13 Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo,+ ndinapatula mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli kuti akhale wanga, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”