Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 3/1 tsamba 22-27
  • ‘Kumayenda Mnjira ya Chowonadi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kumayenda Mnjira ya Chowonadi’
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kubukitsa Nyimbo ya Chowonadi
  • ‘Kumayenda Kaamba ka Chowonadi’
  • Kodi Munawayesa Malingaliro Awa?
  • Kuyamba Njira ya Magazini?
  • ‘Khalanibe Osefukira ndi Chinthu Chokoma’
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 3/1 tsamba 22-27

‘Kumayenda Mnjira ya Chowonadi’

“Ndipo mu ukulu wanu yendani kuchipambano; yendani mnjira ya chowonadi ndi chifatso ndi chilungamo, ndipo dzanja lanu lamanja lidzakuphunzitsani zinthu Zoopsa.”​—MASALMO 45:4, NW.

1, 2. (a) Kodi ndi uthenga wotani umene unasangalatsa wamasalmo? (b) Kodi nchifukwa ninji uthenga wofananawo uyenera kusefukira mwa ife?

WOYIMBA ndakatuloyo anali wofunitsitsa kuyamba nyimbo yake. Chiyembekezo cha kubwera kwa boma labwino mmanja mwa wolamulira wolungama, wosasakazika chinali champhamvu kwambiri. Iye sakanatha kukhala chete. Sanali wokhozanso kudzisunga iye mwini, wamasalmo anabangula ndi mawu awa: “Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndikunena: ‘Ntchito zanga ziri zonena zamfumu.’ Lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.” (Masalmo 45:1) Woyimba ndakatulo woyambirira anafa kale. Koma nyimbo yake yaulosi idakali ndi moyo, ndipo mphamvu ya iyo siinali yamphamvu koposa monga mmene iriri tsopano.​—Yerekezani ndi Akolose 3:16.

2 Kodi nchiyani chomwe chatsimikizira kukhala “chinthu chokoma” chomwe china sefukira mu mtima wa wamasalmo? Icho chikulinganizidwa ndi mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu! Chotero “wokoma” uli uthenga wa Ufumu womwe ukafunikira “kulalikidwa ku dziko lonse” lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse chisanafike “chimaliziro”cha mitundu imeneyi. (Mateyu 24:14) Lerolino, kodi “chinthu chokoma” cha mutu wa Ufumu wa Umesiya wa Mulungu chasefukira mu mtima mwanu? Chiyenera kutero. Nchifukwa ninji? Chifukwa verebu la Chihebri lotembenuzidwa “wasefukira” (ra-chash’) limasonyeza kachitidwe kochititsidwa nthumazi, monga kubwadamuka, madzi owira. Verebulo limagwirizanitsa kotheratu. Ndipo kumbukirani, Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, anati: “M’kamwa mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima.” (Luka 6:45) Mwakutero, kodi inu, monga wamasalmo, muli ndi mtima wosefukira ndi “chinthu chokoma”? Ngati nditero, ndiye kuti .palibe chiri chonse chingakuletseni inu kuyimba chowonadi chapamwamba ichi: Yesu Kristu akulamulira mu Ufumu wa Mulungu!

Kubukitsa Nyimbo ya Chowonadi

3. Kodi ndi njira ziwiri zenizeni ziti zimene zimagwiritsidwa ntchito mkubukitsa mbiri yabwino yaUfumu lero lino?

3 Kodi ndimotani mmene nyimbo yaufumu imeneyi ingabukitsidwire? Mwanjira ya mzimu woyera, lirime la wamasalmo linakhala ngati “peni” mdzanja mwa Yehova. (Yerekezerani ndi 2 SamueU 23:2. ) Nyimbo zake zolembedwa zinaimbidwa kaamba ka olambira onse akale a Yehova kuti azimve. Ife lerolino tingapititse patsogolo chowonadi cha Ufumu wa Mulungu mu njira ziwiri zofananazo. Choyamba, mwakumvedwa kwa mawu athu mkulalikira mu mabwalo ndipo, yachiwiri, mwamawu athu kuwerengedwa mu mabuku athu. Mwakutero, pamene tigawira mabuku ozikidwa pa Baibulo, tikufotokoza zimene lilime la amuna owuziridwa ndi mzimu linanena kale. (2 Timoteo 3:16; 2 Petro 1:20, 21) Ndipo lerolino uthenga wa Ufumu wosindikizidwa ukugawiridwa mu ziwerengero ndi zinenero ndi paliwiro loposa chiyerekezo cha wamasalmo. Kodi inu mukukhala ndi mbali yokhazikika mkubukitsidwa kwake, makamaka mwakugawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!?

4. (a) Kodi ndimotani mmene Kristu wakhalila “wokongola koposa ana a anthu”? (b) Kodi ndimotani mmene gulu la mlonda wodzozedwa akutsanzirira ‘chisomo cha milomo ya Kristu’?

4 Kuwonekera kwa Mfumu ya Yehova kumatsitsimula wamasalmo kulemba: “Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu. Anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu. Chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.” (Masalmo 45:2) Kuyambira pa tsiku lakudzozedwa kwake ndi mzimu wa Mulungu, milonio ya Yesu mosalekeza inalalikira za Ufumu, kufikira athenga aumunthu a Satana kwa kanthawi anawaletsa iwo. Chifukwa cha kumvera kwa Yesu, Yehova kenaka anamudalitsa iye kosatha mwakumuukitsa iye kuchokera kwa akufa ndi kumkweza iye pamwamba pa zolengedwa zonse. (Afilipi 2:8-11) Kuyambira pa ulemerero wakumwamba wa Yesu, pamene iye anakhala ‘chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe cha Mulungu,’ iye ali wokongola koposa wolamulira wokwezeka koposa, waumunthu kapena mngelo. (Ahebri 1:3, 4) Tsopano, monga Mfuinu yokhazikitsidwa, Yesu amapatsa inphamvu milomo ya mlonda wodzozedwa ndi oyanjana nawo anzawo kuimba mopanda mantha mbiri yabwino ya Ufumu. Komabe, iyi irinso nyimbo ya nkhondo.

5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene ‘kuyenda mnjira ya chowonadi’ kwa Kristu kumasonyeza? (b) Kodi ndimotani mmene gulu la mlonda limagwiritsira ntchito Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!?

5 Wamasalmo kenaka akufula kwa Mfumu yolamulira: “Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Ndipo mu ukulu wanu yendani ku chipambano; yendani mnjira ya chowonadi ndi chifatso ndi chilungamo, ndipo dzanja lanu lamanja lidzakuphunzitsani zinthu zoopsa.” (Masalmo 45:3, 4, NW) Kuyambira 1914 Kristu wakhala akukwera pa kavalo wankhondo, wokonzekera kaamba ka kachitidwe. (Chivumbulutso 6:1, 2) Iye wavala lupanga—chizindikiro cha nkhondo ndiponso ulamuliro ndi mphamvu kuchokera kwa Mulungu kupha mitundu yotsutsa. Kristu anamenyana kale ndi Satana ndi ziwanda zake, kuwagwetsera iwo pansi kuchokera kumwamba ndi kuwatsekera iwo kunsi kwa dziko. —Chivumbulutso 12:1-13.

6 Komabe, mtendere usanabwezeretsedwe, zinthu zoopsa kwambiri kuposa izi zidzabweretsedwa ndi dzanja lamanja la Mfumu pamene iye ‘adzayenda mnjira ya chowonadi’ pa Armagedo kuwononga adani onse a Mulungu pa dziko lapansi. (Masalmo 45:4; Chivumbulutso 16:14, 16; 19:17, 18) Kristu walimbikitsa gulu la mlonda wodzozedwa kuimba chenjezo limenelinso. Kodi nchiyani chimene mlonda akugwiritsira ntchito kukulitsa liwu lake? Kwakukulukulu masamba a magazini a Nsanja ya Olonda—magazini yomwe iri yowonekera m’kulengeza Ufumu wokhazikitsidwa wa Yehova. Gulu la mlonda, monga khamu la dzombe loluma ngati chinkhanira, ladzazidwa ndimzimu wofananawo womwe umafulumiza Kristu “kuyenda mnjira ya chowonadi.” (Chivumbulutso 9:7-11) Mokhutiritsa, iwo akugwiritsira ntchito magazini okonzedwa pansi pa chitsogozo cha “mlonda​—Nsanja ya Olonda ndiGalamukani!​—“mnjira ya chowonadi.”​—Mateyu 24:45; yerekezani ndi Chivumbulutso 9:16-19.

‘Kumayenda Kaamba ka Chowonadi’

7. Kodi ndi mnjira yochititsa mantha yotani mmene magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! imapititsira patsogolo chowonadi cha Baibulo?

7 Kwa zaka zoposa zana limodzi, Nsanja yaOlonda yakhala ikupambana ‘njira ya chowonadi cha Ufumu.’ Iyo mwaluso imagwiritsira ntchito mawu a Mulungu monga lupanga mkukalula mitika ya zolakwika zomwe zakuta kuzungulira ziphunzitso za chipembedzo chonyenga. (Yerekezani Aefeso 6:17; Ahebri 4:12. )Magazini ya Galamukani! nayonso imachirikiza njira ya chowonadi. Pamene ibwera ku zochitika zaposachedwa, Galamukani! imacheka chikuto chonyenga chomwe chimakuta nthanthi za sayansi zomwe zimanyoza Baibulo ndi mayanjano oopsa ndi makhalidwe oipa. Kodi nchiyani chomwe tingachite kuti tigawire magazini amenewa mmanja mwa anthu ambiri kotero kuti iwonso amve uthenga wa Ufumu wopulumutsa moyo?

8, 9. Kodi ndimotani mmene kugwiritsira ntchito prinsipulo lopezeka pa Aefeso 5:16 ku kuwerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kungakuthandizireni inu “kukhala osefukira” kutenga mbali mu umboni wa magazini? Perekani zitsanzo

8 Onse amene amakonda chowonadi ayenera “kusefukira” ndi uthenga womwe magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amakhala nawo. (Masalmo 45:1) Motani? Bwanji osaŵerenga iwo mwamsanga pamene mwawalandira? ‘Sindiwerenga magazini akudziko kapena bukhu liri lonse kufikira choyamba nditawerenga magazini athu,’ Lillian anatero kwa iye mwini zaka khumi zapitazo. lye adakali wokhulupirika ku chimango chimenecho. (Mateyu 6:33) Kodi nchiyani chimene mungachite mutatha kuwawerenga iwo? Lankhulani ponena za zomwe ziri mkatimo ndi ena​—banja ndi ziwalo zina za mpingo. Ichi chidzakufulumizaninso kukhala ndi changu kaamba ka kuchitira umboni ndi magazini kotero kuti mungauze anansi anu ponena za zinthu zabwino zomwe mwawerenga. Mosakaikira inu mudzafuna kugawana mu umboni wa magazini mlungu uli wonse, kuwatenga iwo ku makomo a anansi anu. Ichi chingayerekezedwe ndi njira imene mtumwi Paulo “anachitira umboni.”​—Machitidwe 20:20, 21.

9 Peter ndi mkazi wake Petra akhala akutumikira monga amishonale mu dziko la Africa kwa zaka zinayi zapita. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ali magwero awo eni-eni a chakudya chauzimu. “Nsanja ya Olonda imatithandiza ife kukhalabe amaso mwauzimu mu gawo lathu,” akutero Petra. “Timatenga chilimbikitso ndi mphamvu kuchokera ku kope iriyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!” Peter akuwonjezera, “ndipo nthawi iriyonse pamene magazini afika, chimawoneka kwa ife monga tikulandira kalata kuchokera kumudzi.” (Yerekezani ndi Masalmo 46:1. ) Kodi muli ndi chiyamikiro chozama chofananacho kaamba ka magazini athu ndipo kodi muli ofunitsitsa kuwaŵerenga iwo monga mmene aliri Peter ndi Petra? Mzimu umenewo udzakufulumizani inu kugawira magaziniwo mokhazikika kwa enanso.

10. Kodi ndi kawonedwe ka mtundu wanji kamene kakufunikira kaamba ka umboni wa magazini wokhutiritsa, ndipo ndi mapindu otani amene ichi chingatulutse?

10 Ofalitsa a Ufumu ayenera kukhala ndi kaimidwe koyenera kulinga ku umboni wa magazini. Anthu omwe ali moyenerera achipembedzo amalandirabe chidziwitso chozikidwa pa Baibulo chomwe chimapezeka mmagazini athu. (Yerekezani ndi Machitidwe 10:15, 30-33) Chifukwa ninji? Chifukwa iwo sangapeze icho kuchokera kumagwero ena ali wonse. Zoposa zaka 45 zapitazo mu Sweden, Lars anapeza mpukutu wa magazini a Nsanja ya Olonda kuchokera kwa wolembedwa ntchito. “Ichi chimapanga lingaliro,” iye anauza mkazi wake pambuyo pa kuwawerenga iwo. “Zimene Baibulo limanena, Nsanja ya Olonda imanena.” Zimene Lars anawerenga zinamufulumiza iye kufika ku ubatizo —March 1940. Lingalirani chitsanzo china. Aminisitala awiri achipainiya kuchokera kummwera kwa United States ananena kuti:

“Mayi wina anafikiridwa mu ntchito ya magazini. Iye ali msungi chuma wa tchalitchi chachikulu cha Baptist ndipo ali wophunzira Baibulo wosamalitsa kwambiri. Pamene iye anawerenga tsatanetsane wa mitu ya Armagedo mu makope a Nsanja ya Olonda a July 1 ndi July 15, 1985, iye anasangalatsidwa. Iye anali atawononga maora ambiri kufufuza mutu umenewo ndipo sanapeze china chiri chonse kupatulapo kokha lemba lopezeka pa Chivumbulutso 16:16. Iye anali atafunsa minisitala wake: ‘Kodi Armagedo nchiyani? Kodi mungalongosole iyo?’ Iye anayang’ana kwa iye ndi kunena kuti ‘Limenelo liri phunziro lozama,’ ndipo kenaka anachokapo. Iye anapereka ndemanga kuti Nsanja ya Olonda, ku mbali ina, inayankha funso lake liri lonse ndipo kuti iyo inali magwero okha amene iye anapeza kaamba ka malemba ofunikira pa mutu wa Armagedo.”

11. (a) Nchifukwa ninji tiyenera kuchita ndandanda ya umboni wa magazini, ndipo kawirikawiri motani? (b) Kodi utumiki wa magazini ungakhale wothandizo mu ntchito ya phunziro la Baibulo? Longosolani. (c) Kodi ndimotani mmene mungakhozere kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!? Onani bokosi

11 Kodi mungandandalitse chifupifupi tsiku limodzi kaamba ka umboni wa magazini mlungu uli wonse, kupanga iyo kukhala mbali yanu yauzimu ya tsiku ndi tsiku? (Yerekezani ndi Afilipi 3:16.) “Ofalitsa, ndi apainiya nawonso, sawononga nthawi yokwanira mu ntchito ya magazini,” inawona motero nthambi ya Watch Tower Society mu Nigeria. Koma kodi umboni wamagazini uyenera kuphimba ntchito yopanga ophunzira? Mosiyanitsa, maripoti ochokera ku nthambi za Sosaite za Australia ndi Brazil zimasonyeza kuti kugawira magazini ingakhale sitepi yoyambirira mkuyambitsa maphunziro ambiri a Baibulo. “Kuyambira pa kugawira kwanga koyambirira kwa magazini, maphunziro atatu anakhazikitsidwa,” anatero mlongo wa Chiaustralia. Kodi ndimotani mmene mungathere kugawira magazini omwe angatsogolere ku phunziro la Baibulo? Yang’anani mu bokosi lokhala ndi mutu wakuti “kugawira Magazini” kaamba ka malingaliro.

Kodi Munawayesa Malingaliro Awa?

