29 Mudzapapasapapasa masana ngati mmene munthu wavuto losaona amapapasira mumdima,+ ndipo chilichonse chimene mudzachite sichidzakuyenderani bwino. Nthawi zonse anthu azidzakuberani mwachinyengo komanso kukulandani zinthu zanu popanda wokupulumutsani.+