ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri
POFIKA pa 31 August 2015, Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano linali litamasuliridwa lonse kapena mbali yake m’zinenero 129. Baibuloli likupezekanso pawebusaiti yathu ya jw.org m’zinenero zonse zimene lamasuliridwazi, kuphatizapo zinenero zamanja zokwana 7. Mwachitsanzo m’chaka cha utumiki cha 2015 chokha, Baibuloli linamasuliridwa m’zinenero zotsatirazi.