Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwfq nkhani 10
  • Kodi Ndani Anayambitsa Chipembedzo cha Mboni za Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Anayambitsa Chipembedzo cha Mboni za Yehova?
  • Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu Wakhazikitsidwa Kumwamba
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Apasitala Aŵiri Omwe Anayamikira Zimene Russell Analemba
    Nsanja ya Olonda—2002
  • ‘Ine Ndiimabe Pamwamba pa Nsanja’
    Nsanja ya Olonda—1987
  • ‘Mulungu, Tumizani Kuunika Kwanu’
    Nsanja ya Olonda—2000
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
ijwfq nkhani 10
Yesu akuphunzitsa ophunzira ake

Kodi Ndani Anayambitsa Chipembedzo cha Mboni za Yehova?

Gulu la masiku ano la Mboni za Yehova linayamba chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800. Pa nthawiyo, kagulu ka ophunzira Baibulo amene ankakhala pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh, ku Pennsylvania, m’dziko la United States, kanayamba kuphunzira ndiponso kukambirana mfundo za m’Baibulo mwakhama kwambiri. Iwo ankayerekezera zimene matchalitchi ankaphunzitsa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Kenako zimene ankaphunzirazo anayamba kuzifalitsa m’mabuku, manyuzipepala ndiponso m’magazini imene masiku ano imadziwika ndi dzina lakuti Nsanja ya Olonda—Yolengeza Ufumu wa Yehova.

Pagulu la anthu amene ankaphunzira Baibulo mwakhamawo panali munthu wina dzina lake Charles Taze Russell. Ngakhale kuti Russell ankatsogolera pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe inkachitika pa nthawiyo komanso anali mkonzi woyambirira wa Nsanja ya Olonda, iye si amene anayambitsa chipembedzo chatsopanocho. Cholinga cha Russell komanso anzakewo, omwe onse pa nthawiyo ankadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo, chinali kulimbikitsa mfundo zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso kutsanzira zimene mpingo wa Akhristu oyambirira unkachita. Popeza Yesu ndi amene anayambitsa Chikhristu, timaona kuti Yesuyo ndi amene anayambitsa gulu lathu.—Akolose 1:18-20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena