NASA Photo
KHALANI MASO
Kodi Pali Boma Lodalirika Limene Lingalamulire Dzikoli?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Padzikoli, maboma akukumana ndi mavuto ambiri. Ngakhale mayiko amene akuoneka kuti ali ndi boma lokhazikika, maboma oterewa akuvutika ndi zinthu monga kuphwanya malamulo, kubera zisankho, mpungwepungwe pa ndale komanso anthu amachita zionetsero.
Baibulo limanena kuti pali boma limodzi lokha lomwe ndi lodalirika. N’kutheka kuti munamvapo za boma limeneli. Ndi limene Yesu Khristu analitchula mu pemphero la chitsanzo.
“Koma inu muzipemphera chonchi: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.’”—Mateyu 6:9, 10.
Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza Ufumuwu?
Ufumu wa Mulungu ndi boma lodalirika
Ufumuwu ukulamulira kuchokera kumwamba.
Yesu anatchula bomali kuti “Ufumu wakumwamba.” (Mateyu 4:17; 5:3, 10, 19, 20) Pa chifukwa chimenechi, iye ananena kuti Ufumu wake suli mbali ya dzikoli.—Yohane 18:36.
Ufumuwu udzalowa m’malo mwa maboma a anthu.
Baibulo limanena kuti: “Ufumu umenewu . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena [a anthu] onsewa ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
Ufumu wa Mulungu womwe Mfumu yake ndi Yesu Khristu, sudzawonongedwa.
Baibulo limanena kuti: “Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—Danieli 7:13, 14.
Ufumuwu udzabweretsa mtendere ndi chitetezo padzikoli.
Baibulo limanena kuti: “Aliyense adzakhala mwamtendere pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu, ndipo sipadzakhala wowaopseza.”—Mika 4:4, Good News Translation.
Phunzirani zambiri zokhudza Ufumu
Yesu ali padzikoli, ankathera nthawi yake yambiri “kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 9:35) Ananeneratunso kuti:
“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.
Masiku ano, uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa m’mayiko oposa 240. Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza boma limeneli komanso zimene mungachite kuti mupindule ndi ulamuliro wake.
Onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?