18 Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova nʼkumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ nʼkuiika mʼmanja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga mʼdzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+