17 Koma usawombole ngʼombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi ake uziwawaza paguwa lansembe,+ ndipo mafuta ake uziwawotcha pamoto kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa kwa Yehova.+