8 Koma ngati wolakwiridwayo wamwalira wopanda wachibale wake weniweni, amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aperekedwe kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Wochimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo am’phimbire machimo ake.+