13 Iye adzakukondani, kukudalitsani komanso kukuchulukitsani. Adzakudalitsani ndithu pokupatsani ana ambiri,+ adzadalitsa zokolola za nthaka yanu, mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu,+ ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu, mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.+