19 Iwo anamuyankha kuti: “Khala chete. Tseka pakamwa pako, ndipo upite nafe kuti ukakhale mlangizi ndi wansembe wathu. Chabwino nʼchiyani, kuti ukhale wansembe mʼnyumba ya munthu mmodzi,+ ndi kuti ukakhale wansembe wa banja ndi fuko lonse mu Isiraeli?”+