panitan/stock.adobe.com
Yesu Adzathetsa Umphawi
Ali padzikoli, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa anthu, makamaka osauka komanso amene anali ndi nkhawa. (Mateyu 9:36) Iye anafika popereka moyo wake kuti athandize anthu. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posachedwapa, asonyezanso kuti amakonda kwambiri anthu pamene athetse umphawi padziko lonse pogwiritsa ntchito mphamvu komanso udindo wake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.
Baibulo limafotokoza mwandakatulo zimene Yesu adzachite, limati:
“Ateteze anthu onyozeka pakati pa anthu, apulumutse ana a anthu osauka.”—Salimo 72:4.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene atichitire posachedwapa? Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kuphunzira zambiri zokhudza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene iye ankalalikira. (Luka 4:43) Werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”