pamene mukukonzekera kudzapezeka pamwambo wa Chikumbutso wa chaka chino?
13 Taganizirani mmene moyo udzakhalire mukadzakhala angwiro, kudzuka m’mawa uliwonse mukumva bwino komanso mulibe nkhawa kuti inuyo kapena wachibale wanu avutika ndi njala, adwala kapenanso amwalira. Ngakhale panopa mukhoza kukhala ndi mtendere ngati ‘mumakhulupirira kwambiri zinthu zimene tikuyembekezera zomwe zili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo nʼzotsimikizika komanso zokhazikika.’ (Aheb. 6:18, 19) Mofanana ndi nangula amene amathandiza kuti boti likhazikike, chiyembekezo chathu chimatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tizipirira mavuto alionse amene tikukumana nawo. Tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova adzapereka “mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Chifukwa cha dipo, timalimbikitsidwa komanso timayembekezera kuti zinthu m’tsogolomu zidzakhala bwino.
DIPO LIMATITHANDIZA KUTI TIKHALENSO PA UBWENZI NDI YEHOVA
14. Kodi uchimo unasokoneza bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?
14 Adamu ndi Hava atachimwa, anthu anatalikirana kapena kuti kulekanitsidwa ndi Mulungu. Ndipotu Baibulo limanena kuti ubwenzi wa anthu ndi Mulungu unasokonekera. (Aroma 8:7, 8; Akol. 1:21) Izi zili choncho chifukwa Yehova ndi wolungama ndipo salekerera machimo. Ponena za Yehova, Baibulo limanena kuti: “Maso anu ndi oyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa, ndipo simungalekerere khalidwe loipa.” (Hab. 1:13) Choncho uchimo unachititsa kuti anthu atalikirane kwambiri ndi Mulungu. Palibe aliyense amene angakhale pa ubwenzi ndi Yehova pokhapokha patachitika zinazake zothandiza kuti tikhale nayenso pa ubwenzi. Dipo ndi limene limachititsa kuti zimenezi zitheke.
15. Kodi dipo linathandiza bwanji kuti anthu akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova?
15 Baibulo limanena kuti Yesu ndi “nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yoh. 2:2) Ndiye kodi imfa ya Yesu inachititsa bwanji kuti zikhale zotheka kuti anthu akhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu? Sikuti imfayi inachititsa kuti Yehova azimvako bwino. Mmalomwake inamupatsa chifukwa chomveka chomuchititsa kuti akhalenso pa mtendere ndi anthu. (Aroma 3:23-26) Iye akanathanso kuona kuti anthu amene ankamulambira Yesu asanafe, anali olungama. (Gen. 15:1, 6) Zimenezi zikanatheka chifukwa choti iye ankayembekezera kuti nsembe ya dipo idzaperekedwa. Yehova sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Mwana wake Yesu adzapereka nsembeyi. (Yes. 46:10) Dipo linachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu azikhalanso pa ubwenzi ndi Mulungu.
16. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene mungaziganizire pamene mukukonzekera kudzapezeka pa Chikumbutso cha chaka chino? (Onaninso chithunzi.)
16 Taganizirani zinthu zabwino zimene mukusangalala nazo chifukwa chokhala pa ubwenzi ndi Yehova. Mwachitsanzo, mukhoza kumatchula Yehova kuti “Atate” wanu mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa. (Mat. 6:9) Nthawi zina mungamutchulenso kuti “Mnzanu.” Tikamatchula Yehova kuti “Atate” kapena “Mnzathu,” tizichita zimenezo mwaulemu kwambiri komanso modzichepetsa. Tikutero chifukwa chakuti anthu ochimwafe patokha sitingathe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Ndi nsembe ya dipo yokha imene imatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Kudzera mwa Yesu, Yehova anachititsa kuti zikhale zotheka kuti “agwirizanitsenso zinthu zina zonse ndi iyeyo. . . . Anachita zimenezi pokhazikitsa mtendere kudzera mʼmagazi amene Khristu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo.” (Akol. 1:19, 20) N’chifukwa chake panopa zimatheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngakhale kuti si ife angwiro.
Imfa ya Yesu yokha ndi imene imachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova (Onani ndime 16)
DIPO LIMATITSIMIKIZIRA KUTI YEHOVA NDI WACHIFUNDO
17. Kodi dipo limasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachifundo? (Aefeso 2:4, 5)
17 Dipo limatitsimikizira kuti Yehova ndi “wachifundo chochuluka.” Iye “anapangitsa kuti tikhale amoyo . . . ngakhale kuti tinali akufa.” (Werengani Aefeso 2:4, 5.) Anthu ‘amaganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha,’ amafunitsitsa kuthandizidwa chifukwa amazindikira kuti akwiririka mu uchimo umene tinatengera kwa makolo athu ndipo akufunika kupulumutsidwa. (Mac. 13:48) Yehova amathandiza anthuwa poonetsetsa kuti amva uthenga wa Ufumu kuti adziwe iyeyo komanso Mwana wake, Yesu. (Yoh. 17:3) Ngati Satana ankaganiza kuti kuchimwa kwa Adamu ndi Hava kuchititsa kuti cholinga cha Mulungu chilephereke, ankadzinamiza.
18. Kodi tizikumbukira nkhani iti tikamaganizira za dipo?
18 Tikamaganizira madalitso amene timapeza chifukwa cha dipo, tizikumbukiranso nkhani yofunika kwambiri. M’malo momangoona kuti dipo linaperekedwa kuti litithandize, tizikumbukira kuti ndi njira imene Yehova amagwiritsa ntchito poyankha bodza limene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni. (Gen. 3:1-5, 15) Pogwiritsa ntchito dipo, Yehova amayeretsa dzina lake posonyeza kuti zimene Satana ananena n’zabodza. Iye amatipulumutsanso ku uchimo ndi imfa posonyeza kuti ndi wachikondi. Ndipo chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu, anatipatsa mwayi woti tiyankhe nawo mabodza a Satana ngakhale kuti si ife angwiro. (Miy. 27:11) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso ya dipo? Nkhani yotsatira iyankha funsoli.
NYIMBO NA. 19 Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa kuti kapolo amasulidwe. Imfa ya Yesu ndi dipo chifukwa chakuti imamasula anthu omvera ku ukapolo wa uchimo ndi imfa.