Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 56
  • Kodi Mdyerekezi Angalamulire Zochita za Anthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mdyerekezi Angalamulire Zochita za Anthu?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Pali Mizimu Yoipa?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Mumakhulupirira Kuti Mdyerekezi Alikodi?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 56

Kodi Mdyerekezi Angalamulire Zochita za Anthu?

Yankho la m’Baibulo

Zimene Mdyerekezi ndiponso ziwanda zimachita zimakhudza kwambiri zochita za anthu moti Baibulo limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Baibulo limatiuza njira zimene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu.

  • Chinyengo. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti ‘azilimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.’ (Aefeso 6:11) Imodzi mwa njira zake zachinyengo ndi yakuti amapusitsa anthu kuti aziona ngati atumiki ake ndi atumiki a Mulungu.—2 Akorinto 11:13-15.

  • Kukhulupirira mizimu. Mdyerekezi amasocheretsa anthu pogwiritsa ntchito anthu olankhula ndi mizimu, olosera za m’tsogolo ndiponso anthu ochita zamatsenga kapena okhulupirira nyenyezi. (Deuteronomo 18:10-12) Zinthu zinanso zimene zimachititsa kuti munthu akodwe mumsampha wa ziwanda n’kugwiritsa ntchito mankhwala ogwirizana ndi mizimu, kugonekedwa tulo m’matsenga ndiponso kusinkhasinkha kogwirizana ndi mizimu.—Luka 11:24-26.

  • Chipembedzo chonyenga. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa anthu zinthu zabodza zimachititsa kuti anthuwo asamamvere Mulungu. (1 Akorinto 10:20) Baibulo limanena kuti zinthu zabodza zimene chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa ndi “ziphunzitso za ziwanda.”—1 Timoteyo 4:1.

  • Kugwidwa ndi ziwanda. M’Baibulo muli nkhani zosonyeza kuti mizimu yoipa imalamulira anthu ena. Nthawi zina ziwandazo zinkachititsa khungu anthuwo kapena kuwachititsa kuti asamalankhule, ngakhalenso kuwavulaza kumene.—Mateyu 12:22; Maliko 5:2-5.

Zimene mungachite kuti Mdyerekezi asamakulamulireni

Musachite mantha kuti mwina ziwanda zingayambe kukulamulirani chifukwa Baibulo limasonyeza kuti mungathe kukana zoti Mdyerekezi azikulamulirani.

  • Muzitha kuzindikira ndi kudziwa bwino ziwembu za Mdyerekezi n’cholinga choti asakukoleni.—2 Akorinto 2:11.

  • Muziphunzira mfundo za m’Baibulo n’kumazigwiritsa ntchito. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti musakodwe ndi misampha ya Mdyerekezi.—Aefeso 6:11-18.

  • Mutaye kapena kuwotcha chinthu chilichonse chimene chikugwirizana ndi ziwanda. (Machitidwe 19:19) Zinthu zimenezi zingakhale nyimbo, mabuku, magazini, zithunzi ndiponso mavidiyo amene amalimbikitsa zamizimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena