Kodi Zochita za Mabungwe Pofuna Kulimbikitsa Mtendere Zingabweretsedi Mtendere Padzikoli?
M’madera ambiri padzikoli mukuchitika nkhondo komanso zachiwawa. N’chifukwa chake bungwe la United Nations komanso mabungwe ena akuyesetsa kuchita zinthu zokhazikitsa mtenderea zomwe zikuphatikizapo kutumiza anthu oimira mabungwewa kumalo amene kukuchitika zachiwawazo. Cholinga chawo ndi kukhazikitsa bata kumalo amenewa. António Guterres, yemwe ndi Mlembi Wamkulu wa bungwe la UN, ananena kuti: “Anthu okakhazikitsa mtendere omwe amatumizidwa ndi bungwe la United Nations ndi ofunika kwambiri pa cholinga chathu choti padzikoli pakhale mtendere.”
Pa zaka zingapo zapitazi, mabungwe okhazikitsa mtendere akwanitsa kuchita zinthu zina zofunika. Mwachitsanzo, kuteteza anthu wamba, kuthandiza anthu othawa kwawo kuti abwerere kumayiko awo, kupereka chithandizo ndi kumanganso nyumba komanso zinthu zina zimene zinawonongeka. Koma chifukwa cha mavuto ena akuluakulu, mabungwewa amalephera kuchita zonse zimene anthu amayembekezera. Ndiye kodi pangapezeke njira imene ingathandize kuti padzikoli pakhale mtendere weniweni? Kodi Baibulo limanena zotani?
Mavuto amene amakhalapo pofuna kukhazikitsa mtendere komanso zimene Baibulo limanena
Vuto limene limakhalapo: kusagwirizana. Nthawi zambiri zimakhala zovuta kuti asilikali a mayiko osiyanasiyana komanso mabungwe agwire ntchito limodzi mogwirizana. Nthawi zina zimenezi zimachitika chifukwa cha kusamvetsetsana ndiponso kusiyana zolinga.
Zimene Baibulo limanena: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu . . . nʼkuthetsa maufumu ena onsewa [maboma a anthu] ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
Posachedwapa, Mulungu athetsa nkhondo zonse n’kubweretsa mtendere padziko lonse. (Salimo 46:8, 9) Adzachotsa maboma onse padzikoli n’kukhazikitsa boma limodzi lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Chifukwa choti boma lakumwambali likamadzalamulira padziko padzakhala lamtendere, sipadzafunikanso mabungwe okhazikitsa mtendere.
Vuto limene limakhalapo: anthu amakhala kuti alibe zipangizo, luso komanso mphamvu zokwanira. Nthawi zina zimakhala zovuta kukhazikitsa mtendere chifukwa cha kuchepa kwa anthu ogwira ntchito, thandizo la ndalama kapena zinthu zina zofunika. Anthu omwe atumizidwa kukakhazikitsa mtendere amagwira ntchito m’madera ovuta kwambiri komanso oopsa.
Zimene Baibulo limanena: ‘Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu anamukhazika [Yesu] kudzanja lake lamanja mʼmalo akumwamba. Anamuika pamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, anthu amphamvu onse.’—Aefeso 1:17, 20, 21.
Mulungu Wamphamvuyonse Yehovab anapatsa Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wake, zinthu zonse zofunika. (Danieli 7:13, 14c) Mulungu anamupatsa mphamvu zochuluka, nzeru zozama ndiponso luso lodziwa ndi kumvetsa zinthu kuposa boma kapena bungwe lililonse la anthu. (Yesaya 11:2) Yesu alinso ndi gulu lankhondo la angelo amphamvu lomwe angaligwiritse ntchito. (Chivumbulutso 19:14) Iye akhoza kuchita chilichonse ndipo palibe chomwe chingamuvute.
Pogwiritsa ntchito mphamvu komanso zinthu zina zimene Mulungu wamupatsa, Yesu adzachita zambiri kuwonjezera pa kuthetsa nkhondo. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, iye adzathandiza anthu onse kuti azikhala mwabata, motetezeka komanso mwamtendere.—Yesaya 32:17, 18.
Vuto limene limakhalapo: malamulo a mayiko. Anthu amene amagwira ntchito yokhazikitsa mtendere nthawi zina amalephera kugwira bwino ntchitoyi chifukwa cha malamulo osamveka bwinobwino kapena amene amawaletsa kuchita zinthu zina. Malamulo oterewa akhoza kuwalepheretsa kugwira bwino ntchito yoteteza anthu kapena kukwaniritsa zonse zimene amafuna kuchita.
Zimene Baibulo limanena: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa [Yesu] kumwamba ndi padziko lapansi.”—Mateyu 28:18.
Yehova walamula Yesu kuti akhazikitse mtendere padziko lonse ndipo wamupatsa mphamvu zonse zochitira zimenezi. (Yohane 5:22) Yesu sangachite zinthu zopanda chilungamo kapena zachinyengo ngakhale pang’ono. (Yesaya 11:3-5) Mpake kuti Baibulo limamutchula kuti “Kalonga wa Mtendere,” amene maziko a Ufumu wake ndi “chilungamo ndiponso mtima wowongoka.”—Yesaya 9:6, 7.
Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere weniweni
Magulu a anthu osungitsa mtendere akhoza kukhazikitsa bata pa mlingo winawake komanso mwina kuthetsa nkhondo m’chigawo chinachake. Komabe iwo alibe mphamvu zothetsera chimene chimayambitsa zachiwawa, chomwe ndi chidani chochokera mumtima.
“Vuto lalikulu ndi loti n’zovuta kukhazikitsa mtendere chifukwa mtenderewo unasokonekera kalekale.”—Dennis Jett, kazembe wakale wa dziko la America.
Mosiyana ndi mabungwewa, Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse mtendere weniweni chifukwa wayamba kale kuthandiza anthu kuthetsa chidani chomwe amakhala nacho mumtima. Mwachitsanzo, kudzera mu zolankhula komanso zochita zake, Yesu ali padzikoli anaphunzitsa otsatira ake mmene angakhazikitsire mtendere komanso mmene angasonyezere chikondi kwa ena. Taonani mavesi otsatirawa:
Yesu ananenanso kuti anthu omwe ndi nzika za Ufumu wa Mulungu azidzadziwika ndi chikondi chimene amasonyezana. Baibulo limanena momveka bwino kuti anthu amene amadana ndi anthu anzawo sadzaloledwa kukhala mu Ufumu wa Mulungu. Limati:
Yehova Mulungu, amene analenga anthu onse, amadziwa njira yokhayo yemwe ndi yabwino kwambiri yobweretsera mtendere padzikoli. Ufumu wake udzabweretsa mtendere weniweni, zomwe mabungwe okhazikitsa mtendere alephera kuchita.
a Bungwe la United Nations ndi mabungwe ena amagwiritsanso ntchito mawu akuti “kukhazikitsa mtendere,” “kubweretsa mtendere,” “kulimbikitsa mtendere” komanso “ntchito zobweretsa mtendere.”
b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”
c Mawu akuti “mwana wa munthu” opezeka pa Danieli 7:13, 14, akunena za Yesu Khristu.—Mateyu 25:31; 26:63, 64.