18 Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova n’kumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ n’kuiika m’manja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga m’dzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+