5 Pambuyo pake anthu anauza Davide zimene zinachitikira atumiki ake aja, ndipo iye nthawi yomweyo anatumiza mthenga kuti akakumane nawo chifukwa atumikiwo anachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ kufikira ndevu zanu zitakula ndithu, kenako mudzabwere.”