alfa27/stock.adobe.com
Yesu Adzathetsa Zoipa Zonse
Yesu amadziwa bwino mmene munthu amamvera akamavutika chifukwa cha uchigawenga ndi zinthu zopanda chilungamo. Iye anaimbidwa mlandu wabodza, anamenyedwa ngakhale kuti sanalakwe, anaweruzidwa mopanda chilungamo komanso anafa imfa yowawa kwambiri. Yesu anali wosalakwa koma mofunitsitsa anapereka “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.” (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, posachedwapa Yesu abweretsa chilungamo padziko lonse ndipo athetseratu zoipa zonse.—Yesaya 42:3.
Baibulo limafotokoza zimene zidzachitike padzikoli Yesu akadzayamba kulamulira:
“Oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene atichitire posachedwapa? Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kuphunzira zambiri zokhudza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene iye ankalalikira. (Luka 4:43) Werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”