22 Kenako anthu a ku Yerusalemu anaveka ufumu Ahaziya mwana wake wamngʼono kwambiri kuti alowe mʼmalo mwake chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu.+ Choncho Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.+