‘Ine Ndiimabe Pamwamba pa Nsanja’
“Ndipo iye anapfuulitsa ngati mkango, [Yehova, NW] inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi yausana, ndipo ndiikidwa mu ulondawanga usiku wonse.”—yesaya 21:8.
1, 2. (a) Kodi ndi chonulirapo chotani chimene Charles T. Russell anali nacho? (b) Kodi ndimotani mmene mabuku a Baibulo angathandizire kukwaniritsa chonulirapo chake?
MWAMUNA WOWOPA MULUNGU wa zaka 21 wokhala kumpoto cha kum’mawa kwa United States anali ndi ntchito yoti achite. Chinali chonulirapo chake kuwonetsa ziphunzitso za chipembedzo cha bodza cha mu tsiku lake, makamaka nthanthi za chizunzo chosatha ndi kuneneratu za mtsogolo. Ndiponso, iye anafuna kupititsa patsogolo chowonadi ponena za dipo ndi cholinga ndi mkhalidwe wa kudzanso kwa Kristu. Kodi ndimotani mmene iye akanachitira zinthu zonsezi? Mwakuwalitsa muni wa mawu a Mulungu, Baibulo loyera, pa zikhulupiriro za chipembedzo.—Masalmo 43:3; 119:105.
2 Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anali munthu ameneyo ndipo iye analingalira mu 1873 kufalitsa mabuku a chipembedzo monga njira ya kubweretsera kuwala kwa chowonadi cha Baibulo powonekera. Kwa owerenga ofunitsitsa, zofalitsidwa zimenezo zinavumbula ming’ankha mu zikhulupiriro za chipembedzo cha dziko. Chiphunzitso chiri chonse cholakwika chobisidwa sichikanapulumuka mphamvu yowunikira ya Baibulo. (Aefeso 5:13) Pa nthawi imodzimodziyo, bukhu limeneli lidzawunikira ‘chiphunzitso chopatsa moyo’ kumangilira chikhulupiriro cha awerengi. (Tito 1:9; 2:11; 2 Timoteo 1: 13) Kodi changu kaamba ka chowonadi cha Baibulo chomwe chinafulumiza Russell mu kufunsira kwake chinali ndi malo oyambirira?—Yerekezani ndi 2 Mafumu 19:31.
Akristu Oyambirira: Ngwazi za Mawu a Mulungu
3. Kodi ndimotani mmene Kristu Yesu anakhazikitsira njira kaamba ka kupititsa patsogolo chowonadi?
3 Akristu a mzana loyamba anapititsa patsogolo kugwiritsira ntchito kwa mawu a Mulungu pakati pa Ayuda ndi Akunja. Iwo anaima monga ngati aikidwa pa nsanja, kulengeza chowonadi kwa onse omwe angamve. (Mateyu 10:27) Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, anayamba njirayo. Iye anati: “Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi.” (Yohane 18:37) Ngakhale anali wangwiro, iye anakana kudalira pa nzeru ya iye mwini kapena malingaliro aumwini. Mmalo mwake, ziphunzitso zake zinachokera kwa Mphunzitsi wake Wapamwamba, Yehova Mulungu. “Sindichita kanthu kwa ine ndekha,” iye anauza gulu la Ayuda. “Koma monga anandiphunzitsa Atate ndilankhula izi.” (Yohane 8:28; onaninso Yohane 7:14-18. ) Malinga ndi mbiri ya uthenga wa utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anagwira mawu (kapena kulankhula malingaliro ofanana) kuchokera ku chifupifupi theka la mabuku a Malemba Achihebri.—Luka 4:18, 19 (Yesaya 61:1, 2); Luka 23:46 (Masalmo 31:5).
4. Perekani zitsanzo za mmene Yesu anagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kuphunzitsa chowonadi.
4 Ngakhale pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro, Yesu analikugwiritsirabe ntchito mawu a Mulungu kuphunzitsa chowonadi. Mwachitsanzo, pamene Kleopa ndi mnzake anali kuyenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Emau, Yesu anawathandiza ophunzira amenewo kulingalira mwa Malemba. Nkhaniyo imakamba kuti: “Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha.” (Luka 24: 25-27) Pambuyo pake tsiku lomwelo, Yesu anawonekera kwa atumwi 11 ndi ena a ophunzira ake kumangirira chikhulupiriro chawo. Motani? Mwakugwiritsira ntchito Malemba mwaluntha. Luka akulemba: “Ndipo iye [Yesu] anawatsegulira mitima yawo, kuti adziwitse malembo; ndipo anati kwa iwo, ‘Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu.’ Luka 24:45, 46.
5. Pa Pentekoste wa 33 C.E., ndimotani mmene Petro anatsanzira chitsanzo cha Kristu mkugwiritsira ntchito Malemba?
5 Kutsatira wopereka Chitsanzo wake, mu chaka cha 33 C.E. mpingo wa Chikristu unayamba ulaliki wake wapoyera mwakugwiritsira ntchito Malemba. Malo: gawo lotseguka kunja kwa nyumba mu Yerusalemu. Pambuyo pa kumva mawu onga “nkokomo wa mphepo yolimba” pa nyumba imeneyi, khamu la zikwi za Ayuda a mu Yerusalemu ndi Ayuda oyenda pa ulendo wachipembedzo akokedwera ku malo amenewa. Petro akupita kutsogolo—atumwi 11 ena akumamzungulira iye—ndipo ndi mawu amphamvu iye ayamba kulankhula: “Amuna inu Ayuda ndi inu nonse akukhala mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu ndipo tcherani khutu ku mawu anga.” Ndipo kenaka akumaloza kunja “chimene chinanenedwa mwa mneneri Yoweli” ndi chimene “Davide ananena,” Petro akulongosola chozizwitsa chomwe changochitika ndi kuti “Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.”—Machitidwe 2:2, 14, 16, 25, 36.
6. (a) Longosolani chomwe chinachitika pa msonkhano wa bungwe lolamulira la zana loyamba. (b) Ndimotani mmene mipingo inadziwitsidwira ponena za chigamulo cha bungwe lolamulira, ndipo ndi miapindu otani?
6 Pamene Akristu oyambirira anafuna mawu olongosola ponena za chikhulupiriro ndi khalidwe, bungwe lolamulira la zana loyamba linagwiritsira ntchito bwinonso Malemba. Mwachitsanzo, pa msonkhano wa bungwe lolamulira mu chaka cha 49 C.E., wophunzira Yakobo, akumaimira monga tcheyamani, analunjikitsa chidwi chawo pa lemba lozolowereka la Amosi 9:11, 12. “Amuna inu, abale inu, mverani ine,” iye anatero. “Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. Ndipo mawu a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa.” (Machitidwe 15:13-17) Bungwe lonse linavomerezana ndi lingaliro la Yakobo ndipo kenaka anaika chigamulo chawo chozikidwa pa malemba molembedwa kotero kuti chitumizidwe ku mipingo yonse ndi kuwerengedwa ndi iyo. Kodi nziti zomwe zinali zotulukapo zake? Akristuwo “anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake,” ndipo “mipingoyo inalimbikitsidwa mchikhulupiriro, nachuluka mchiwerengero chawo tsiku ndi tsiku.” (Machitidwe 15:22-31; 16:4, 5) Mwakutero, mpingo woyambirira wa Chikristu unakhala “nzati ndi nchirikizo wa chowonadi.” Koma bwanji ponena za mbiri yamakono? Kodi C. T. Russell ndi ophunzira anzake a Baibulo angatsanzire chitsanzo chabwino chimenechi, cha zana loyamba? Kodi ndimotani mmene iwo angapititsire patsogolo chowonadi?—1 Timoteo 3:15.
Magazini Okhala ndi Kayang’anidwe Kofika Kutali
7. (a) Kodi nchiyani chomwe chinali chifuno cha Zion’s Watch Tower? (b) Ndi kwa ndani kumene imayang’ana kaamba ka chirikizo?
