11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Ndiyeno Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.