Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 15
  • Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso amene angakuthandizeni
  • ‘N’chifukwa chiyani sindisangalala ndi mmene ndimaonekera?’
  • ‘Kodi ndisinthe mmene ndimaonekera?’
  • Malangizo amene angakuthandizeni
  • Kodi Ndiyeneradi Kudandaula Ndi Mmene Ndimaonekera?
    Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Kodi Ndingatani Ngati Sindikusangalala ndi Mmene Ndikuonekera?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 15

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

  • Mafunso amene angakuthandizeni

  • N’chifukwa chiyani sindisangalala ndi mmene ndimaonekera?

  • Kodi Ndisinthe Mmene Ndimaonekera?

  • Malangizo amene angakuthandizeni

  • Zimene Julia ananena

Mafunso amene angakuthandizeni

  1. Kodi ndi chiganizo chiti chimene chikugwirizana ndi mmene mumadzionera?

    • Sindimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

    • Nthawi zina ndimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

    • Nthawi zonse ndimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

  2. Kodi n’chiyani chimene mungafunitsitse mutasintha pa thupi lanu?

    • Kutalika

    • Kunenepa

    • Mmene thupi lanu linaumbidwira

    • Tsitsi

    • Kaonekedwe ka khungu

    • Kukula kwa masozi

    • Zina

  3. Malizitsani kulemba chiganizo chotsatirachi.

    Sindimasangalala ndi mmene ndimaonekera . . .

    • Ndikakwera pasikelo.

    • Ndikayang’ana pagalasi.

    • Ndikadziyerekezera ndi anthu ena (anzanga, anthu oonetsedwa pamafashoni, anthu a m’mafilimu).

  4. Malizitsani kulemba chiganizo chotsatirachi.

    Ndimakwera pasikelo . . .

    • Tsiku lililonse.

    • Mlungu uliwonse.

    • Pakapita nthawi.

  5. Kodi ndi mawu ati amene akugwirizana ndi mmene mumamvera?

    • Sindisangalala ndi mmene ndimaonekera. (Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Serena ananena kuti: “Nthawi iliyonse ndikadziyang’anira pagalasi, ndimaona kuti ndine chimunthu chonenepa kwambiri komanso chosaoneka bwino. Moti nthawi zina ndimadzizunza ndi njala kuti ndichepeko thupi.”)

    • Sindikhumudwa ndi mmene ndimaonekera. (Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Natanya ananena kuti: “N’zoona kuti pamakhala zinthu zina zokhudza maonekedwe athu zimene sizitisangalatsa koma timangofunika kuvomereza kuti ndi mmene tinabadwira. Kungakhale kupanda nzeru kumadandaula ndi zinthu zimene sitingathe kuzisintha.”)

Baibulo limatiuza kuti tisamadziganizire kuposa ‘mmene tiyenera kudziganizira.’ (Aroma 12:3) N’zoona kuti sikulakwa ndipo ndi zofunika kumaganizira mmene timaonekera. N’chifukwa chake timachita zinthu zodzisamalira monga kutsuka m’kamwa komanso kukhala aukhondo.

Komabe sibwino kumaganizira monyanyira za maonekedwe athu.Komano kodi mungatani ngati nthawi zambiri simusangalala ndi mmene mumaonekera? Mwina munadzifunsapo funso lakuti. . .

‘N’chifukwa chiyani sindisangalala ndi mmene ndimaonekera?’

Pakhoza kukhala zifukwa zambiri. Zina mwa zifukwazo zikhoza kukhala:

  • Mauthenga a pa TV ndi malo ena. “Mauthenga ambiri a pa TV kapena pa zipangizo zina amasonyeza kuti wachinyamata ayenera kukhala wochepa thupi kwambiri komanso nthawi zonse azioneka wokopa. Ndiye ukakhala kuti ndiwe wonenepa komanso suoneka mokopa zimapangitsa kuti usamasangalale ndi mmene umaonekera.”—Kellie.

  • Makolo. “Ndinaona kuti ngati mayi amangokhalira kuganizira za maonekedwe awo ananso amachita chimodzimodzi. Izi zimachitikanso ngati bambo amangokhalira kuganizira za maonekedwe awo. Nawonso ana aamuna amachita chimodzimodzi.”—Rita.

  • Kudzikayikira. “Anthu amene amangokhalira kuganizira mmene amaonekera amafuna kuti nthawi zonse anthu aziwauza kuti akuoneka bwino kapena atchena. Zimakhala zotopetsa kukhala ndi anthu otere.”—Jeanne.

Mosasamala kanthu za chifukwa chimene chimapangitsa kuti musamasangalale ndi mmene mumaonekera, mwina mukhoza kumadzifunsabe kuti . . .

‘Kodi ndisinthe mmene ndimaonekera?’

Taonani zimene achinyamata anzanu ananena.

“Sungathe kusintha zinthu zonse zimene sizikusangalatsa zokhudza mmene umaonekera. Choncho ndi bwino kungovomereza kuti ndi mmene unabadwira. Ndipo ukavomereza mmene umaonekera, anthunso amangokuona mmene ulili basi.”—Rori.

“Ndi bwino kuchita zonse zimene ungathe kuti ukhale ndi thanzi labwino. Ukakhala ndi thanzi labwino umaoneka mmene unafunikira kuonekera. Ndipo ngati munthu wina sangamasangalale ndi khalidwe lako labwino koma kumafuna kuti uzioneka mmene iyeyo akufunira, ameneyo si mnzako wabwino.”—Olivia.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Muzichita zonse zimene mungathe kuti muzioneka bwino. Koma musamadandaule ndi zinthu zimene simungathe kuzisintha. Kudera nkhawa kwambiri ndi mmene mumaonekera kungakubweretsereni mavuto aakulu. (Onani mutu wakuti “Zimene Julia Ananena.”)

Kuganizira moyenerera mmene mumaonekera kungakuthandizeni kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Erin. Iye ananena kuti: “N’zoona kuti pali zinthu zina zokhudza mmene ndimaonekera zimene sindisangalala nazo. Koma ndikuona kuti ndimakhumudwa kwambiri ndikamaganizira kwambiri zinthu zimene sizindisangalatsa. Panopa ndimaonetsetsa kuti ndikuchita masewera olimbitsa thupi nthawi ndi nthawi komanso ndikudya moyenerera. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndizisangalala ndi mmene ndimaonekera.”

Malangizo amene angakuthandizeni

Mukamaganizira moyenera mmene mumaonekera mumasangalala komanso mumaoneka bwino. Baibulo lingakuthandizeni pa nkhani imeneyi ndipo likukulimbikitsani kuchita zinthu zotsatirazi:

  • Kukhala wokhutira. “Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima. Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 6:9.

  • Kuchita masewera olimbitsa thupi moyenera. “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono.”—1 Timoteyo 4:8.

  • Kukhala ndi Khalidwe labwino. “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.

“Mmene nkhope yathu imaonekera zimasonyeza mmene timamvera muntima. Ngati munthu amasangalala ndi mmene amaonekera, anthu ena amazindikira zimenezo ndipo amasangalala kucheza naye.”—Sarah.

“N’zoona kuti anthu akhoza kutengeka nawe mwansanga chifukwa cha maonekedwe ako. Koma anthu amakukumbukira kwambiri chifukwa cha umunthu wako komanso khalidwe lako labwino.”—Phylicia.

Onaninso Miyambo 11:22; Akolose 3:10, 12; 1 Petulo 3:3, 4.

Zimene Julia Ananena

Ndili ndi zaka 16, ndinkaona kuti ndine wonenepa ndipo ndinkadandaula kwambiri. Sikuti ndinali wonenepa kwambiri komanso sindinabadwe wochepa thupi kwambiri. Kungoti ndinali ndi mahipi aakulu. Ndinkaganiza kuti mwina ndikanakhalako wochepa thupi pang’ono anyamata bwenzi akundifuna. Ndiye ndinayamba kudzikhaulitsa ndi njala kuti ndikhale wochepa thupi.

Ndinakwanitsa kuchepa thupi koma zimenezi zinandipangitsa kuti ndiyambe kudwala. N’zoona kuti ndinachira koma ndimadandaulabe ndikakumbukira ndipo mpaka pano ndimavutika kudya zakudya zina. Panopa ndinavomereza mmene ndimaonekera ndipo ndimadya moyenerera komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. Komabe ndimati ndikakhumudwa ndi chinachake, zimene zimandibwerera mwachangu m’mutu mwanga ndi kudzikhaulitsa ndi njala basi.

Ndikanakhala ndi mwayi wolangiza achinyamata anzanga, ndikanawauza kuti azikumbukira kuti aliyense amaona zinthu mosiyana ndi mnzake. Mulimonse mmene mungamaonekere, pamakhalabe anthu ena amene amaona kuti mumaoneka bwino pomwe ena amaona kuti simuoneka bwino. Muzingoonetsetsa kuti muli ndi thanzi labwino basi. Ndipo anthu amene amakufunirani zabwino amasangalala akaona kuti muli ndi thanzi labwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena