19 Gidiyoni ndi amuna 100 amene anali naye anafika kumalire a msasa ulonda wapakati pa usiku ukungoyamba kumene. Pa nthawiyi nʼkuti atangosintha kumene alonda ena apamsasa. Ndiyeno analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ nʼkuphwanya mitsuko yaikulu imene inali mʼmanja mwawo.+