26 Bedi lililonse limene angagonepo pa nthawi imene akukha magaziwo,+ lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi imene akusamba. Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa ngati mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi imene akusamba.