Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwwd nkhani 13
  • Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo
  • Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Nkhani Yofanana
  • Tetezani Khungu Lanu
    Galamukani!—2005
  • Khungu la Njoka
    Galamukani!—2014
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2005
  • Kusunga Misozi M’nsupa
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Kodi Zinangochitika Zokha?
ijwwd nkhani 13
Chipatso cha pomelo chikulendewera mumtengo.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo

Pomelo ndi chipatso cha m’gulu la zipatso zowawasa koma chimatsekemera. Chipatsochi chimakhala chachikulu ndipo ngakhale chitagwa mumtengo pamtunda woposa mamita 10 kuchokera pamwamba kufika pansi, sichimaphulika. Kodi n’chiyani chimene chimathandiza kuti chipatsochi chisaphulike chikagwa pansi?

Taganizirani izi: Akatswiri ofufuza apeza kuti mkati mwa khoko la chipatso cha pomelo, momwe mtundu wake ndi woyera, muli maselo ooneka ngati siponji komanso timipata. Timipata tamaselowa timakula pang’onopang’ono tikamalowerera mkati kwambiri ndipo timadzaza ndi mpweya kapena timadzi. Chipatsochi chikagwa pansi, khoko lake limalimba kwambiri ndipo timadziti timathandiza kuti chisaphulike.

Chipatso cha pomelo chadulidwa pakati ndipo mkati mwa khoko lake mukuoneka ngati siponji. Chithunzi chomwe chakulitsidwa chikusonyeza maselo komanso timipata tamkati mwake.

Asayansi akuyeserera kupanga zipangizo za zitsulo zomwe sizingaphwanyike zikagwa pansi potengera khoko la chipatso cha pomelo. Iwo akukhulupilira kuti akhoza kutengera luso limeneli popanga zipewa za njinga yamoto, zipangizo zotetezera galimoto ikachita ngozi komanso kuteteza zipangizo zawo zakuthambo kuti zisamaonongeke zikagundana ndi miyala yamumlengalenga.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khoko la pomelo lisamaphulike likagwa pansi? Kapena pali winawake amene analilenga?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena