Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 3
  • Ndikulephera Kuti Ndisiye Kuonerera Zinthu Zolaula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndikulephera Kuti Ndisiye Kuonerera Zinthu Zolaula
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene mungachite
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuona Zithunzi Zolaula?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Kuona Zithunzi Zolaula?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuonerera Zolaula?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 3
Mnyamata akuonerera zolaula pa Intaneti

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kuonerera Zinthu Zolaula?

Zimene mungachite

Zindikirani cholinga cha zinthu zolaula. Zinthu zolaula ndi njira imene Satana akugwiritsa ntchito pofuna kunyoza zinthu zimene Yehova analenga kuti zikhale zolemekezeka. Mukamvetsa kuti cholinga cha zithunzi zolaula n’chimenechi mungathe kuyamba ‘kudana n’choipa.’—Salimo 97:10.

Ganizirani zotsatira zake. Zithunzi zolaula zimachotsera ulemu anthu amene ajambulidwawo komanso munthu amene akuzionayo. N’chifukwa chaketu Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.”—Miyambo 22:3.

Tsimikizani mtima. Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anenana kuti: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Nanunso mungathe kutsimikiza mtima kuchita zotsatirazi:

  • Sindidzagwiritsa ntchito Intaneti ndili pamalo a ndekha.

  • Ngati chithunzi cholaula chitatulukira mwadzidzidzi, ndizichitseka nthawi yomweyo.

  • Ngati nditayambiranso khalidweli, ndiziuza munthu wina wachikulire amene ndimagwirizana naye.

Manja akodwa ndi ulusi

Mukamakonda kuonerera zolaula, mumavutikanso kwambiri kuti musiye khalidweli

Pemphererani za nkhaniyi. Wamasalimo anapemphera kwa Yehova Mulungu kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” (Salimo 119:37) Mulungu amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino, ndipo ngati mutapemphera iye akhoza kukupatsani mphamvu yokuthandizani kuti muchita zoyenera—Afilipi 4:13.

Uzaniko munthu wina. Nthawi zambiri, kuuza nkhaniyi munthu amene mumamudalira kumathandiza kwambiri kuti musiye khalidweli.—Miyambo 17:17.

Muzikumbukira mfundo iyi: Nthawi iliyonse mukapewa kuona zinthu zolaula, ndiye kuti mukupambana pa nkhondoyi. Nthawi iliyonse mukakwanitsa kupewa kuonerera zolaula, muzimuuza Yehova, ndiponso muzimuthokoza chifukwa chokupatsani mphamvu zimene zakuthandizani kupewa zimenezo. Mukapewa kuonerera zinthu zolaula, mumasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena