22 Kenako anthu okhala mu Yerusalemu analonga ufumu Ahaziya+ mwana wake wamng’ono kwambiri, kukhala mfumu m’malo mwake (chifukwa gulu la achifwamba limene linabwera ndi Aluya+ kumsasa linapha ana ake onse akuluakulu).+ Tsopano Ahaziya mwana wa Yehoramu anayamba kulamulira monga mfumu ya Yuda.