36 Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+