5 Choncho anagwirizana kuti alengeze zimenezi mu Isiraeli monse kuyambira ku Beere-seba mpaka ku Dani+ kuti anthu abwere ku Yerusalemu adzachitire Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa anthuwo anali asanasonkhanepo kuti achite Pasika mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+