8 Choncho anaitanitsa olamulira onse a Afilisiti nʼkuwafunsa kuti: “Tipange bwanji ndi Likasa la Mulungu wa Isiraeli?” Iwo anayankha kuti: “Likasa limeneli, la Mulungu wa Isiraeli, tilitumize ku Gati.”+ Choncho Likasa la Mulungu wa Isiraeli analipititsa kumeneko.