11 Kenako anaitanitsa olamulira onse a Afilisiti nʼkuwauza kuti: “Chotsani Likasa la Mulungu wa Isiraeli kuno, libwerere kwawo kuti anthufe tisaphedwe.” Ananena zimenezi chifukwa mumzinda wonsewo anthu ankaopa kuti afa, chifukwa dzanja la Mulungu woona linkawasautsa.+