12. Kodi ndi malingaliro otani amene anatsimikizira kukhala othandiza kwa wofalitsa m’modzi?

12 Utumiki Wathu Wa Ufumu wa May 1984 unali ndi mphatika ya masamba 4 pa kuchitira umboni ndi magazini. Kodi munayamba mwawayesa malingaliro omwe anaperekedwa? Ofalitsa a Ufumu angachite bwino kuwerenganso kachiwiri mphatikayo ndi kugwiritsira ntchito langizo lake mu utumiki wa mmunda. Mlongo mmodzi wochokera ku United States anachita chimenecho; zotulukapo zake mosangalatsa zinamudabwitsa iye. Iye akulemba:

“Ndakhala ndikugwiritsira ntchito nsonga zomwe zinandandalitsidwa mu mphatika ya Utumiki Wathu Wa Ufumu wa May 1984 ponena za kugawira magazini, ndipo chikugwira ntchito! Kumapeto kwa 1983 ndinali nditagawira magazini 36 chaka chonse chathunthu! Ndinali wopanda chimwemwe, osati chifukwa cha kuchepa kwa ripoti, koma chifukwa ndinalephera kupereka chidziwitso chopatsa moyo chimenechi mmanja mwa anthu omwe anachifuna icho. Ndinapemphera kwa Yehova ponena za nkhaniyo ndipo ndinatsimikizira kupanga kuyesayesa kokulira kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndinagwiritsira ntchito malingaliro onena za kuika chonulirapo chaumwini pa zogawira, kugwiritsira ntchito kagawiridwe kachidule komwe kamaunikira magazini imodzi yokha, mokhazikika kupita mu utumiki wa mmunda pa tsiku la magazini, ndi kukhala ndi khalidwe la kawonedwe koyenerera. Tsopano pamene mwini nyumba akana chogawira cha nthawiyo, ndimanena kuti: ‘Chabwino, mnjira imeneyo ndidzangosiya kope yatsopano ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pa chopereka cha 40 cents.’ Nsonga zimenezi zimagwiradi ntchito. Mu miyezi inayi yapitayi, Ndakhala wokhoza kufikira avereji ya magazini 14 pa mwezi!”

13. Kodi ndi langizo lotani limene linafalitsidwa mu 1888 lomwe likugwirabe ntchito lero lino?

13 Mu kope la December 1888 la Zion’s Watch Tower, pansi pa mutu wakuti “Lingaliro kwa Otuta,” langizo iri linaperekedwa: “Vuto lalikulu kwambiri kumbali ya ambiri limawoneka kukhala kuti, mitima yawo iri yodzadza kwambiri ndi mafunde abwino, kuti ali ofuna kuuza zowonjezerekapo ponena za kakonzedwe ka Mulungu.” Kodi langizo limenelo likugwirabe ntchito? Pamene anafunsidwa nchiyani chimene ofalitsa angachite kuti awonjezere kugawira kwawo magazini, woyang’anira wadera mmodzi wochokera ku France anayankha: “Khalani wachidule. Fikani pa nsonga.”

14, 15. Kodi ndimotani mmene zithunzithunzi za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zingagwiritsidwire ntchito mu umboni? Perekani zitsanzo

14 Mu zinenero zambiri mmene magaziniwo amawoneka, zisonyezero zokongola mu mitundu inayi zawonjezera ku kufunika kwa uthenga wa Ufumu pamene ukufikira anthu amitundu yosiyanasiyana mu zinenero zambiri mu zimene magaziniyo ikuwoneka. Kuyambira ndi kope la January 8, 1987, Galamukani! inagwirizana ndi Nsanja ya Olonda mkusindikizidwa mu mitundu inayi mu zinenero zazikulu zambiri. Kodi mwagwiritsira ntchito zisonyezero ndi zithunzithunzi mu magazini monga nsonga zokambitsirana? Ambiri atero, ndi zotulukapo zabwino. Theresa, mmishonale wa ku Far East kuyambira 1976, watero. Iye amagawira magazini 260 pa mwezi. “Ndimagwiritsira ntchito zithunzi kuunikira nsonga yeniyeni ya chogawira changa,” iye akutero. “Nthawi zambiri ndimangowonetsa chikuto kwa mwini nyumba ndi kutchula mutu wa nkhani, ndipo magaziniyo imadzigawira yokha.”

