AspctStyle/stock.adobe.com
Yesu Adzathetsa Nkhondo
Ali padzikoli, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa anthu onse, moti anafika popereka moyo wake kuti awawombole. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posachedwapa, adzasonyeza umboni winanso wakuti amakonda anthu onse pogwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Iye ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.
Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza zimene Yesu adzachite:
“Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa.”—Salimo 72:12-14.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene atichitire posachedwapa?. Njira imodzi ndi kuphunzira zokhudza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene ankalalikira. (Luka 4:43) Werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”