13 Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe 13 zazingʼono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+