15 Kay, mmishonale mu dziko la Suriname, anakhala ndi chokumana nacho chofananacho. Iye limodzi ndi mwamuna wake akhala ali kumeneko kwa zaka khumi, ndipo amazipeza zithunzithunzi kukhala zokhutiritsa pamene akuchitira umboni, makamaka kwa awo achikhulupiriro cha Chihindu. Nchifukwa ninji? Kay akulongosola:

““Chipembedzo cha Chihindu chiri chipembedzo cha zithunzithunzi. Pa khomo limodzi, ndinafunsa mkazi: ‘Chonde ndiuzeni inu dzina la milungu yanu kuchokera pa zithunzithunzi zanu.’

“‘“Uyu ndi Shiva,’ iye anayankha.

“‘Tsopano, kodi ndi uti amene ali mulungu wapamwamba?’ Ndinamfunsa kenako. Sanayankhe.‘Kodi tingawerenge Yeremiya 10:10-12? Kodi ndi Mulungu uti amene angadzinenere kukhala Mlengi? Yehova yekha. Timadziwa kuti mumakonda zithunzithunzi. Kodi zithunzithunzi izi za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! siziri zokongola ndipo zosangalatsa? Kodi simungakonde chimwemwe cha kuphunzira zimene izo zimatanthauza?’”

Bwanji osayesa kugwiritsira ntchito zithunzithunzi mkukambitsirana kwanu nthawi ina pamene muli mu ntchito ya magazini?

16. Kodi ndi malingaliro otani ochokera kwa wofalitsa wa ku Hong Kong amene mungawapeze kukhala athandizo?

16“Pamene anali kutumikira mu Hong Kong, Gene anafikira avereji ya kugawira magazini oposa 300 pa mwezi. Kodi ndimotani mmene iye anachitira icho? Iye akulongosola:

“Choyamba, pempherani kwa Yehova kaamba ka dalitso pa umboni wanu wa magazini. Chachiwiri, khalani oyenerera, mwetulirani, ndipo aubwenzi. Chachitatu, khalani wokhoza kusintha ndipo wogwirizanika, ndi kuyang’ana kaamba ka mayambidwe ofanana ndi mwini nyumba. Chachinayi, itanitsani magazini okwanira kaamba ka mwezi wonse. Ndiri ndi orda yaikulu popeza ichi chimandipatsa ine chifulumizo chowonjezereka. Chachisanu, ikani pambali madzulo amodzi mkati mwa mlungu kaamba ka utumiki wa magazini, popeza anthu owonjezereka amapezeka kunyumba nthawiyo ndipo ali opuma bwino. Chachisanu ndi chimodzi, yambani njira ya magazini, ngakhale kuti iri yaing’ono.”

Kuyamba Njira ya Magazini?

17. (a) Ndi kumbali iti ya umboni wathu wa magazini kumene prinsipulo la pa Machitidwe 15:36 lingagwiritsidwire ntchito? (b) M’maiko amene ali ndi mautumiki akulandira makalata osakhazikika, kodi ndi njira imodzi iti imene wofalitsa angagwiritsire ntchito kugawira magazini?

17 “Kusunga zolembera zabwino za kumene magazini anagawiridwa ndipo kenaka kubwereramo mokhazikika iri njira imodzi yakuwonjezera kugawira kwanu magazini,” akutero Ollie, yemwe anatumikira mu dziko la mu Africa la Burkina Faso. “Ndinakhala ndi anthu 15 pa njira yanga ya magazini. Popeza Burkina Faso siiri nthambi yosindikiza ndipo kayendedwe ka makalata kali kosatsimikizirika, Mbonizo kawirikawiri zimalandira magazini awo kaamba ka kugawira mu mipukutu, mwina mwake makope anayi kapena asanu pa nthawi imodzi.” Kodi chimenecho chiri chowona ponena za dziko lanunso? Ngati nditero, kodi nchiyani chimene chingapangidwe kuti mulake chitokoso chimenechi cha kugawira magazini? “Mungagwire makope a kope iriyonse m’manja mwanu ndi kuwakupiza magazini ndi kuitana wokondwererayo kuti asankhe ndi iti imene angakonde kuwerenga,” akulingalira motero Ollie. “Kawirikawiri, iye adzatenga onse.”

