8 Ngati mu umodzi mwa mizinda yanu muli mlandu wovuta kwambiri kuweruza kaya ndi mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma, mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano, muzinyamuka nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+