19 Muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova, yomwe ndi nsembe yowotcha pamoto. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazo nʼzopanda chilema.+