‘Khalanibe Osefukira ndi Chinthu Chokoma’

18. Ndi mbali ziti za maripoti a utumiki wa m’munda aposachedwapa zimene ziri mwapadera zoyamikiridwa, ndipo ndi kumbali iti kumene tiyenera kupereka chisamaliro chokulira?

18 Inu ofalitsa a Ufumu mwathandiza chiwerengero cha masabuskripishoni opezedwa a magazini onse awiri kuti chikwere mosangalatsa. Muyenera kuyamikiridwa kaamba ka changu chanu mkufalitsa mbiri yabwino mnjira imeneyi. Koyamikirikanso kuli kukwera kwachionkhetso cha chiwerengero cha magaziniogawiridwa. Mwina mwake, ngakhale kulitero, tingapereke chisamaliro chowonjezereka ku kugawira kwathu kwa magazini kwa umwini. Ndi kukwaniritsidwa kokulira kwa gawo, kugawira kwa magazini kwa wofalitsa aliyense kumatsika. Popeza tiri kukhala mkati mwa nthawi yamapeto, kodi tingakhale ‘osefukira kwambiri ndi chinthu chokoma’ cha Ufumu mwanjira ya umboni wa magazini?​—Masalmo 45:1; 1 Petro 4:7.

19. Ndi mnjira ziwiri ziti zimene tingapititsire patsogolo chowonadi cha Ufumu?

19 Kristu mu ukulu wa Ufumu akuyenda ku chipambano mkuyeretsa dzina loyera la Atate wake ndi kulemekeza ulamuliro Wake wa chilengedwe chonse. (Chivumbulutso 6:2) Tiyeni ife tigwiritsire ntchito malirime athu ndi masamba osindikizidwa kulengeza za kufika kwake. Tiyeni tonse momvera tikweze mawu athu limodzi ndi gulu lodzozedwa la mlonda pamene ligwirizana ndi Kristu mkupititsa patsogolo chowonadi cha Ufumu wokhazikitsidwa wa Umesiya wa Mulungu. Inde, tiyeni ife mofala tigawire Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!​—magazini omwe amadzaza mbali yofunika kwambiri pamene Mfumu yathu ‘ikuyenda mnjira ya chowonadi.’​—Masalmo 45:4.​—

Kodi Mumakumbukira?

◻ Kodi ndi “chinthu chokoma” chiti chimene chiyenera kusefukira mu mtima mwanu?

◻ ‘Kuyenda mnjira ya chowonadi’ kwa Kristu kumabweretsa zotulukapo zotani?

◻ Kodi ndi mwanjira yotani mmene Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimatumikirira “mu njira ya chowonadi”?

◻ Kodi ndimotani mmene tingaperekere chisamaliro chowonjezereka ku umboni wa magazini?

[Bokisi/​Chithunzi patsamba 25

KUGAWIRA MAGAZINI

Kodi Munayamba Mwayesa?—

◆ Umboni wa ku khomo ndi khomo

◆ Umboni wa mkhwalala

◆ Umboni wa ku malo a malonda

◆ Umboni wa njira ya magazini

◆ Umboni wa madzulo

◆ Pamene chogawira cha bukhu chakanidwa

◆ Pamene mupanga maulendo obwereza

◆ Pamene mufika kwa maphunziro a Baibulo akale

◆ Pamene mukuyenda kapena kugula zinthu

◆ Pamene mukulankhula kwa anansi, ogwiranawo ntchito, anzanu, anzanu a pa sukulu, kapena aphunzitsi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena