6 Ine ndidzathamangitsa pamaso pa Aisiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu+ komanso Asidoni+ onse. Iweyo ungopereka maderawa kwa Aisiraeli+ kuti akhale cholowa chawo mogwirizana ndi zimene ndinakulamula.+