8 Koma ngati munthu amene walakwiridwayo wamwalira ndipo alibe wachibale wapafupi amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aziperekedwa kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Munthu amene wachimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo amuphimbire machimo ake.+