7 July 1879 inawona kubadwa kwa njira yeni yeni ya kuwalitsa Baibulo kwa Russell—Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence. Kope lake loyambirira linandandalitsa zifuno zolemekezeka za magaziniyo: “Monga mmene dzina lake likusonyezera, iyo ikulinga pa kuyang’ana kuchokera kumene zinthu zosangalatsa ndi zopindulitsa zingalengezedwere ku ‘kagulu ka nkhosa,’ ndipo monga Herald of Christ’s Presence,’ kupereka ‘nyama mu nthawi yake’ kwa ‘mbumba yachikhulupiriro.’” kukhulupirirani mwa Mulungu wamphamvuyonse inali ngodya ya maziko ya magaziniyo. Kope lake lachiwiri linalongosola: “‘Zion’s Watch Tower’ iri, tikukhulupirira, ndi YEHOVA monga mchiriki zi wake, ndipo pamene izo ziri choncho iyo si dzapempha kapena kupembedzera anthu kaamba ka chirikizo. Pamene iye amene anena: ‘Golide yense ndi siliva wa mmapiri ndi zanga,’ alephera kupereka ndalama zoyenerera, tidzamvetsetsa kuti iri nthaŵi ya kuleka kusindikiza chofalitsidwacho.”
8. Longosolani kukula kwa Nsanja ya Olonda mkuwunikira Yesaya 60:22 ndi Zekariya 4:10.
8 Zion’s Watch Tower, tsopano Nsanja ya Olo-nda, yakhala ikufalitsidwa mosalekeza kwa zaka zoposa 107. Iyo yakula kuchoka ku magazini yakamodzi pamwezi ya makope 6, 000 osindikizidwa mu chinenero chimodzi kufika ku magazini ya kaŵiri pa mwezi ya makope 12, 315, 000 yopezeka mu zinenero 103.—Yerekezani ndi Yesaya60:22; Zekariya 4:10.
9. Ndimotani mmene mutu wakuti Nsanja ya Olonda unaliri woyenerera?
9 Mutu wakuti, Nsanja ya Olonda, unali chosankha cha mwamsanga cha Russell. Liwu logwiritsidwa ntchito kaŵikaŵiri mu Malemba Achihebri kaamba ka “Nsanja” limatanthauza “kuyang’ana” kapena “malo oyang’anira,” kuchokera pa amene mlonda mosavuta angawone mdani pamene akubwera kuchokera kutali ndipo ndi kufuula chenjezo la mwamsanga ponena za kufika kwa tsoka. Moyenerera, ndiyeno, kwa zaka zake zoyambirira 59 za kufalitsidwa, mutu wa pa tsamba loyambirira unatenga kugwidwa mawu kwa chitokoso kuchokera pa Yesaya 21: 11, 12, King James Version: “Mlonda, Nthawi Yanji ya Usiku?” “Kukali Kucha.”
10. Kodi ndani amene akutumikira monga mlonda wa Yesaya 21:11, ndipo kodi ndi uthenga wotani umene iye akulengeza?
10 Mlonda wokhazikitsidwa wa mu ulosi wa Yesaya—anayenera kupita kutsogolo posachedwapa. Pakati pa mkhalidwe wopambana woipa wa mdima wa dziko lerolino, Russell mwachimwemwe analengeza za mbiri yabwino ya “kucha” komwe kuli kudza. Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu kwa mtendere kuli mutu wa mbiri yosangalatsa. Koma “kucha” kusanafike, gulu lotumikira monga mlonda—otsalira a Israyeli wauzimu lerolino—molimba mtima limachenjeza ponena za kufika kwa “mdima,” umene udzafika pa nsonga ya kuda kwambiri mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Har-Magedo.—Chivumbulutso 16:14-16.
11, 12. (a) Kodi ndimotani mmene mawu a pa Yesaya 21:8 amasonyezera kuti gulu la mlonda liri lokhulupirika ndipo la maso? (b) Kodi ndi kudzera mwa mthenga uti mmene ripoti linabwerera, ndipo kodi ndimotani mmene ilo mokulira limabukitsidwira?
11 Poyambirira, mu Yesaya 21:8, ife tadziwikitsidwa kwa mlonda wokhulupirika ameneyundi mawu awa: “Ndipo iye anapfuulitsa ngatimkango, [Yehova, NW] inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipb ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;”
12 Dzilingalireni inu mwini m’maganizo anu monga mlonda mutaima pamwamba pa nsanja, mutaweramira kutsogolo mukumawona malekezero a dziko mkati mwa tsiku, ndi kuyesayesa kuwona kupyola mu mdima, mkati mwa usiku—nthawi zonse muli wamaso. Tsopano muli ndi lingaliro lenileni lomwe likuperekedwa ndi liwu la Chihebri kaamba ka liwu lakuti “nsanja” (mitspeh/) monga lagwiritsidwa ntchito mu Yesaya 21:8. Popeza mlonda ali wamphamvu kotero, ndi ndani amene mumaganizo ake olondola angakaikire ponena za ripoti lake? Mofananamo lerolino, gulu la mlonda ladzikanikiza ilo leni mkufufuzafufuza mu Malemba kuti awone nchiyani chimene Yehova ali nacho kaamba ka dongosolo iri la zinthu. (Yakobo 1:25) Mlonda ameneyu kenaka akupfuula uthengawo mokwezeka ndipo mopanda mantha, kwenikweni kudzera mu masamba a Nsanja ya Olonda (Yerekezani ndi Amosi 3:4, 8. ) Magazini imeneyi sidzakhwinyata mu mantha kuchokera ku kupititsa patsogolo chowonadi!—Yesaya 43:9, 10.
13. Kodi ndi magazini yofanana iti imene inawoneka mu 1919, ndipo kodi ndi cholinga chofanana chotani iyo inali nayo?
13 Pa October 1, 1919, magazini yatsopano inawoneka pa dziko: The Golden Age.aGulu la mlonda lingagwiritsire ntchito chida chimenechi monga chinzake cha Nsanja ya Olonda. Ngakhale kuti nkhani zake sizingalowerere mu mitu ya Baibulo mozama monga izo za mu Nsanja ya Olonda, idzakhalitsa maso mtundu wa anthu ku ziphunzitso zonyenga za chipembedzo, chiwonongeko chikudzacho cha dongosolo iri la zinthu loipa, ndi dziko latsopano la chilungamo lomwe lidzatsatira. Inde, iyonso idzapititsa patsogolo chowonadi!
14. Kodi nchiyani chimene chinali chonulirapo cha Consolation, ndipo pambuyo pake Galamukani!?
14 Zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu pambuyo pake dzina la The Golden Age linasinthidwira ku Consolation. “Dzina latsopanolo limaimira chowonadi,” linatero kope la October 6, 1937. Consolation inakhala Galamukani! mu kope la August 22, 1946. Mu kope limenelo inalonjeza: “Umphumphu ku chowonadi chidzakhala chonulirapo chapamwamba cha magaziniyi.” Kufikira tsiku lino, iyo siinalephere kusunga lonjezo limenelo. Mwapadera, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zanyamula mbendera za Chowonadi paimwamba kaamba ka onse kuti awone. Mkuchita tero, magaziniwa amatsatira njira yoyambitsidwa ndi mpingo woyambirira wa Chikristu.—3 Yohane 3, 4, 8.
Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!: Ngwazi za Chowonadi
15. (a) Kodi ndi njira yotani ya kugawirira chakudya chauzimu lerolino imene iri yofanana ndi ija ya mpingo woyambirira wa Chikristu? (b) Pa mbali pa kugwira mawu maversi mu Baibulo, kodi nchiyani chinanso chimene chimafunikira? Perekani zitsanzo.
15 Gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” “mlonda,” lerolino limagwiritsira ntchito magazini a Nsanja ya Olonda pansi pa chitsogozo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova monga njira yake yeniyeni yakugawirira“chakudya cha uzimu pa nthawi yake.” (Mate-yu 24:45) Ichi chimatsatira njira ya mpingo wazana loyamba, womwe umaika chidziwitso cholongosoledwa bwino cha ziphunzitso ndi makhalidwe molembedwa “kaamba kakuti awerengedwe kwa abale onse.” (1 Atesalonika 5:27)Kuyambira pa chiyambi chake Nsanja ya Olo-nda yakhala magazini yogwiritsira ntchito Baibulo ndi kuphunzitsa Baibulo. Mwachitsanzo, kope yoyambirira ya Zion’s Watch Tower inkagwira mawu kapena kolozera ku Malemba oposa 200 kuchokera ku chifupifupi mabuku 30 aBaibulo. Koma zowonjezereka zimafunikira. kuposa ndi kungogwira mawu maversi a Baibulo. Anthu amafunikira kuthandizidwa kuti awamvetsetse iwo. Nsanja ya Olonda nthawi zonse yapititsa patsogolo kumvetsetsa kwa Baibulo. Kuyambira mu 1892 mpaka 1927 kope iriyonse inali ndi kuwerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu ndi kukambitsirana kwa lemba la chitsogozo kuchokera ku kuwerenga kuli konse. Kaamba ka zitsanzo zina, onani charti yokhala ndi mutu wakuti: “Nkhani za mu Nsanja ya Olonda, Zopanga Mbiri Zaka Khumi ndi Khumi.
16, 17. Kodi nchiyani chimene mlembi woyambirira wa Nsanja ya Olonda anachita kutsimikizira kuti magazini iyi nthawi zonse idzapititsa patsogolo chowonadi cha Baibulo?
16 Kodi ndimotani mmene Nsanja ya Olonda idzasungirira kuyera kwake kwa uthenga wakewosindikizidwa? Mlembi woyambirira wa magaziniyo, C. T. Russell, anakhazikitsa alonda otsimikizira kuti chomwe chinasindikizidwamu Nsanja ya Olonda chinali chowonadi chomwe chinamvedwa pa nthawiyo. Mmodzi wa alonda amenewo anazindikiritsidwa mu chikhumbo chake chomwe chinapangidwa pa June 27, 1907. (Russell anafa pa October 31, 1916. ) Chikhumbo chake chinanena kuti:
“Ndikutsogoza kuti chitsogozo cha kulemba konse kwa ZlON’S Watch Tower chiyenera kukhala mmanja mwa komiti ya abale asanu, omwe ndikuwachenjeza kuchisamaliro chokulira ndi chikhulupiriro ku chowonadi. Nkhani zonse zowoneka mu danga la Zion’S Watch Tower zidzakhala ndi chivomerezo chosayeneretsedwa cha chifupifupi atatu a asanu a mkomitiwo, ndipo ndikuchenjezani kuti ngati nkhani ina yomwe yavomerezedwa ndi atatuwo idziwika kapena kulingaliridwa kukhala yosiyana ndi kawonedwe ka mmodzi kapena onse awiri aziwalo zina za komiti, nkhani zoterozo ziyenera kuikidwa pambali kaamba ka kulingalira kowonjezereka, pemphero ndi kukambitsirana kwa miyezi itatu isanafalitsidwe—chotero monga mmene kungathekere umodzi wa chikhulupiriro ndi chomangila cha mtendere ziyenera kusungidwa mkatsogozedwe ka kulemba kwa magaziniyi.”
17 Chiwalo chiri chonse cha Komiti Yolemba, malinga ndi chikhumbo cha Russell, chinayenera kukhala “chomvera ku ziphunzitso za Malemba” ndipo chinayenera kusonyeza, monga zochitika zowonekera, “kuyera kwa moyo, omvekera mchowonadi, changu kaamba ka Mulungu, chikondi kaamba ka abale ndi kukhulupirika kwa Mpulumutsi.” Ndiponso, Russell anakhazikitsa kuti: “Sichiyenera mnjira iriyonse kusonyezedwa kuti nkhani zosiyanasiyanazo zopezeka mu magaziniwo zinalembedwa ndi ndani. . . kotero kuti chowonadi chidzazindikiridwe ndikuyamikiridwa kaamba ka chiyenerero cha icho chokha, ndi kuti Ambuye moyenerera ayenera kuzindikiridwa monga mutu wa eklesia ndi Mtsinje wa chowonadi.”
18. Nchifukwa ninji tingawerenge Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi chikhulupiriro?
18 Kufikira nthawi ino Bungwe Lolamulira limatsatira zitsogozo zofananazo. Nkhani iri yonse mu magazini onse awiri a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi tsamba liri lonse, kuphatikizapo ntchito ya manja, imayang’anitsitsidwa ndi chiwalo chosankhidwa cha Bungwe Lolamulira lisanasindikizidwe. Kuwonjezerapo, awo amene amathandiza mkulemba nkhani kaamba ka Nsanja ya Olonda, ali akulu Achikristu omwe amayamikira kufunika kwa thayo lawo. (Yerekezani ndi 2 Mbiri 19:7. ) Iwo amawononga maora ambiri mkufufuza mu Baibulo ndi zolozera zina kutsimikizira kuti zomwe zalembedwa ziri zowonadi ndi kuti mokhulupirika ziri kutsatira Malemba. (Mlaliki 12:9, 10; 2 Timoteo 1:13) Sichiri chosayembekezereka kaamba ka nkhani imodzi ya magazini—yomwe mungawerenge mu mphindi 15—kutenga kuchokera ku milungu iwiri mpaka kuposa mwezi umodzi kuikonzekera.
19. Kodi nchiyani chimene mungachite kuti mupititse patsogolo chowonadi cha Baibulo?
19 Chotero, mungawerenge Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi chitsimikiziro. Koma mungachite zowonjezereka. Inu motenthedwa maganizo mungagawire magazini amenewo kwa ena kotero kuti nawonso aphunzire chowonadi ndi kupindula kuchokera mu kumva uthenga wa ‘mlonda woima pa nsanja.’ (Yesaya 21:8) Inde, limodzi ndi mlonda wa mu tsiku lathu, nanunso mungapititse patsogolo chowonadi cha Baibulo.
Mawu a M’munsi
a Mosangalatsa, aŵerengi ena poyambirira anakhumudwitsidwa ndi kapangidwe ka chikuto cha kunja cha The Golden Age. Kwa iwo chinawoneka kukhala chofala kwambiri. Mkuyankha ripoti la pachaka la Watch Tower Society linanena kuti: “Mchigwirizano ichi ife tingalingalire kuti pa nthawi imene chofalitsidwa cha The Golden Age chinayamba panali kukana kugwira ntchito kwa osindikiza mu Greater New York. Masiku ochepa okha lisanafike tsikulo, kontrakiti inapangidwa kaamba ka The Golden Age ndipo amuna omwe anali kuyendetsa makina osindikizira omwe amatenga mtundu wa pepala ndi chikuto chomwe chinagwiritsidwa ntchito mu iyo sanakane kugwira ntchito. Icho mwakutero chinawoneka kukhala chanzeru kuti kawonekedwe ka chikuto ndi pepala kanakhala katasankhidwa, kaamba ka chifukwa chakuti mtundu wina wake ukanasankhidwa chikanakhala chosatheka kuyambitsa magaziniyo nkomwe. Chotero Ambuye anawoneka kukhala atasonyeza chiyanjo kaamba ka chofalitsidwa cha ukhanda chimenechi.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa ninji C. T. Russell ; anayamba kufalitsa mabuku a Baibulo?
◻ Kodi ndimotani mmene Akristu oyambirira anapititsira patsogolo chowonadi?
◻ Kodi ndi chifukwa ninji liwu lakuti“Nsanja ya Olonda” iri mutu wa magaziniyi?
◻ Kodi ndi ndani amene ali mlonda, wamakono ndipo kodi ndi chida chotani chimene iye kwenikweni akugwiritsira ntchito kukulitsira mawu ake?
◻ Kodi ndimotani mmene Nsanja ya Olonda ndi Galamukani imapititsira’ patsogolo chowonadi cha Baibulo?
[Tchati patsamba 20]
Nkhani za mu Nsanja ya Olonda Zopanga Mbiri, Zaka Khumi ndi Khumi
1879: “Mulungu ndi Chikondi”—inapititsa patsogolo nsembe ya dipo ya Yesu monga maziko kaamba ka chipulumutso cha mtundu wa anthu
1879: “Nchifukwa ninji Kuipa Kunaloledwa”—inalongosola nchifukwa ninji kufika kwa Yesu Kristu kudzakhala kosawoneka
1880: “Thupi Limodzi, Mzimu Umodzi, Chiyembekezo Chimodzi”—inaloza mwachindunji 1914 kaamba ka kutha kwa nthawi za amitundu
1882: “Mphoto ya Uchimo Ndi Imfa“—Inavumbuiutsa chiphunzjtso cha chizunzo chosatha monga kukana kwa chikondi cha Mulungu
1885: ”Chisinthiko ndi Mbadwo wa Bongo“—inavumbulutsa nthanthi ya chisinthiko kukhala yabodza
1897: “Nchiani Chimene Malemba Amanena Ponena za Mizimu?“—inapereka chitsimikiziro cha magwero auchiwanda amizimu
1902: “Mulungu Choyamba—Makhazikitsidwe Ake”-inagogomezera kumvera lamulo la Mulungu mbanja ndi mkachitidwe ka bizinesi
1919: “Odala Ali Opanda Mantha”—Inabweretsa moyo watsopano ku gulu lomagalamuka la olamblra opanda mantha
1925: “Kubadwa kwa Mtundu”—inamveketsa bwino maulosi kusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unabadwamu 1914
1931: “Dzina Latsopano”—kuyambira tsopano dzina lakuti Mboni za Yehova Ildzapatula Akristu owona kuchokera ku chipembedzo cha dziko chopanduka
1935: “Khamu Lalikulu”—inasonyeza kuti kusonkhanitsa kwa awo omwe adzakhala kosatha pa dziko lapansi kunali mkati
1938: “Gulu“—inadziwitsa kakonzedwe ka teokratiki pakati pa Mboni za Yehova
1939: “Uchete”—inalimbikitsa Mboni za Yehova kuzungullra pa dziko lonse lapansi kupirira ndi zitsenderezo za Nkhondo ya Dziko ya II
1942: “Kuwala Kokha”—inapfuula chizindikiro cha “pitani patsogolo” kaamba kakuti ntchito yoQmba mtima ya umboni ipitirire
1945: “Osagwedezeka Kaamba ka Kulambira Koona”—inasonyeza kuti Akristu ayenera kusala kulandira mwazi
1952: “Kusunga Gulu Kukhala Loyera”—inasonyeza kuti kuchotsedwa ndi mipingo kulikwa Malemba
1962: “Kugonjera ku Maulamuliro Aakulu’—Nchifukwa it Ninji?”—Inapereka zifukwa kaamba ka kugonjera ku mphamvu za anthu
1973: “Kusunga Mpingo wa Mulungu Woyera mu ‘Nthawi ya Chiweruzo Chake’“—inafulumiza kupewa kugwiritsira ntchito fodya
1979: “Changu Kaamba ka Nyumba ya Yehova”—inabwereza kuti kulalikira kwa ku nyumba ndi nyumba kumatsanzlra chitsanzo cha atumwi
1982: “Okondedwa, . . . Dzisungeni Inu Eni Mchikondi cha Mulungu’-inadziwitsa Akristu ponena za njira za ampatuko
1983: “Kuyenda ndi Mulungu mu Dziko Laupandu”—inatsimikizira kuti Akristu sayenera kukhala ndi mbali mu upandu
1984: “Khola latsopano kaamba ka ‘nkhosa zina’“—inamveketsa ndimotani mmene gulu iri lapadziko lapansi limagwirizanira ndi awo a ‘khola’ la chipangano chatsopano
1987: “Chaka Choliza Upenga cha Akristu Chifika pa Chimake mu Zaka Chikwi—inasonyeza ndimotani mmene Akristu onse amene ali omvera amapezera ufulu ndi moyo