5 Davide atamva zomwe zinachitikira atumiki akewo, nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane nawo chifukwa atumiki akewo anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ mpaka ndevu zanu zitakula, kenako mudzabwere.”