26 Bedi lililonse limene angagonepo pa tsiku lililonse mwa masiku amene akukha magaziwo, lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi ya kusamba kwake.+ Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi ya kusamba kwake.